bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Isaiah 52
Isaiah 52
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 51
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 53 →
1
Galamuka galamuka, tabvala mphamvu zako, Ziyoni; tabvala zobvala zako zokongola, Yerusalemu, mzinda wopatulika; pakuti kuyambira tsopano sadzalowanso kwa iwe wosadulidwa ndi wodetsedwa.
2
Dzisanse pfumbi; uka, khala tsonga, Yerusalemu; udzimasulire maunyolo a pakhosi pako, iwe mwana wamkazi wam'nsinga wa Ziyoni.
3
Pakuti atero Yehova, Inu munagulitsidwa cabe, ndipo mudzaomboledwa opanda ndalama.
4
Pakuti Ambuye Yehova atero, Anthu anga ananka ku Aigupto poyamba paja, kukakhala kumeneko; ndipo Asuri anawatsendereza popanda cifukwa.
5
Cifukwa cace kodi ndicitenji pano? ati Yehova; popeza anthu anga acotsedwa popanda kanthu? akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa licitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.
6
Cifukwa cace anthu anga adzadziwa dzina langa; cifukwa cacersiku limenelo iwo adzadziwa kuti Ine ndine amene ndinena; taonani, ndine pano.
7
Ha, akongolatu pamapiri mapazi a iye amene adza ndi uthenga wabwino, amene abukitsa mtendere, amene adza ndi uthenga wabwino wa zinthu zabwino, amene abukitsa cipulumutso; amene ati kwa Ziyoni, Mulungu wako ndi mfumu.
8
Mau a alonda ako! akweza mau, ayimba pamodzi; pakuti adzaona maso ndi maso, pamene Yehova abwerera kudza ku Ziyoni.
9
Kondwani zolimba, yimbani pamodzi, inu malo abwinja a pa Yerusalemu; pakuti Yehova watonthoza mtima wa anthu ace, waombola Yerusalemu.
10
Yehova wabvula mkono wace woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona cipulumutso ca Mulungu wathu.
11
Cokani inu, cokani inu, turukani ku Babulo; musakhudze kanthu kodetsa; turukani pakati pace, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.
12
Pakuti simudzacoka mofulumira, kapena kunka mothawa; pakuti Yehova adzakutsogolerani, ndi Mulungu wa Israyeli adzadikira pambuyo panu.
13
Taonani, Mtumiki wanga adzacita mwanzeru; adzakwezedwa ndi kutukulidwa pamwamba, nadzakhala pamwambamwamba.
14
Monga ambiri anazizwa ndi iwe Israyeli, momwemo nkhope yace yaipitsidwa ndithu, kupambana munthu ali yense, ndi maonekedwe ace kupambana ana a anthu;
15
momwemonso Iye adzawazawaza mitundu yambiri; mafumu adzamtsekera Iye pakamwa pao; pakuti cimene sicinauzidwa kwa iwo adzaciona, ndi cimene iwo sanamva adzazindikira.
← Chapter 51
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 53 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66