bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Samuel 9
1 Samuel 9
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 10 →
1
Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.
2
Iye anali ndi mwana wamwamuna dzina lake Saulo, mnyamata wokongola; pakati pa anthu onse a Israele panalibe wina wokongola ngati iye; anali wamtali, anthu onse ena anamlekeza m'chifuwa.
3
Ndipo abulu a Kisi, atate wa Saulo, analowerera. Ndipo Kisi anati kwa Saulo mwana wake, Utenge mnyamata mmodzi, nunyamuke, kukafuna abuluwo.
4
Ndipo anapyola dziko lamapiri la Efuremu, napyola dziko la Salisa, koma sanawapeze; pamenepo anapyolanso dziko la Salimu, koma panalibe pamenepo, napyola dziko la Abenjamini, osawapeza.
5
Pamene anafika ku dziko la Zufu, Saulo anamuuza mnyamata amene anali naye, kuti, Tiye tibwerere; kuti atate wanga angaleke kusamalira abuluwo, ndi kutenga nkhawa chifukwa cha ife.
6
Koma ananena naye, Onatu, m'mudzi muno muli munthu wa Mulungu, ndiye munthu anthu amchitira ulemu; zonse azinena zichitika ndithu; tiyeni tipite komweko, kapena adzakhoza kutidziwitsa zimene tili kuyendera.
7
Ndipo Saulo ananena ndi mnyamata wake, Koma taona, tikapitako timtengere chiyani munthuyo? Popeza mkate udatha m'zotengera zathu, ndiponso tilibe mphatso yakumtengera munthu wa Mulungu, tili nacho chiyani?
8
Ndipo mnyamatayo anayankhanso kwa Saulo nati, Onani m'dzanja langa muli limodzi la magawo anai a sekeli wa siliva; ndidzampatsa munthu wa Mulungu limeneli kuti atiuze njira yathu.
9
Kale m'Israele, munthu akati afunse kwa Mulungu, ankatero kuti, Tiyeni tipite kwa mlauliyo; popeza iye wotchedwa mneneri makono ano, anatchedwa mlauli kale.
10
Pamenepo Saulo anati kwa mnyamata wake, Wanena bwino; tiye tipite. Chomwecho iwowa anapita kumudzi kumene kunali munthu wa Mulunguyo.
11
Pakukwera kumudziko anapeza anthu akazi alikutuluka kuti akatunge madzi, nanena nao, Mlauliyo alipo kodi?
12
Ndipo anawayankha nati, Alipo; onani ali m'tsogolo mwanu; fulumirani pakuti wabwera lero kumudzi kuno; popeza lero anthu akuti aphere nsembe pamsanje;
13
mutafika m'mudzi, pomwepo mudzampeza, asanakwere kumsanje kukadya; pakuti anthu sadzadya, koma iye atafika ndipo; pakuti iye amadalitsa nsembeyo; ndipo atatero oitanidwawo amadya. Chifukwa chake kwerani; popeza nthawi yino mudzampeza.
14
Ndipo iwowa anakwera kumudzi; ndipo m'mene analowa m'mudzimo, onani, Samuele anatulukira pali iwo, kuti akakwere kumsanje.
15
Ndipo Yehova anaululiratu m'khutu la Samuele dzulo lake la tsiku limene Saulo anabwera, kuti,
16
Mawa, monga dzuwa lino, ndidzakutumizira munthu wochokera ku dziko la Benjamini, udzamdzoza iye akhale mtsogoleri wa anthu anga Israele, kuti akawapulumutse anthu anga m'manja a Afilisti; pakuti Ine ndinapenya pa anthu anga, popeza kulira kwao kunandifika Ine.
17
Ndipo pamene Samuele anaona Saulo, Yehova anati kwa iye, Ona munthu amene ndinakuuza za iye! Ameneyu adzaweruza anthu anga.
18
Pomwepo Saulo anayandikira kwa Samuele pakati pa chipata, nati, Mundidziwitse nyumba ya mlauliyo ili kuti.
19
Ndipo Samuele anayankha Saulo nati, Ine ndine mlauliyo. Kwera, batsogola kumsanje, pakuti mudzadya ndi ine lero; ndipo m'mawa ndidzakulola upite, ndi kukudziwitsa zonse zili mumtima mwako.
20
Za abulu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo chifuniro chonse cha Israele chili kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako?
21
Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine?
22
Ndipo Samuele anatenga Saulo ndi mnyamata wake, napita nao ku chipinda cha alendo, nawakhalitsa pa malo a ulemu pakati pa oitanidwa onse; ndiwo anthu monga makumi atatu.
23
Ndipo Samuele ananena ndi wophika, Tenga nyama ndinakupatsa, ndi kuti, Ibakhala ndi iwe.
24
Ndipo wophikayo ananyamula mwendo ndi mnofu wake, nauika pamaso pa Saulo. Ndipo Samuele anati, Onani chimene tinakuikirani? Muchiike pamaso panu, nudye; pakuti ichi anakuikirani kufikira nthawi yonenedwa, popeza ndinati, Ndinaitana anthuwo. Chomwecho Saulo anadya ndi Samuele tsiku lija.
25
Ndipo pamene anatsika kumsanje kulowanso kumudzi, iye anakamba ndi Saulo pamwamba pa nyumba yake.
26
Ndipo anauka mamawa; ndipo kutacha, Samuele anaitana Saulo ali pamwamba pa nyumba, nati, Ukani kuti ndikuloleni mumuke. Ndipo Saulo anauka, natuluka onse awiri, iye ndi Samuele, kunka kunja.
27
Ndipo pamene analikutsika polekeza mudzi, Samuele ananena ndi Saulo, Uzani mnyamatayo abatsogola; napita iyeyo. Koma inu muime pano, kuti ndikumvetseni mau a Mulungu.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31