bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ephesians 5
Ephesians 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 6 →
1
Tsono popeza kuti ndinu ana okondedwa a Mulungu, muziyesa kumtsanzira.
2
Muzikondana, monga Khristu adatikonda ife, nadzipereka kwa Mulungu chifukwa cha ife. Adadzipereka ngati chopereka ndi nsembe ya fungo lokondweretsa Mulungu.
3
Popeza kuti ndinu anthu a Mulungu, ndiye kuti dama kapena zonyansa, kapena masiriro oipa zisatchulidwe nkomwe pakati panu.
4
Ndiponso musamalankhule zolaula, zopusa, kapena zopandapake, koma muzilankhula zoyamika Mulungu.
5
Mudziŵe ichi, kuti munthu aliyense wadama, kapena wochita zonyansa, kapena wa masiriro oipa (pakuti wa masiriro oipa ali ngati wopembedza fano) sadzaloŵa nao mu Ufumu wa Khristu ndi wa Mulungu.
6
Munthu wina aliyense asakupusitseni ndi mau onyenga, pakuti zinthu zotere ndizo zimadzetsa ukali wa Mulungu pa anthu omupandukira.
7
Nchifukwa chake musamagwirizane nawo anthu otere.
8
Inunso kale mudaali mu mdima, koma tsopano muli m'kuŵala, popeza kuti ndinu ao a Ambuye. Tsono muziyenda ngati anthu okhala m'kuŵala.
9
Pajatu pamene pali kuŵala, pamapezekanso ubwino wonse, chilungamo chonse ndi choona chonse.
10
Muziyesa kudziŵa kwenikweni zimene zingakondweretse Ambuye.
11
Musayanjane nawo anthu ochita zopanda pake za mdima, koma muŵatsutse.
12
Paja zimene iwo amachita mobisa, ngakhale kuzitchula komwe kumachititsa manyazi.
13
Koma kuŵala kumaunika zinthu, ndipo zonse zimaonekera poyera.
14
Motero chilichonse choonekera poyera, chimasanduka kuŵala. Nchifukwa chake amati, “Dzuka wam'tulo iwe, uka kwa akufa, ndipo Khristu adzakuŵalira.”
15
Samalirani bwino mayendedwe anu. Musayende monga anthu opanda nzeru, koma monga anthu anzeru.
16
Mukhale achangu, osataya nthaŵi yanu pachabe, pakuti masiku ano ngoipa.
17
Nchifukwa chake musakhale opusa, koma dziŵani zimene Ambuye afuna kuti muchite.
18
Musaledzere vinyo, kumeneko nkudzitaya, koma mudzazidwe ndi Mzimu Woyera.
19
Muzichezerana ndi mau a masalimo ndi a nyimbo za Mulungu ndi zauzimu. Ndipo muziimbira Ambuye mopolokezana ndi mtima wanu wonse.
20
Muziyamika Mulungu Atate nthaŵi zonse chifukwa cha zonse, m'dzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
21
Inu amene mumaopa Khristu, muzimverana.
22
Inu akazi, muzimvera amuna anu, monga mumamvera Ambuye.
23
Paja mwamuna ndi mutu wa mkazi wake, monga momwe Khristu ali mutu wa Mpingo, umene uli thupi lake, ndipo Iye mwini ndi Mpulumutsi wa Mpingowo.
24
Tsono monga Mpingo umamvera Khristu, momwemonso akazi azimvera amuna ao pa zonse.
25
Inu amuna, muzikonda akazi anu, monga momwe Khristu adakondera Mpingo, nadzipereka chifukwa cha Mpingowo.
26
Adachita zimenezi kuti aupatule ukhale wakewake, atauyeretsa pakuutsuka ndi madzi ndiponso ndi mau ake.
27
Adafuna kuti akauimike pamaso pake uli waulemerero, wopanda banga kapena makwinya, kapena kanthu kena kalikonse kouipitsa, koma uli woyera ndi wangwiro kotheratu.
28
Momwemonso amuna azikonda akazi ao, monga momwe eniakewo amakondera matupi ao. Amene amakonda mkazi wake, ndiye kuti amadzikonda iye yemwe.
29
Palibiretu munthu amene amadana ndi thupi lake, koma amalidyetsa ndi kulisamala bwino, monga momwe Khristu amachitira Mpingo wake.
30
Amatero chifukwa Mpingowo ndi thupi lake, ndipo ife ndife ziwalo zake.
31
Paja mau a Mulungu akuti, “Nchifukwa chake mwamuna adzasiye atate ndi amai ake, nkukaphatikizana ndi mkazi wake, kuti aŵiriwo asanduke thupi limodzi.”
32
Mau ameneŵa akutiwululira chinsinsi chozama, ndipo ndikuti chinsinsicho nchokhudza Khristu ndi Mpingo.
33
Komabe akunenanso za inu, kuti mwamuna aliyense azikonda mkazi wake monga momwe amadzikondera iye mwini, ndiponso kuti mkazi aliyense azilemekeza mwamuna wake.
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 6 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6