bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Leviticus 21
Leviticus 21
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 22 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Nena ndi ansembe, ana a Aroniwo, nuti nao, Asadzidetse mmodzi wa inu chifukwa cha wakufa mwa anthu a mtundu wake;
2
koma chifukwa cha abale ake enieni ndiwo, mai wake, ndi atate wake, ndi mwana wake wamwamuna, ndi mwana wake wamkazi, ndi mbale wake;
3
ndi chifukwa cha mlongo wake weniweni, akakhala namwali wosakhala naye mwamuna, nkuloleka adzidetse chifukwa cha iwowa.
4
Akakhala mwini banja pakati pa anthu a mtundu wake, asadzidetse, ndi kudziipsa.
5
Asamete tsitsi la pamtu pao, kapena kuchecherera ndevu zao, kapena kudzicheka matupi ao.
6
Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika.
7
Asadzitengere mkazi wachigololo, kapena woipsidwa; asatenge mkazi woti adamchotsa mwamuna wake; popeza apatulikira Mulungu wake.
8
Chifukwa chake umpatule; popeza amapereka mkate wa Mulungu wako; umuyese wopatulika; pakuti Ine Yehova wakupatula iwe, ndine woyera,
9
Akadziipsa mwana wamkazi wa wansembe ndi kuchita chigololo, alikuipsa atate wake, amtenthe ndi moto.
10
Ndipo iye wokhala mkulu wansembe mwa abale ake, amene anamtsanulira mafuta odzoza pamutu pake, amene anamdzaza dzanja kuti avale zovalazo, asawinde, kapena kung'amba zovala zake.
11
Asafike kuli mtembo; asadzidetse chifukwa cha atate wake, kapena mai wake.
12
Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.
13
Ndipo adzitengere mkazi akali namwali.
14
Mkazi wamasiye, kapena womleka, kapena woipsidwa, wachigololo, oterewa asawatenge; koma azitenga namwali wa anthu a mtundu wake akhale mkazi wake.
15
Asaipse mbeu yake mwa anthu a mtundu wake; popeza Ine ndine Yehova wakumpatula iye.
16
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
17
Nena ndi Aroni, kuti, Aliyense wa mbeu zako mwa mibadwo yao wakukhala nacho chilema, asayandikize kupereka mkate wa Mulungu wake.
18
Pakuti munthu aliyense wokhala nacho chilema, asayandikize; wakhungu, kapena wotsimphina, kapena wopunduka mphuno, kapena wamkulu chiwalo,
19
kapena munthu wopunduka phazi kapena wopunduka dzanja,
20
kapena wowerama, kapena wamfupi msinkhu, kapena wopunduka diso, kapena munthu wamphere, kapena wachipere, kapena wopunduka kumoto.
21
Wa mbeu ya Aroni wansembe asayandikize mmodzi wokhala nacho chilema, kupereka nsembe zamoto za Yehova; ali nacho chilema asayandikize kupereka chakudya cha Mulungu wake.
22
Adye chakudya cha Mulungu wake, chopatulika kwambiri, ndi chopatulika;
23
koma asafike ku nsalu yotchinga, asayandikize ku guwa la nsembe, popeza ali nacho chilema; kuti angaipse malo anga opatulika; popeza Ine ndine Yehova wakuwapatula.
24
Momwemo Mose ananena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana onse a Israele.
← Chapter 20
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 22 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27