bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Leviticus 22
Leviticus 22
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 23 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
2
Nena ndi Aroni ndi ana ake amuna, kuti azikhala padera ndi zinthu zopatulika za ana a Israele, zimene amandipatulira Ine, ndipo asaipse dzina langa loyera; Ine ndine Yehova.
3
Nena nao, Aliyense wa mbeu zanu zonse mwa mibadwo yanu, akayandikiza zinthu zopatulika, zimene ana a Israele azipatulira Yehova, pokhala ali nacho chomdetsa chake, azimsadza munthuyo pankhope panga; Ine ndine Yehova.
4
Munthu aliyense wa mbeu za Aroni wokhala ndi khate, kapena kukha, asadyeko zinthu zopatulika, kufikira atayera. Ndipo aliyense wokhudza chinthu chodetsedwa ndi wakufa, kapena mwamuna wogona uipa;
5
ndi aliyense wokhudza chinthu chokwawa chakudetsedwa nacho, kapenanso munthu amene akamdetsa nacho, chodetsa chake chilichonse;
6
munthu wokhudza chilichonse chotere adzakhala wodetsedwa kufikira madzulo, ndipo asadye zinthu zopatulika, akapanda kusamba thupi lake ndi madzi.
7
Koma litalowa dzuwa, adzakhala woyera, ndi pambuyo pake adyeko zoyerazo, popeza ndizo chakudya chake.
8
Asamadya zakufa zokha, kapena zojiwa, kudzidetsa nazo; Ine ndine Yehova.
9
Potero asunge chilangizo changa, angasenzepo uchimo, ndi kufera m'mwemo, pakuchiipsa; Ine ndine Yehova wakuwapatula iwo.
10
Mlendo asadyeko chopatulikacho; wakungokhala, ndi wansembe, kapena wolembedwa ntchito, asadyeko chopatulikacho.
11
Koma wansembe atakagula munthu ndi ndalama zake, iyeyu adyeko; ndi iwo amene anabadwa m'nyumba yake, adyeko mkate wake.
12
Ndipo mwana wamkazi wa wansembe akakwatibwa ndi mlendo, asadyeko nsembe yokweza ya zinthu zopatulika.
13
Koma mwana wamkazi wa wansembe akakhala wamasiye kapena wochotsedwa, ndipo alibe mwana, nabwerera kunyumba ya atate wake, monga muja anali mwana, adyeko mkate wa atate wake; koma mlendo asamadyako.
14
Ndipo munthu akadyako chinthu chopatulika mosadziwa, azionjezapo limodzi la magawo asanu, nalipereke kwa wansembe, pamodzi ndi chopatulikacho.
15
Potero asaipse zinthu zopatulika za ana a Israele, zopereka iwo kwa Yehova;
16
ndi kuwasenzetsa mphulupulu yakuwapalamulitsa, pakudya iwo zopatulika zao; pakuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.
17
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
18
Nena ndi Aroni, ndi ana ake amuna, ndi ana onse a Israele, nuti nao, Aliyense wa mbumba ya Israele, kapena wa alendo ali m'Israele, akabwera nacho chopereka chake, monga mwa zowinda zao zonse, kapena monga mwa zopereka zaufulu zao, zimene abwera nazo kwa Yehova zikhale nsembe zopsereza;
19
kuti mulandiridwe, azibwera nayo yaimuna yopanda chilema, ya ng'ombe, kapena nkhosa kapena mbuzi.
20
Musamabwera nayo yokhala ndi chilema; popeza siidzalandirikira inu.
21
Ndipo munthu akabwera nayo nsembe yoyamika kwa Yehova, ya pa chowinda chachikulu, kapena ya pa chopereka chaufulu, ya ng'ombe kapena nkhosa, ikhale yangwiro kuti ilandirike; ikhale yopanda chilema.
22
Musamabwera nazo kwa Yehova yakhungu, kapena yoduka mwendo, kapena yopunduka, kapena yafundo, kapena yausemwe, kapena ya usemwe waukulu, musamazipereka kwa Yehova nsembe zamoto pa guwa la nsembe.
23
Ng'ombe kapena nkhosa yokula kapena yochepa chiwalo, ikhale nsembe yaufulu; koma pa chowinda siidzalandirika.
24
Nyama yofula, kapena chopwanya kapena chosansantha, kapena chotudzula, kapena chodula, musamabwera nazo kwa Yehova; inde musamachita ichi m'dziko mwanu.
25
Ndipo musamazilandira izi ku dzanja la mlendo ndi kubwera nazo zikhale chakudya cha Mulungu wanu; popeza zili nako kuvunda kwao; zili ndi chilema; sizidzalandirikira inu.
26
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti,
27
Zikamabadwa ng'ombe kapena nkhosa, kapena mbuzi, zikhale ndi make masiku asanu ndi awiri; kuyambira tsiku lachisanu ndi chitatu ndi m'tsogolo mwake, idzalandirika ngati chopereka nsembe yamoto ya Yehova.
28
Koma musamaipha ng'ombe kapena nkhosa pamodzi ndi mwana wake tsiku limodzimodzi.
29
Ndipo mukamaphera Yehova nsembe yoyamika, muiphere kuti mulandirike.
30
Idyedwe tsiku lomwelo; musamasiyako kufikira m'mawa; Ine ndine Yehova.
31
Potero muwasunge malamulo anga, ndi kuwachita; Ine ndine Yehova.
32
Musamaipsa dzina langa loyera; koma ndikhale woyera pakati pa ana a Israele; Ine ndine Yehova wakukupatulani,
33
amene ndinakutulutsani m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale Mulungu wanu; Ine ndine Yehova.
← Chapter 21
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 23 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27