bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ephesians 1
Ephesians 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 2 →
1
Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwa kufuna kwa Mulungu. Ndikulembera anthu a Mulungu amene ali ku Efeso, amenenso ali okhulupirika mwa Khristu Yesu.
2
Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu akukomereni mtima ndi kukupatsani mtendere.
3
Tiyamike Mulungu, Atate a Ambuye athu Yesu Khristu. Mwa Khristu Iye adatipatsa madalitso onse auzimu Kumwamba.
4
Mulungu asanalenge dziko lapansi, adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale oyera mtima ndi opanda cholakwa pamaso pake.
5
Chifukwa chotikonda, adakonzeratu kuti mwa Yesu Khristu atilandire ngati ana ake. Adachita zimenezi chifukwa adaafuna kutero mwa kukoma mtima kwake.
6
Adaafuna kuti tizitamanda ulemu wake chifukwa adatikomera mtima kopambana, pakutipatsa Mwana wake wokondedwa ngati mphatso yaulere.
7
Ndi imfa ya Mwana wakeyo Mulungu adatipulumutsa, adatikhululukira machimo athu. Nzazikuludi mphatso zaulere
8
zimene Mulungu adatipatsa mochuluka.
9
Mwa luntha ndi nzeru adatiwululira chifuniro chake chimene kale chinali chobisika. Zimene adaati achite mwa kukoma mtima kwake ndi zomwe Iye mwini adaakonzeratu kale.
10
Chimene Mulungu adalongosola kuti achite itakwana nthaŵi, nchakuti asonkhanitse pamodzi mwa Khristu zinthu zonse za Kumwamba ndi zapansipano.
11
Paja Mulungu amaongolera zinthu zonse monga momwe Iye wafunira ndi m'mene watsimikizira. Iye adatisankhiratu mwa Khristu kuti tikhale akeake. Adazikonzeratu kuti ziyenera kukhala choncho.
12
Adafuna kuti ife, amene tinali oyamba kuyembekeza Khristu, tilemekeze ulemerero wake.
13
Mwa Khristu, inunso mutamva mau oona, amene ali Uthenga Wabwino wokupulumutsani, mudaukhulupirira. Nchifukwa chake Mulungu adakusindikizani chizindikiro chotsimikizira kuti ndinu akedi, pakukupatsani Mzimu Woyera amene Iye adaalonjeza.
14
Mzimu Woyerayo ndiye chikole chotsimikizira kuti tidzalandiradi madalitso onse amene Mulungu adalonjeza kupatsa anthu ake, ndipo kuti Mulungu adzapulumutsa kwathunthu anthu amene adaŵaombola kuti akhale ake enieni. Cholinga cha zonsezi ndi chakuti tilemekeze ulemerero wake.
15
Ndamva kuti mukukhulupirira Ambuye Yesu, ndiponso kuti mumakonda anthu a Mulungu.
16
Nchifukwa chake sindilekeza kuthokoza Mulungu chifukwa cha inu. Ndimakukumbukirani m'mapemphero anga,
17
ndipo ndimapemphera kuti Mulungu wa Ambuye athu Yesu Khristu, Atate aulemerero, akuninkheni Mzimu Woyera, amene adzakupatsani nzeru, nadzaulula Mulungu kwa inu, kuti mumdziŵe kwenikweni.
18
Ndimapemphera kuti Mzimu Woyerayo akuunikireni m'mitima mwanu, kuti mudziŵe zimene mungathe kuyembekezera kwa Mulungu amene adakuitanani. Ndimafunanso kuti mudziŵe kukula kwake kwa ulemerero ndi madalitso amene Mulungu amalonjeza kupatsa anthu ake.
19
Ndiponso ndikufuna kuti mudziŵe mphamvu yake yopitirira muyeso imene ikugwira ntchito mwa ife omkhulupirira. Mphamvuyi ndi yomwe ija yolimba koposa,
20
imene Mulungu adaigwiritsa ntchito pamene adaukitsa Khristu kwa akufa, namkhazika ku dzanja lake lamanja m'dziko la Kumwamba.
21
Adamkhazika pamwamba pa mafumu onse, aulamuliro onse ndi akuluakulu onse a Kumwamba, ndiponso pamwamba pa maina ena onse amene anthu angaŵatchule nthaŵi ino kapenanso nthaŵi ilikudza.
22
Mulungu adagonjetsa zonse kuti zikhale pansi pa mapazi a Khristu, ndipo adamkhazika pamwamba pa zonse kuti akhale mutu wa Mpingo.
23
Mpingowu ndi thupi la Khristu, ndipo ndi wodzazidwa ndi Khristuyo amene amadzaza zinthu zonse kotheratu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6