bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Samuel 16
1 Samuel 16
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 17 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Samuele, Iwe ukuti ulire chifukwa cha Saulo nthawi yotani, popeza Ine ndinamkana kuti asakhale mfumu ya Israele? Dzaza nyanga yako ndi mafuta, numuke, ndidzakutumiza kwa Yese wa ku Betelehemu; pakuti ndinadzionera mfumu pakati pa ana ake.
2
Ndipo Samuele anati, Ndikamuka bwanji? Saulo akachimva, adzandipha. Ndipo Yehova anati, Umuke nayo ng'ombe yaikazi, nunene kuti, Ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova.
3
Ndipo uitane Yese abwere kunsembeko, ndipo Ine ndidzakusonyeza chimene uyenera kuchita; ndipo udzandidzozera iye amene ndidzakutchulira dzina lake.
4
Ndipo Samuele anachita chimene Yehova ananena, nadza ku Betelehemu. Ndipo akulu a mudziwo anadza kukomana naye monthunthumira, nati, Mubwera ndi mtendere kodi?
5
Nati iye, Ndi mtendere umene; ndadza kudzaphera nsembe kwa Yehova; mudzipatule ndi kufika ndi ine kunsembeko. Ndipo iye anapatula Yese ndi ana ake, nawaitanira kunsembeko.
6
Ndipo kunali, pakufika iwo, iye anayang'ana pa Eliyabu, nati, Zoonadi, wodzozedwa wa Yehova ali pamaso pake.
7
Koma Yehova ananena ndi Samuele, Usayang'ane nkhope yake, kapena kutalika kwa msinkhu wake, popeza Ine ndinamkana iye; pakuti Yehova saona monga aona munthu; pakuti munthu ayang'ana chooneka ndi maso, koma Yehova ayang'ana mumtima.
8
Pamenepo Yese anaitana Abinadabu nampititsa pa Samuele. Ndipo iye adati, Koma uyunso Yehova sadamsankhe.
9
Pamenepo Yese anapititsapo Sama. Ndipo anati, Koma uyunso Yehova sanamsankhe.
10
Ndipo Yese anapititsapo ana ake amuna asanu ndi awiri. Koma Samuele anati kwa Yese, Yehova sanawasankhe awa.
11
Ndipo Samuele anati kwa Yese, Ana anu ndi omwewa kodi? Nati iye, Watsala wina, mng'ono wa onse, ndipo taonani, iye alikuweta nkhosa. Ndipo Samuele anati kwa Yese, Tumiza munthu akamtenge; pakuti ife sitidzakhala pansi kufikira iye atadza kuno.
12
Ndipo anatumiza munthu, nabwera naye. Tsono iye anali wofiirira, ndi wa nkhope yokongola, ndi maonekedwe okoma. Ndipo Yehova anati, Nyamuka umdzoze, pakuti ndi ameneyu.
13
Pamenepo Samuele anatenga nyanga ya mafuta, namdzoza pakati pa abale ake; ndipo mzimu wa Yehova unalimbika pa Davide kuyambira tsiku lomweli. Ndipo Samuele ananyamuka, nanka ku Rama.
14
Koma mzimu wa Yehova unamchokera Saulo, ndi mzimu woipa wochokera kwa Yehova unamvuta iye.
15
Ndipo anyamata a Saulo ananena naye, Onani tsopano, mzimu woipa wochokera kwa Mulungu ulikuvuta inu.
16
Tsono inu mbuye wathu muuze anyamata anu, amene ali pamaso panu, kuti afune munthu wanthetemya wodziwa kuimba zeze; ndipo kudzakhala, pamene mzimu woipa wochokera kwa Mulungu uli pa inu, iyeyo adzaimba ndi dzanja lake, ndipo mudzakhala wolama.
17
Ndipo Saulo anati kwa anyamata ake, Mundifunire tsono munthu wakudziwa kuimba bwino, nimubwere naye kwa ine.
18
Ndipo mnyamata wake wina anayankha, nati, Taonani, ine ndaona mwana wa Yese wa ku Betelehemu, ndiye wanthetemya wodziwa kuimbira, ndipo ali wa mtima wolimba ndi woyenera nkhondo, ndiponso ali wochenjera manenedwe ake; ndiye munthu wokongola, ndipo Yehova ali naye.
19
Chifukwa chake Saulo anatumiza mithenga kwa Yese, nati, Unditumizire Davide, mwana wako, amene ali kunkhosa.
20
Ndipo Yese anatenga bulu namsenza mkate, ndi thumba la vinyo, ndi mwanawambuzi, nazitumiza kwa Saulo ndi Davide mwana wake.
21
Ndipo Davide anafika kwa Saulo, naima pamaso pake; ndipo iye anamkonda kwambiri, namsandutsa wonyamula zida zake.
22
Ndipo Saulo anatumiza kwa Yese, nati, Ulole kuti Davide aime pamaso panga; pakuti ndamkomera mtima.
23
Ndipo kunali kuti pamene mzimu woipawo wochokera kwa Mulungu unali pa Saulo, Davide anatenga zeze, naliza ndi dzanja lake; chomwecho Saulo anatsitsimuka, nakhala bwino, ndi mzimu woipa unamchokera iye.
← Chapter 15
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 17 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31