bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Leviticus 26
Leviticus 26
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 27 →
1
Musamadzipangira mafano, kapena kudziutsira mafano osema, kapena choimiritsa, kapena kuika mwala wozokota m'dziko mwanu kuugwadira umene; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wanu.
2
Musunge masabata anga, ndi kuchitira ulemu malo anga opatulika; Ine ndine Yehova.
3
Mukamayenda m'malemba anga, ndi kusunga malamulo anga, ndi kuwachita;
4
ndidzakupatsani mvula m'nyengo zake, ndi dziko lidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'minda idzabala zipatso zake.
5
Ndipo nyengo yopuntha tirigu idzafikira nyengo yotchera mphesa, ndi nyengo yotchera mphesa idzafikira nyengo zobzala; ndipo mudzakhuta nacho chakudya chanu, ndi kukhala m'dziko mwanu okhazikika.
6
Ndipo ndidzapatsa mtendere m'dzikomo, kuti mudzagone pansi, wopanda wina wakukuopsani; ndidzaletsanso zilombo zisakhale m'dzikomo, lupanga lomwe silidzapita m'dziko mwanu.
7
Mudzapirikitsa adani anu, ndipo adzagwa pamaso panu ndi lupanga.
8
Asanu a inu adzapirikitsa zana limodzi, ndi zana limodzi la inu adzapirikitsa zikwi khumi; ndi adani anu adzagwa pamaso panu ndi lupanga.
9
Ndipo ndidzatembenukira kwa inu, ndi kukubalitsani, ndi kukuchulukitsani; ndipo ndidzakhazika chipangano changa ndinapangana nanucho.
10
Ndipo mudzadya za sundwe wakale ndi kutulutsa zakale chifukwa cha zatsopano.
11
Ndidzamanga Kachisi wanga pakati pa inu, ndipo moyo wanga sudzanyansidwa nanu.
12
Ndipo ndidzayendayenda pakati pa inu, ndi kukhala Mulungu wanu ndi inu mudzakhala anthu anga.
13
Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti musakhale akapolo ao; ndipo ndinathyola mitengo ya magoli anu, ndi kukuyendetsani choweramuka.
14
Koma mukapanda kundimvera Ine, osachita malamulo awa onse;
15
ndipo mukakaniza malemba anga, ndi moyo wanu ukanyansidwa nao maweruzo anga, kotero kuti simudzachita malamulo anga onse, koma kuthyola chipangano changa;
16
ndidzachitira inu ichinso; ndidzakuikirani zoopsa, nthenda yoondetsa ya m'chifuwa ndi malungo, zakulanda maso ndi mphamvu, ndi kuzunza moyo; ndipo mudzabzala mbeu zanu chabe, popeza adani anu adzazidya.
17
Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.
18
Ndipo mukapanda kundimvera, zingakhale izi, ndidzaonjeza kukulangani kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.
19
Popeza ndidzathyola mphamvu yanu yodzikuza; ndi kusandutsa thambo lanu likhale ngati chitsulo ndi dziko lanu ngati mkuwa;
20
ndipo mudzachita nayo mphamvu yanu chabe; ndi nthaka yanu siidzapereka zipatso zake, ndi mitengo ya m'dziko siidzabala zobala zake.
21
Ndipo mukayenda motsutsana nane, osalola kumvera Ine; ndidzakuonjezerani miliri kasanu ndi kawiri, monga mwa zochimwa zanu.
22
Popeza ndidzatumiza chilombo cha kuthengo pakati pa inu, ndipo chidzalanda ana anu, ndi kuononga zoweta zanu nichidzachepetsa inu kuti mukhale pang'ono; ndi njira zanu zidzakhala zakufa.
23
Ndipo mukapanda kulangika nazo ndi kubwera kwa Ine, mukayenda motsutsana ndi Ine;
24
Inenso ndidzayenda motsutsana ndi inu; ndipo ndidzakukanthani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zoipa zanu.
25
Ndipo ndidzadzetsa kwa inu lupanga lakuchita chilango cha chipangano; kotero kuti mudzasonkhanidwa m'midzi mwanu; ndipo ndidzatumiza mliri pakati pa inu; ndipo mudzaperekedwa m'manja mwa mdani.
