bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Samuel 10
1 Samuel 10
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
1
Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?
2
M'mene talekana lero, mudzakomana ndi anthu awiri pa manda a Rakele, pa malire a Benjamini ku Zeliza; iwo ndiwo adzanena nanu, Abulu aja munakafuna, anapezedwa; ndipo onani, atate wanu analeka kulingalira abuluwo, koma alikulingalira za inu, ndi kuti, Ndidzachita chiyani, chifukwa cha mwana wanga?
3
Mukapitirira pamenepo tsono ndi kufika ku mtengo wathundu wa ku Tabori, kumeneko adzakomana nanu anthu atatu akukwera kwa Mulungu ku Betele, wina wonyamula anaambuzi atatu, wina mikate itatu, wina thumba la vinyo.
4
Iwowa adzakupatsani moni, ndi kukupatsani mikate iwiri; imeneyi mudzailandira m'manja mwao.
5
Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumudziko mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;
6
ndipo Mzimu wa Yehova udzagwera inu kolimba, nanunso mudzanenera pamodzi nao, nimudzasandulika munthu wina.
7
Ndipo zitakufikirani zizindikiro izi mudzachita monga mudzaona pochita, pakuti Mulungu ali nanu.
8
Ndipo mudzatsika patsogolo pa ine kunka ku Giligala; ndipo, taonani, ndidzatsikira kwa inu kukapereka zopsereza, ndi kuphera nsembe zamtendere. Mutsotsepo masiku asanu ndi awiri kufikira ndikatsikira kwa inu ndi kukudziwitsani chimene mudzachita.
9
Ndipo kunali, pamene iye anapotoloka kuti alekane ndi Samuele, Mulungu anampatsa mtima wina watsopano; ndipo zizindikiro zija zonse zinachitika tsiku lija.
10
Ndipo pamene anafika ku Gibea, onani, gulu la aneneri linakomana naye; ndi Mzimu wa Mulungu unamgwera mwamphamvu, iye nanenera pakati pao.
11
Ndipo kunali, kuti onse amene anamdziwiratu kale, pakuona ichi chakuti, onani, iye ananenera pamodzi ndi aneneri, anati wina ndi mnzake, Ichi nchiyani chinamgwera mwana wa Kisi? Kodi Saulonso ali mwa aneneri?
12
Ndipo munthu wina wa komweko anayankha nati, Ndipo atate wao ndiye yani? Chifukwa chake mauwa anakhala ngati mwambi, Kodi Saulonso ali mwa aneneri?
13
Ndipo pamene adatha kunenera anafika kumsanjeko.
14
Ndipo mbale wa atate wake wa Saulo ananena kwa iye ndi mnyamata wake, Munanka kuti? Ndipo iye anati, Kukafuna abuluwo; ndipo pakuona kuti sitinawapeza, tinadza kwa Samuele.
15
Ndipo mbale wa atate wa Saulo anati, Undiuze chimene Samuele analankhula nawe.
16
Ndipo Saulo anati kwa mbale wa atate wake, Anatiuza momveka kuti abuluwo anapezedwa kale. Koma sanamdziwitse mau aja Samuele ananena za ufumuwo.
17
Ndipo Samuele anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa;
18
nanena ndi ana a Israele, Atero Yehova, Mulungu wa Israele kuti, Ine ndinatulutsa Israele m'Ejipito, ndipo ndinakupulumutsani m'manja a Aejipito, ndi m'manja a maufumu onse anakusautsani;
19
koma lero inu mwakana Mulungu wanu amene anakupulumutsani yekha m'matsoka anu onse, ndi m'masautso anu; ndipo munanena naye, Koma mutipatse mfumu. Chifukwa chake tsono mudzionetse pamaso pa Yehova mafukomafuko, ndi magulumagulu.
20
Chomwecho Samuele anayandikizitsa mafuko onse a Israele, ndipo fuko la Benjamini linasankhidwa.
21
Nayandikizitsa fuko la Benjamini, banja ndi banja, ndipo banja la Amatiri linasankhidwa; nasankhidwa Saulo mwana wa Kisi. Koma pamene anamfuna, anapeza palibe.
22
Chifukwa chake anaonjeza kufunsa Yehova, Watsala wina kodi woyenera kubwera kuno? Ndipo Yehova anati, Onani, alikubisala pakati pa akatundu.
23
Ndipo anathamanga, namtenga komweko; ndipo iye pamene anaima pakati pa anthuwo, anali wamtali koposa anthu onse anamlekeza m'chifukwa.
24
Ndipo Samuele ananena ndi anthu onse, Mumuona kodi iye amene Yehova anamsankha, kuti palibe wina wakufanana naye pakati pa anthu onse? Ndipo anthu onse anafuula, kuti, Akhale ndi moyo mfumuyo.
25
Pamenepo Samuele anafotokozera anthu machitidwe a ufumu, nawalembera m'buku, nalisunga pamaso pa Yehova. Ndipo Samuele anauza anthu onse amuke, yense kunyumba yake.
26
Ndi Saulo yemwe anamuka kunyumba yake ku Gibea; ndipo am'khamu anatsagana naye iwo amene Mulungu adakhudza mitima yao.
27
Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31