bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Leviticus 14
Leviticus 14
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 15 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,
2
Chilamulo cha wakhate tsiku la kumyeretsa kwake ndi ichi: azidza naye kwa wansembe;
3
ndipo wansembe atuluke kunka kunja kwa chigono; ndipo wansembe aone, ndipo taonani, ngati nthenda yakhate yapola pa wakhateyo;
4
pamenepo wansembe auze kuti amtengere iye wakuti akonzedwe, mbalame ziwiri zoyera zamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope;
5
ndipo wansembe auze kuti aphe mbalame imodzi m'mbale yadothi pamwamba pa madzi oyenda;
6
natenge mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, naziviike pamodzi ndi mbalame yamoyo m'mwazi wa mbalame adaipha pamwamba pa madzi oyenda;
7
nawaze kasanu ndi kawiri iye amene akuti amyeretse khate lake, namutche woyera, nataye mbalame yamoyo padambo poyera.
8
Ndipo iye wakuti ayeretsedwe atsuke zovala zake, namete tsitsi lake lonse, nasambe madzi, nakhale woyera; ndipo atatero alowe kuchigono, koma agone pa bwalo la hema wake masiku asanu ndi awiri.
9
Ndipo tsiku lachisanu ndi chiwiri kudzakhala kuti amete tsitsi lake lonse la pamutu pake, ndi ndevu zake, ndi nsidze zake, inde amete tsitsi lake lonse; natsuke zovala zake, nasambe thupi lake ndi madzi, nakhale woyera.
10
Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu atenge anaankhosa awiri, amuna opanda chilema, ndi mwanawankhosa mmodzi wamkazi wa chaka chimodzi wopanda chilema, ndi atatu a magawo khumi a efa la ufa wosalala ukhale nsembe yaufa, wosanganiza ndi mafuta, ndi muyeso umodzi wa magawo atatu wa mafuta.
11
Ndipo wansembe amene amyeretsayo, amuike munthu uja wakuti ayeretsedwe, ndi zinthu zija, pamaso pa Yehova, pa khomo la chihema chokomanako;
12
ndipo wansembe atenge mwanawankhosa mmodzi wamwamuna, nabwere naye akhale nsembe yopalamula, pamodzi ndi muyeso uja wa mafuta, naziweyule nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
13
Ndipo akaphere mwanawankhosa wamwamuna paja amapherapo nsembe yauchimo, ndi nsembe yopsereza, pa malo popatulika; pakuti monga nsembe yauchimo momwemo nsembe yopalamula nja wansembe; ndiyo yopatulika kwambiri.
14
Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe aupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;
15
ndipo wansembe atengeko muyeso uja wa mafuta, nawathire pa chikhato cha dzanja lake lamanzere la iye mwini;
16
ndipo wansembe aviike chala chake cha dzanja lake lamanja cha iye mwini m'mafuta ali m'dzanja lake lamanzere, nawaze mafuta kasanu ndi kawiri ndi chala chake pamaso pa Yehova;
17
ndipo wansembe apakeko mafuta okhala m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa mwazi wa nsembe yopalamula;
18
natsitsitize mafuta otsala m'dzanja lake la wansembe, pamutu pa iye wakuti ayeretsedwe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova.
19
Ndipo wansembe apereke nsembe yauchimo, namchitire chomtetezera amene akuti ayeretsedwe, chifukwa cha kudetsedwa kwake; ndipo atatero aphe nsembe yopsereza;
20
ndipo wansembe atenthe nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa pa guwa la nsembe; ndipo wansembe amchitire chomtetezera, ndipo adzakhala iye woyera.
21
Ndipo akakhala waumphawi chosafikana chuma chake azitenga mwanawankhosa mmodzi wamwamuna akhale nsembe yopalamula, aiweyule kumchitira chomtetezera, ndi limodzi la magawo khumi la efa la ufa wosalala, wosanganiza ndi mafuta, ukhale nsembe yaufa, ndi muyeso umodzi magawo atatu wa mafuta;
22
ndi njiwa ziwiri, kapena maunda awiri, monga akhoza kufikana; limodzi likhale la nsembe yauchimo, ndi linzake la nsembe yopsereza.
23
Ndipo tsiku lachisanu ndi chitatu abwere nao kwa wansembe, ku khomo la chihema chokomanako, pamaso pa Yehova, kuti ayeretsedwe.
