bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Isaiah 7
Isaiah 7
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 8 →
1
Ndipo panali masiku a Ahazi, mwana wa Yotamu, mwana wa Uziya, mfumu ya Yuda, kuti Rezini, mfumu ya Aramu, ndi Peka, mwana wa Remaliya, mfumu ya Israyeli, anakwera kunka ku Yerusalemu, kumenyana nao; koma sanathe kuupamnana.
2
Ndipo anauza a nyumba ya Davide, kuti Aramu wapangana ndi Efraimu. Ndipo mtima wace unagwedezeka, ndi mtima wa anthu ace, monga mitengo ya m'nkhalango igwedezeka ndi mphepo.
3
Ndipo Yehova anati kwa Yesaya, Turuka tsopano kukacingamira Ahazi, iwe ndi Seariyasubu, mwana wamwamuna wako, pa mamariziro a mcerenje wa thamanda la pamtunda, ku khwalala la pa mwaniko wa wotsuka nsaru;
4
nukati kwa iye, Cenjera, khala ulipo; usaope, mtima wako usalefuke, cifukwa ca zidutswa ziwirizi za miuni yofuka, cifukwa ca mkwiyo waukali wa Rezini ndi Aramu, ndi wa mwana wa Remaliya.
5
Cifukwa Aramu ndi Efraimu, ndi mwana wa Remaliya anapangana kukucitira zoipa, nati,
6
Tiyeni, tikwere, timenyane ndi Yuda, timbvute; tiyeni, tidzigumulire mpata, pamenepo tikhazike mfumu pakati pace, ngakhale mwana wamwamuna wa Tabeeli;
7
atero Ambuye Yehova, Upo wao sudzaimai, sudzacitidwa.
8
Pakuti mutu wa Aramu ndi Damasiko, ndi mutu wa Damasiko ndi Rezini, zisadapite zaka makumi asanu ndi limodzi mphambu zisanu Efraimu adzatyokatyoka, sadzakhalanso mtundu wa anthu;
9
ndipo mutu wa Efraimu ndi Samariya, ndi mutu wa Samariya ndi mwana wa Remaliya, mukapanda kukhulupirira ndithu simudzakhazikika.
10
Ndipo Yehova ananenanso kwa Ahazi nati,
11
Udzipemphere wekha cizindikilo ca kwa Yehova Mulungu wako; pempha cam'mwakuya, kapena cam'mwamba.
12
Koma Ahazi anati, Sindipemphai ngakhale kumyesa Yehova.
13
Ndipo iye anati, Mverani inu tsopano, inu a nyumba ya Davide; kodi ndi kanthu kakang'ono kwa inu kutopetsa anthu, kuti inu mutopetsa Mulungu wanga?
14
Cifukwa cace Ambuye mwini yekha adzakupatsani inu cizindikilo; taonani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, nadzamucha dzina lace Imanueli.
15
Iye adzadya mafuta ndi uci, pamene adziwa kukana coipa ndi kusankha cabwino.
16
Popeza kuti asanadziwe mwanayo kukana coipa ndi kusankha cabwino, dziko limene mafumu ace awiri udana nao lidzasyidwa.
17
Yehova adzatengera pa iwe, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba ya atate wako, masiku, akuti sanadze oterewa kuyambira tsiku limene Efraimu analekana ndi Yuda; kunena mfumu ya Asuri.
18
Ndipo padzakhala tsiku limenelo kuti Yehova adzayimbira mluzu cimphanga ciri m'mbali ya kumtunda kwa nyanja za Aigupto, ndi njuci iri m'dziko la Asuri.
19
Ndipo zidzafika nizitera zonse m'zigwa zabwinja, ndi m'maenje a matanthwe, ndi paminga ponse, ndi pamabusa ponse.
20
Tsiku limenelo Ambuye adzameta mutu, ndi ubweya wa m'mapazi, ndi lumo lobwereka liri tsidya lija la Nyanja, kunena mfumu ya Asuri; ndilo lidzamarizanso ndebvu.
21
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti munthu adzaweta ng'ombe yaikazi yaing'ono, ndi nkhosa ziwiri;
22
ndipo padzakhala, cifukwa ca kucuruka kwa mkaka umene zidzapatsa, iye adzadya mafuta; pakuti mafuta ndi uci adzadya yense wosiyidwa pakati pa dziko.
23
Ndipo padzakhala tsiku limenelo, kuti pali ponse panali mipesa cikwi cimodzi ya mtengo wace wa ndalama cikwi cimodzi, padzakhala lunguzi ndi minga.
24
Munthu adzafikako ndi mibvi ndi uta; pakuti dziko lonse lidzakhala la lunguzi ndi minga.
25
Ndipo zitunda zonse zinalimidwa ndi khasu, iwe sudzafikako cifukwa ca kuopa lunguzi ndi minga, koma pomwepo padzakhala potumizira ng'ombe ndi popondaponda nkhosa.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66
Recommended Reading
Commentary
Isaiah Commentaries
→
Devotional
Isaiah Devotional Guide
→
Get This Bible
BL Study Bible
→