bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Isaiah 63
Isaiah 63
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 62
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 64 →
1
Ndani uyu alinkudza kucokera ku Edomu, ndi zobvala zonika zocokera ku Bozira? uyu wolemekezeka m'cobvala cace, nayenda mu ukuru wa mphamvu zace? Ndine amene ndilankhula m'colungama, wa mphamvu yakupulumutsa,
2
Cophimba cako cifiiriranji, ndi zobvala zako zifanana bwanji ndi woponda mopondera mphesa?
3
Ndaponda ndekha mopondera mphesa, ndipo panalibe nane mmodzi wa mitundu ya anthu; inde ndinawaponda m'kukwiya kwanga, ndi kuwapondereza mu ukali wanga: ndi mwazi wa moyo wao unawazidwa pa zobvala zanga; ndipo ndadetsa copfunda canga conse.
4
Pakuti tsiku lakubwezera liri mumtima mwanga, ndi caka ca kuombola anthu anga cafika.
5
Ndipo ndinayang'ana, koma panalibe wothangata; ndipo ndinadabwa kuti panalibe wocirikiza; cifukwa cace mkono wanga wanga unanditengera cipulumutso, ndi ukali wanga unandicirikiza Ine.
6
Ndipo ndinapondereza anthu m'kukwiya kwanga, ndi kuwatswanya mu ukali wanga, ndi kutsanulira mwazi wa moyo wao.
7
Ndidzachula za cifundo cace ca Yehova, ndi matamando a Yehova, monga mwa zonse zimene Yehova wapereka kwa ife; ndi ubwino wace waukuru kwa banja la Israyeli, umene Iye wapereka kwa iwo, monga mwa cifundo cace, ndi monga mwa nchito zocuruka za cikondi cace.
8
Pakuti anati, Zoonadi iwo ndiwo anthu anga, ana amene sangacite monyenga; comweco Iye anali Mpulumutsi wao.
9
M'mazunzo ao onse Iye anazunzidwa, ndipo mthenga wakuimirira pamaso pace anawapulumutsa; m'kukonda kwace ndi m'cisoni cace Iye anawaombola, nawabereka nawanyamula masiku onse akale.
10
Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa cisoni mzimu wace woyera, cifukwa cace Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.
11
Pamenepo iwo anakumbukira masiku akale, Mose ndi anthu ace, nati, Ali kuti Iye amene anawaturutsa m'nyanja pamodzi ndi abusa a gulu lace? Ali kuti Iye amene anaika mzimu wace woyera pakati pao,
12
amene anayendetsa mkono wace waulemerero pa dzanja lamanja la Mose? amene anagawanitsa madzi pamaso pao, kuti adzitengere mbiri yosatha?
13
amene anawatsogolera kupitira mwa kuya monga kavalo m'cipululu osapunthwa iwo?
14
Monga ng'ombe zotsikira kucigwa mzimu wa Yehova unawapumitsa; comweco inu munatsogolera anthu anu kudzitengera mbiri yaulemerero.
15
Tayang'anani kunsi, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, cangu canu ndi nchito zanu zamphamvu ziri kuti? mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi cisoni canu.
16
Pakuti Inu ndinu Atate wathu, ngakhale Abrahamu satidziwa ife, ndi Israyeli satizindikira ife. Inu Yehova ndinu Atate wathu, Mombolo wathu wacikhalire ndi dzina lanu.
17
Yehova bwanji mwatisoceretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, cifukwa ca atumiki anu, mafuko a colowa canu.
18
Anthu anu opatulika anakhala naco kanthawi kokha; adani athu apondereza kacisi wanu wopatulika.
19
Ife takhala ngati iwo amene simunawalamulira konse, ngati iwo amene sanachedwa dzina lanu.
← Chapter 62
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 51
Chapter 52
Chapter 53
Chapter 54
Chapter 55
Chapter 56
Chapter 57
Chapter 58
Chapter 59
Chapter 60
Chapter 61
Chapter 62
Chapter 63
Chapter 64
Chapter 65
Chapter 66
Chapter 64 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
51
52
53
54
55
56
57
58
59
60
61
62
63
64
65
66