24
Ndipo wansembe atenge mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndi muyeso uja wa mafuta, ndipo wansembe aziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova;
25
naphe mwanawankhosa wa nsembe yopalamula, ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yopalamula, naupake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye akuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja;
26
ndipo wansembe athireko mafuta aja m'chikhato chake chamanzere cha iye mwini;
27
ndipo wansembe awazeko mafuta aja ali m'dzanja lake lamanzere ndi chala chake cha dzanja lamanja, kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova;
28
ndipo wansembe apakeko mafuta aja ali m'dzanja lake pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la iye wakuti ayeretsedwe, ndi pa chala chachikulu cha dzanja lake lamanja, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja, pa malo paja pali mwazi wa nsembe yopalamula;
29
ndipo mafuta otsala m'dzanja la wansembe atsitsitize pa mutu wa iye wakuti ayeretsedwe, kumchitira chomtetezera pamaso pa Yehova.
30
Ndipo iye apereke imodzi ya njiwazo, kapena limodzi la maunda, monga akhoza kufikana nazo,
31
limodzi la nsembe yauchimo, ndi lina la nsembe yopsereza, pamodzi ndi nsembe yaufa; ndipo wansembe amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova iye wakuyeretsedwa.
32
Ichi ndi chilamulo cha iye ali ndi nthenda yakhate, wosakhoza kufikana nazo zofunika pomyeretsa pake.
33
Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nati,
34
Mutakafika m'dziko la Kanani, limene ndikupatsani likhale lanulanu, ndipo ndikaika nthenda yakhate m'nyumba ya dziko lanulanu;
35
pamenepo mwini nyumbayo adzauze wansembe, kuti, Ndiyesa muli ngati nthenda m'nyumba.
36
Ndipo wansembe aziuza kuti atulutse zonse za m'nyumba, asanalowe kudzaona nthendayi, zinthu zonse zili m'nyumba zingakhale zodetsedwa; ndipo atatero wansembe alowe kukaona nyumbayi;
37
naone nthendayo, ndipo taonani, nthenda ikakhala yosumbudzuka m'makoma a nyumba yobiriwira kapena yofiira, ndipo maonekedwe ake yakumba kubzola khoma;
38
pamenepo wansembe azituluka ku khomo la nyumba, natseka nyumbayo masiku asanu ndi awiri;
39
ndipo wansembe abwerenso tsiku lachisanu ndi chiwiri, naonenso, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'makoma a nyumba;
40
pamenepo wansembe auze kuti agumule miyalayi pali nthenda, naitayire ku malo akuda kunja kwa mudzi;
41
napalitse nyumba m'kati monsemo, natayire ku malo akuda kunja kwa mudzi dothi adapalako;
42
natenge miyala ina, naikhazike m'malo mwa miyala ija; natenge dothi lina, namatenso nyumbayo.
43
Ndipo ikabweranso nthenda, nibukanso m'nyumba atagumula miyala, ndipo atapala m'nyumba namatanso;
44
pamenepo wansembe alowe naonemo, ndipo taonani, ngati nthenda yakula m'nyumba, ndiyo khate lonyeka m'nyumba; ndiyo yodetsedwa.
45
Ndipo apasule nyumbayo, miyala yake, ndi mitengo yake, ndi dothi lake lonse kumudzi kuzitaya ku malo akuda.
46
Ndiponso iye wakulowa m'nyumba masiku ake ili yotsekedwa, adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo.
47
Ndipo iye wakugona m'nyumbayo atsuke zovala zake; ndi iye wakudya m'nyumbayo atsuke zovala zake.
48
Ndipo wansembe akalowa, nakaona, ndipo taonani, nthenda siinakula m'nyumba, ataimata nyumba; wansembe aitche nyumbayo yoyera, popeza nthenda yaleka.
49
Pamenepo atenge mbalame ziwiri, ndi mtengo wamkungudza, ndi ubweya wofiira, ndi hisope, kuti ayeretse nazo nyumbayo;
50
naphe mbalame imodzi m'mbale yadothi, pamwamba pa madzi oyenda;
51
natenge mtengo wamkungudza ndi hisope, ndi ubweya wofiira, ndi mbalame yamoyo, naziviike m'mwazi wa mbalame yakuphayo, ndi m'madzi oyenda, nawaze kasanu ndi kawiri m'nyumba;
52
nayeretse nyumba ndi mwazi wa mbalame, ndi madzi oyenda, ndi mbalame yamoyo, ndi mtengo wamkungudza, ndi hisope, ndi ubweya wofiira.
53
Koma ataye mbalame yamoyo kunja kwa mudzi kuthengo koyera; motero aichitire choitetezera nyumbayo; ndipo idzakhala yoyera.
54
Ichi ndi chilamulo cha nthenda iliyonse yakhate, ndi yamfundu;
55
ndi ya khate la chovala, ndi la nyumba;
56
ndi yachotupa, ndi yankhanambo, ndi yachikanga;
57
kulangiza tsiku loti chikhala chodetsa, ndi tsiku loti chikhala choyera; ichi ndi chilamulo cha khate.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27