bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Samuel 8
1 Samuel 8
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 9 →
1
Ndipo kunali, pamene Samuele anakalamba, anaika ana ake amuna akhale oweruza a Israele.
2
Dzina la mwana wake woyamba ndiye Yowele, ndi dzina la wachiwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba.
3
Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.
4
Pamenepo akulu onse a Israele anasonkhana, nadza kwa Samuele ku Rama;
5
nanena naye, Taonani, mwakalamba, ndipo ana anu satsanza makhalidwe anu; tsono, mutilongere mfumu kuti ikatiweruze, monga umo muchitidwa m'mitundu yonse ya anthu.
6
Koma chimenechi sichinakondweretsa Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova.
7
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.
8
Monga ntchito zao zonse anazichita kuyambira tsiku lija ndinawatulutsa ku Ejipito, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu ina, momwemo alikutero ndi iwenso.
9
Chifukwa chake tsono umvere mau ao; koma uwachenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ake a mfumu imene idzawaweruza.
10
Ndipo Samuele anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova.
11
Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu amuna, akhale akusunga magaleta, ndi akavalo ake; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magaleta ake;
12
idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.
13
Ndipo idzatenga ana anu akazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate.
14
Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda ya mphesa yanu, ndi minda ya azitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ake.
15
Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yamphesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake.
16
Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi abulu anu, nidzawagwiritsa ntchito yake.
17
Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapolo ake.
18
Ndipo tsiku lija mudzafuula chifukwa cha mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo.
19
Koma anthu anakana kumvera mau a Samuele; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu;
20
kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse; kuti mfumu yathuyo ikatiweruzire, ndi kutuluka kutitsogolera, ndi kuponya nafe nkhondo zathu.
21
Ndipo Samuele anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m'makutu a Yehova.
22
Ndipo Yehova anati kwa Samuele, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu. Ndipo Samuele anati kwa amuna a Israele, Mupite, munthu yense kumudzi wake.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31