bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
1 Samuel 20
1 Samuel 20
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 21 →
1
Ndipo Davide anathawa ku Nayoti m'Rama, nadzanena pamaso pa Yonatani, Ndachitanji ine? Kuipa kwanga kuli kotani? Ndi tchimo langa la pamaso pa atate wanu ndi chiyani, kuti amafuna moyo wanga?
2
Namyankha, Usatero iai, sudzafa; ona, atate wanga sachita kanthu kakakulu kapena kakang'ono wosandidziwitsa ine; atate wanga adzandibisiranji chinthu chimenechi? Si kutero ai.
3
Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.
4
Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Chilichonse mtima wako, unena ndidzakuchitira.
5
Nati Davide kwa Yonatani, Onani, mawa mwezi ukhala, ndipo ine ndiyenera kupita kukadya kwa mfumu, wosatsala; koma undilole ndikabisale kuthengo, kufikira tsiku lachitatu madzulo ake.
6
Atate wako akandifuna pang'ono ponse, unene kuti, Davide anandiumirira ndimlole athamangire kwao ku Betelehemu, pakuti kumeneko kuli nsembe ya pachaka ya banja lao lonse.
7
Tsono akati, Chabwino; kapolo wako adzakhala ndi mtendere; koma akapsa mtima, uzindikirepo kuti anatsimikiza mtima kundichitira choipa.
8
Chifukwa chake uchitire kapolo wako zokoma mtima; popeza wamchititsa kapolo wako kupangana nawe pangano la kwa Yehova; koma ngati mwa ine muli choipa chilichonse, undiphe wekha; udzapita nane bwanji kwa atate wako?
9
Ndipo Yonatani anati, Iai ndi pang'ono ponse; ine ndikadziwa konse kuti atate wanga anatsimikiza mtima kukuchitira choipa, sindidzadziwitsa iwe kodi?
10
Tsono Davide anati kwa Yonatani, Adzandiuza ndani ngati atate wako alankhulira iwe mokalipa?
11
Nati Yonatani kwa Davide, Tiyeni timuke kuthengo. Namuka onse awiri kuthengoko.
12
Ndipo Yonatani anati kwa Davide, Yehova, Mulungu wa Israele, akhale mboni; nditaphera mwambi atate wanga mawa dzuwa lino, kapena mkucha, onani, pakakhala kanthu kabwino kakuchitira Davide, sindidzakutumiza mthenga ndi kukuululira kodi?
13
Mulungu alange Yonatani, ndi kuonjezapo, ngati atate wanga akondwera kukuchitira choipa, ine osakuululira, ndi kukuchotsa kuti upite mumtendere; ndipo Yehova akhale nawe, monga anakhala naye atate wanga.
14
Ndipo undionetsere chifundo cha Yehova, si pokhala ine ndi moyo pokha, kuti ndingafe;
15
komanso usaleke kuchitira chifundo a m'nyumba yanga nthawi zonse: mungakhale m'tsogolomo Yehova atathera adani onse a Davide pa dziko lapansi.
16
Chomwecho Yonatani anapangana pangano ndi nyumba ya Davide, ndipo Yehova anakwaniritsa izi polanga adani a Davide.
17
Ndipo Yonatani anamlumbiritsa Davide kachiwiri, chifukwa anamkonda; popeza anamkonda monga anakonda moyo wa iye yekha.
18
Tsono Yonatani ananena kwa Davide, Mawa mwezi ukhala; ndipo adzakufuna, popeza udzasoweka pamalo pako.
19
Ndipo atapita masiku atatu, utsike msanga, nufike kumene unabisala tsiku la mlandu uja, nukhale pa mwala wa Ezeri.
20
Ndipo ine ndidzaponya mivi itatu pambali pake, monga ngati ndilikuponya pachandamali.