26
Pamene ndithyola mchirikizo wanu wa mkate, akazi khumi adzaphika mkate wanu mu mchembo umodzi, nadzabweza mkate wanu ndi kuuyesa; ndipo mudzadya, koma osakhuta.
27
Ndipo mukapanda kundimvera Ine, chingakhale ichi, ndi kuyenda motsutsana nane;
28
Ine ndidzayenda nanu motsutsana mwa kukuzazirani, ndi kukulangani Inedi kasanu ndi kawiri chifukwa cha zochimwa zanu.
29
Ndipo mudzadya nyama ya ana anu amuna; inde nyama ya ana anu akazi mudzaidya.
30
Ndipo ndidzaononga malo amsanje anu, ndi kulikha zoimiritsa zanu za dzuwa, ndi kuponya mitembo yanu pa mitembo ya mafano anu; ndi moyo wanga udzanyansidwa nanu.
31
Ndipo ndidzasandutsa midzi yanu bwinja, ndi kupasula malo anu opatulika, wosanunkhiza Ine za fungo lanu lokoma.
32
Inde, ndidzapasula dzikoli, ndipo adani anu akukhala m'mwemo adzadabwa nako.
33
Ndipo ndidzabalalitsa inu mwa amitundu, ndi kusolola lupanga kukutsatani; ndi dziko lanu lidzakhala lopasuka, ndi midzi yanu idzakhala bwinja.
34
Pamenepo dzikoli lidzakondwera nao masabata ake, masiku onse a kupasuka kwake, pokhala inu m'dziko la adani anu; pamenepo dziko lidzapumula, ndi kukondwera nao masabata ake.
35
Masiku onse a kupasuka kwake lipumula; ndiko mpumulo udalisowa m'masabata anu, pokhala inu pamenepo.
36
Kunena za iwo akutsalira, ndidzalonga kukomoka kumtima kwao m'maiko a adani ao; ndi liu la tsamba lotengeka ndi mphepo lidzawapirikitsa; ndipo adzathawa monga amathawa lupanga; ndipo adzagwa wopanda wakuwalondola.
37
Ndipo adzakhumudwitsana monga pothawa lupanga, wopanda wakuwalondola; ndipo mudzakhala opanda mphamvu yakuima pamaso pa adani anu.
38
Ndipo mudzatayika mwa amitundu, ndi dziko la adani anu lidzakudyani.
39
Ndipo otsala mwa inu adzazunzika m'moyo ndi mphulupulu zao m'maiko a adani anu; ndiponso ndi mphulupulu za makolo ao adzazunzika m'moyo.
40
Pamenepo adzavomereza mphulupulu zao, ndi mphulupulu za makolo ao, pochita zosakhulupirika pa Ine; ndiponso popeza anayenda motsutsana ndi Ine,
41
Inenso ndinayenda motsutsana nao, ndi kuwatengera ku dziko la adani ao. Ngati tsono mtima wao wosadulidwa udzichepetsa, ndipo avomereza kulanga kwa mphulupulu zao;
42
pamenepo ndidzakumbukira pangano langa ndi Yakobo; ndiponso pangano langa ndi Isaki, ndiponso pangano langa ndi Abrahamu ndidzakumbukira; ndipo ndidzakumbukira dzikoli.
43
Dziko lomwe lidzasiyidwa nao, ndi kukondwera ndi masabata ake, pokhala lopasuka, iwowa palibe; ndipo iwo adzavomereza kulanga kwa mphulupulu zao; popeza, inde popeza anakaniza maweruzo anga, ndi moyo wao unanyansidwa nao malemba anga.
44
Ndiponso pali ichinso: pokhala iwo m'dziko la adani ao sindidzawakaniza, kapena kunyansidwa nao, kuwaononga konse, ndi kuthyola pangano langa ndinapangana nao; popeza Ine ndine Yehova Mulungu wao.
45
Koma chifukwa cha iwo ndidzawakumbukira pangano la makolo ao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito pamaso pa amitundu, kuti ndikhale Mulungu wao; Ine ndine Yehova.
46
Awa ndi malemba ndi maweruzo ndi malamulo amene Yehova anaika pakati pa Iye ndi ana a Israele m'phiri la Sinai, ndi dzanja la Mose.
← Chapter 25
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 27 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27