bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ephesians 3
Ephesians 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 4 →
1
Nchifukwa chake ine Paulo ndimakupemphererani. Ndine womangidwa m'ndende chifukwa chotumikira Khristu ndi kugwirira ntchito inu amene simuli Ayuda.
2
Kumva mudamva za ntchito imene mwa ufulu wake Mulungu adandipatsa, yolalika pakati panu za kukoma mtima kwake.
3
Adandiwululira chinsinsi chake, monga ndidakulemberani mwachidule posachedwapa.
4
Pamene muŵerenga zimenezi, mungathe kuwona kuti ndikumvetsetsadi chinsinsi chonena za Khristu.
5
Chinsinsi chimenechi anthu a mibadwo yakale sadachidziŵe, koma Mulungu wachiwulula tsopano mwa Mzimu Woyera kwa atumwi ake oyera mtima, ndiponso kwa aneneri ake.
6
Chinsinsicho nchakuti mwa Uthenga Wabwino anthu a mitundu ina nawonso ngoyenera kulandira madalitso a Mulungu pamodzi ndi Ayuda. Pamodzinso ndi Ayuda ali ziwalo za thupi limodzi, ndipo mwa Khristu Yesu amalandira nao lonjezo la Mulungu.
7
Mwa kukoma mtima kwake Mulungu adandisandutsa wolalika Uthenga Wabwino umenewu, ndipo pakutero adaonetsapo mphamvu yake.
8
Pakati pa anthu onse a Mulungu ine ndine wamng'ono koposa, komabe Mulungu adandipatsa ineyo ntchito iyi, yakuti ndilalikire anthu a mitundu ina za chuma chopanda malire, chimene Mulungu amatipatsa mwa Khristu.
9
Adandipatsanso ntchito yofotokozera anthu onse za m'mene Mulungu adzachitira zonse zimene Iye adakonzeratu mwa chinsinsi chake. Mulungu amene adalenga zonse, adasunga chinsinsichi chikhalire, nthaŵi isanayambe.
10
Tsopano afuna kuti kudzera mwa Mpingo, mafumu ndi aulamuliro onse a Kumwamba adziŵe nzeru za Mulungu zamitundumitundu.
11
Mulungu adachita zimenezi kuti zichitikedi zimene Iye adakonzeratu mwa Khristu Yesu Ambuye athu chikhalire, nthaŵi isanayambe.
12
Popeza kuti timakhulupirira Iyeyu, tingathe kulimba mtima kuyandikira kwa Mulungu mosakayika konse.
13
Ndikukupemphani tsono kuti musataye mtima chifukwa chakuti ndikukusaukirani. Kwenikweni muyenera kunyadira chifukwa cha kusauka kwangaku.
14
Nchifukwa chake tsono ndikugwadira Atate,
15
amene banja lililonse Kumwamba ndi pansi pano limatchulidwa ndi dzina lao.
16
Ndikupempha Mulungu kuti kuchokera m'chuma cha ulemerero wake akupatseni mphamvu, ndipo mwa Mzimu wake Woyera alimbitse moyo wanu wauzimu.
17
Ndikupemphera kuti mwa chikhulupiriro chanu Khristu akhazikike m'mitima mwanu, kuti muzike mizu yanu m'chikondi, ndiponso kuti mumange moyo wanu wonse pa chikondi.
18
Ndikupempha Mulungu kuti, pamodzi ndi anthu ake onse, muthe kuzindikira kupingasa kwake ndi kutalika kwake, kukwera kwake ndi kuzama kwake kwa chikondi cha Khristu.
19
Ndithu ndikupemphera kuti mudziŵe chikondi chija cha Khristu chopitirira nzeru za anthu, kuti mudzazidwe kotheratu ndi moyo wa Mulungu mwini.
20
Ulemerero ukhale kwa Mulungu amene, mwa mphamvu yake yogwira ntchito mwa ife, angathe kuchita zochuluka kupitirira kutalitali zimene tingazipemphe kapena kuziganiza.
21
Mulungu alandire ulemuwo mu Mpingo ndi mwa Khristu Yesu pa mibadwo yonse mpaka muyaya. Amen.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6