21
Ndipo taona, ndidzatumiza mnyamatayo, ndi kuti, Kafune miviyo. Ndikamuuza mwanayo, kuti, Taona mivi ili chakuno; uitole nubwere, popeza pali mtendere kwa iwe, palibe kanthu, pali Yehova.
22
Koma ndikati kwa mnyamatayo, Ona mivi ili kutsogoloko; pamenepo unyamuke ulendo wako; popeza Yehova wakuuza umuke.
23
Ndipo za chija tinakambirana iwe ndi ine, taona, Yehova ali pakati pa ife nthawi zonse.
24
Chomwecho Davide anabisala kuthengo; ndipo pakukhala mwezi, mfumu inakhala pansi kudya.
25
Mfumu nikhala pa mpando wake, monga ankachita nthawi zina, pa mpando wa pafupi pa khoma. Ndipo Yonatani anaimirira, ndi Abinere anakhala pa mbali ya Saulo; koma Davide anasoweka pamalo pake.
26
Koma Saulo sananene kanthu tsiku lomwelo; chifukwa anaganizira, Kanthu kanamgwera iye, ali wodetsedwa; indedi ali wodetsedwa.
27
Ndipo kunali tsiku lachiwiri mwezi utakhala, Davide adasowekanso pamalo pake; ndipo Saulo anati kwa Yonatani mwana wake, Mwana wa Yese walekeranji kubwera kudya dzulo ndi lero lomwe?
28
Ndipo Yonatani anayankha Saulo, Davide anandiumiriza ndimlole amuke ku Betelehemu;
29
nati, Ndiloleni, ndimuke; chifukwa banja lathu lipereka nsembe m'mudzimo; ndi mbale wanga anandiuzitsa ndifikeko; tsono ngati wandikomera mtima undilole ndichoke, ndikaone abale anga. Chifukwa cha ichi safika ku gome la mfumu.
30
Pamenepo Saulo anapsa mtima ndi Yonatani, nanena naye, Iwe mwana wa mkazi wa matsutso ndi wopikisana, sindidziwa kodi kuti wasankha mwana wa Yeseyo kudzinyaza wekha, ndi usiwa wa mai wako yemwe?
31
Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.
32
Ndipo Yonatani anayankha Saulo atate wake, nanena, Aphedwe chifukwa ninji? Anachitanji?
33
Ndipo Saulo anamponyera mkondo kuti amgwaze; momwemo Yonatani anazindikira kuti atate wake anatsimikiza mtima kupha Davide.
34
Pamenepo Yonatani anauka pagome wolunda ndithu, osadya kanthu tsiku lachiwiri la mwezi, pakuti mtima wake unali ndi chisoni chifukwa cha Davide, popeza atate wake anamchititsa manyazi.
35
Ndipo m'mawa, Yonatani ananka kuthengoko pa nthawi imene anapangana ndi Davide, ali ndi kamnyamata.
36
Ndipo anauza mnyamata wakeyo, Thamanga uzikatola mivi imene ndidzaponya; ndipo analikuthamanga mnyamatayu, iye anaponya muvi kuutumphitsa iye.
37
Ndipo mnyamatayo atafika pa malo a muvi umene Yonatani anauponya, nati, Muviwo suli m'tsogolo mwako kodi?
38
Ndipo Yonatani anafuulira mnyamatayo, nati, Yendetsa, fulumira, usaima. Ndi mnyamata wa Yonatani anatola mivi, nafika kwa mbuye wake.
39
Koma mnyamatayo sanadziwe kanthu; Davide ndi Yonatani okha anadziwa za mlanduwo.
40
Ndipo Yonatani anapatsa mnyamata wake zida zake, nanena naye, Muka, tenga izi kunka nazo kumudzi.
41
Pomwepo pochoka mnyamatayo, Davide, anauka chakumwera, nagwa nkhope yake pansi, nawerama katatu; ndipo iwowa anapsompsonana, nalirirana, kufikira Davide analiritsa.
42
Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumudzi.
← Chapter 19
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 21 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31