bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Isaiah 36
Isaiah 36
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 37 →
1
Koma panali caka cakhumi ndi cinai ca mfumu Hezekiya, Sanakeribu, mfumu ya Asuri anadza, nathira nkhondo pa midzi ya malinga yonse ya Yuda, nailanda.
2
Ndipo mfumu ya Asuri inatumiza kazembe kucokera pa Lakisi, kunka ku Yerusalemu, kwa mfumu Hezekiya, ndi nkhondo yambiri. Ndipo iye anaima cifupi ndi mcerenje wa thamanda la kumtunda, m'khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsaru.
3
Ndipo anamturukira Eliakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yoaki, mwana wa Asafu, mkumbutsi.
4
Ndipo kazembeyo anati kwa iwo, Nenani inu tsopano kwa Hezekiya, Itero mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri, Kodi cikhulupiriro ici ncotani, ucikhulupirira iwe?
5
Ine nditi, Uphungu wako, ndi mphamvu zako za kunkhondo, zingokhala mau acabe; tsopano ukhulupirira yani, kuti wandipandukira ine?
6
Taona, ukhulupirira ndodo yabango iyi yophwanyika, kunena Aigupto; imene munthu akaitsamira, idzalowa m'dzanja mwace, ndi kulipyoza; momwemo Farao, mfumu ya Aigupto, kwa onse amene amkhulupirira iye.
7
Koma ukanena kwa ine, Ife tikhulupirira Yehova Mulungu wathu; kodi si ndiye amene Hezekiya wacotsa misanje yace ndi maguwa ace a nsembe, nati kwa Yuda, ndi kwa Yerusalemu, Inu mudzapembedzera patsogolo pa suwa la nsembe ili?
8
Cifukwa cace upereketu zikole kwa mbuyanga, mfumu ya Asuri, ndipo ine ndidzakupatsa iwe akavalo zikwi ziwiri, ngati iwe udzaona okwerapo.
9
Bwanji tsono iwe ungathe kubweza nkhope ya nduna mmodzi wamng'ono wa atumiki a mbuyanga, ndi kukhulupirira Aigupto, kuti adzakupatsa magareta ndi apakavalo?
10
Ndipo ine tsopano, kodi ndafika opanda Yehova kudzamenyana ndi dziko ili, kudzalipasula? Yehova anati kwa ine, Kwera, ndi kumenyana ndi dziko ili, ndi kulipasula.
11
Ndipo Eliakimu, ndi Sebina, ndi Yoaki, anati kwa kazembeyo, Nenanitu kwa atumiki anu m'cinenero ca Aramu; pakuti ife ticimva; ndipo musanene kwa ife m'Ciyuda, m'makutu a anthu amene ali palinga.
12
Koma kazembeyo anati, Kodi mbuyanga ananditumiza ine kwa mbuyako ndi kwa iwe kunena mau amenewa? kodi iye sananditumiza ine kwa amuna okhala palinga, kuti adye ndowe zao zao, ndi kumwa madzi ao ao ndi inu?
13
Pamenepo kazembeyo anaima, napfuula ndi mau akuru m'Ciyuda, nati, Imvani, inu, mau a mfumu yaikuru, mfumu ya Asuri.
14
Mfumu itere, Musaleke Hezekiya anyenge inu; pakuti iye sadzathai kukupulumutsani:
15
ngakhale musaleke Hezekiya akhulupiritse inu kwa Yehova, ndi kunena, Yehova adzatipulumutsa ndithu; mudzi uwu sudzaperekedwa m'manja mwa mfumu ya Asuri.
16
Musamvere Hezekiya, pakuti mfumu ya ku Asuri itere, Mupangane nane, turukirani kwa ine; ndipo yense adye mphesa zace, ndi nkhuyu zace, namwe yense madzi a pa citsime cace;
17
kufikira ine ndidzadza, ndi kunka nanu ku dziko lofanana ndi lanu, dziko la tirigu ndi vinyo, dziko la cakudya ndi minda yamphesa.
18
Cenjerani angakukopeni inu Hezekiya, ndi kuti, Yehova adzatipulumutsa ife. Kodi milungu iri yonse ya amitundu inapulumutsa dziko lao m'manja mwa mfumu ya ku Asuri?
19
Iri kuti milungu ya Hamati, ndi Aripadi? iri kuti milungu ya Sefaravaimu? kodi inapulumutsa Samariya m'manja mwanga?
20
Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga?
21
Koma iwo anakhala cete, osamuyankha mau, pakuti mfumu inawalamulira kuti, Musamuyankhe.
22
Ndipo anafika Eliakimu, mwana wa Hilikiya, amene anali wapanyumba, ndi Sebina, mlembi, ndi Yoaki, mwana wa Asafu, mkumbutsi, kwa Hezekiya ndi zobvala zao zong'ambika, namuuza iye mau a kazembeyo.
← Chapter 35
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 37 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66