bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Leviticus 8
Leviticus 8
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 9 →
1
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, nati,
2
Tenga Aroni ndi ana ake pamodzi naye ndi zovalazo, ndi mafuta odzozawo; ndi ng'ombe ya nsembe yauchimoyo, ndi nkhosa zamphongo ziwirizo, ndi dengu la mkate wopanda chotupitsawo;
3
nusonkhanitse khamu lonse ku khomo la chihema chokomanako.
4
Ndipo Mose anachita monga Yehova anamuuza; ndi khamulo linasonkhana pa khomo la chihema chokomanako.
5
Ndipo Mose anati kwa msonkhanowo, Ichi ndi chimene Yehova adauza kuti chichitike.
6
Ndipo Mose anabwera nao Aroni ndi ana ake, nawasambitsa ndi madzi.
7
Ndipo anamveka ndi malaya a m'kati, nammanga m'chuuno ndi mpango, namveka ndi mwinjiro, namveka ndi efodi, nammanga m'chuuno ndi mpango wa efodi nammanga nao pathupi pake.
8
Ndipo anamuika chapachifuwa; naika m'chapachifuwa Urimu ndi Tumimu.
9
Naika nduwirayo pamutu pake; ndi panduwira, pamphumi pake anaika golide waphanthiphanthi, ndiwo korona wopatulika; monga Yehova adauza Mose.
10
Ndipo Mose anatenga mafuta odzoza, nadzoza Kachisi, ndi zonse zili m'mwemo, nazipatula.
11
Ndipo anawazako pa guwa la nsembe kasanu ndi kawiri, nadzoza guwa la nsembe, ndi zipangizo zake zonse, ndi mkhate ndi tsinde lake, kuzipatula.
12
Ndipo anatsanulirako mafuta odzoza pamutu pa Aroni, namdzoza kumpatula.
13
Ndipo Mose anatenga ana a Aroni, nawaveka malaya a m'kati, nawamanga m'chuuno ndi mipango, nawamanga akapa; monga Yehova adzauza Mose.
14
Ndipo anabwera nayo ng'ombe ya nsembe yauchimo; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa ng'ombe ya nsembe yauchimo.
15
Ndipo anaipha; ndi Mose anatenga mwaziwo, naupaka ndi chala chake pa nyanga za guwa la nsembe pozungulira; nayeretsa guwa la nsembe, nathira mwazi patsinde pa guwa la nsembe, nalipatula, kuti alichitire cholitetezera.
16
Ndipo anatenga mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndipo Mose anazitentha pa guwa la nsembe.
17
Koma ng'ombeyo, ndi chikopa chake, ndi nyama yake, ndi chipwidza chake, anazitentha ndi moto kunja kwa chigono; monga Yehova adamuuza Mose.
18
Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo ya nsembe yopsereza; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pamutu pa mphongoyo.
19
Ndipo anaipha; ndi Mose anawaza mwazi wake pa guwa la nsembe pozungulira.
20
Ndipo anapadzula mphongoyo ziwalo zake; ndi Mose anatentha mutuwo ndi ziwalo, ndi mafuta.
21
Koma anatsuka matumbo ndi miyendo ndi madzi; ndi Mose anatentha mphongo yonse pa guwa la nsembe; ndiyo nsembe yopsereza yochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose.
22
Ndipo anabwera nayo nkhosa yamphongo yinayo, ndiyo mphongo ya kudzaza manja; ndipo Aroni ndi ana ake amuna anaika manja ao pa mutu wa mphongoyo.
23
Ndipo anaipha; ndi Mose anatengako mwazi wake naupaka pa ndewerere ya khutu la ku dzanja lamanja la Aroni, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lake, ndi pa chala chachikulu cha phazi lake la ku dzanja lamanja.
24
Pamenepo anabwera nao ana amuna a Aroni, ndi Mose anatengako mwazi, naupaka pa ndewerere ya khutu lao la ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja lao, ndi pa chala chachikulu cha phazi lao la ku dzanja lamanja; ndipo Mose anawaza mwaziwo pa guwa la nsembe pozungulira.
25
Ndipo anatenga mafutawo ndi mchira wamafuta, ndi mafuta onse a pamatumbo, ndi chokuta cha mphafa, ndi impso ziwiri, ndi mafuta ake, ndi mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;
26
ndipo mu dengu la mkate wopanda chotupitsa wokhala pamaso pa Yehova, anatengeramo kamtanda kamodzi kopanda chotupitsa, ndi kamtanda kamodzi ka mkate wamafuta, ndi kamtanda kamodzi kaphanthi, natiika pa mafutawo, ndi pa mwendo wathako wa ku dzanja lamanja;
27
anaika zonsezi m'manja mwa Aroni, ndi m'manja mwa ana ake amuna, naziweyula nsembe yoweyula pamaso pa Yehova.
28
Pamenepo Mose anazichotsa ku manja ao, nazitentha pa guwa la nsembe, pa nsembe yopsereza; ndizo nsembe zodzaza manja zochita fungo lokoma; ndiyo nsembe yamoto ya kwa Yehova.
29
Ndipo Mose anatenga ngangayo naiweyula, nsembe yoweyula pamaso pa Yehova; ndilo gawo la Mose la ku nkhosa yamphongo ya kudzaza manja; monga Yehova adamuuza Mose.
30
Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala pa guwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake amuna, ndi pa zovala za ana ake amuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake amuna, ndi zovala za ana ake amuna omwe.
31
Ndipo Mose anati kwa Aroni ndi kwa ana ake amuna, Phikani nyamayi pakhomo pa chihema chokomanako; ndipo muidyere komweko ndi mkate uli mu dengu la nsembe zodzaza manja, monga ndinauza, ndi kuti, Aroni ndi ana ake aidye.
32
Koma chotsalira cha nyama ndi mkate muchitenthe ndi moto.
33
Ndipo musatuluka pa khomo la chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, kufikira anakwanira masiku a kudzaza manja kwanu; pakuti adzaze manja anu masiku asanu ndi awiri.
34
Monga anachita lero lino, momwemo Yehova anauza kuchita, kukuchitirani chotetezera.
35
Ndipo mukhale pakhomo pa chihema chokomanako masiku asanu ndi awiri, usana ndi usiku, ndi kusunga chilangizo cha Yehova, kuti mungafe; pakuti anandiuza kotero.
36
Ndipo Aroni ndi ana ake amuna anachita zonse zimene Yehova anauza pa dzanja la Mose.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27