bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ephesians 2
Ephesians 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 3 →
1
Kale inu munali akufa chifukwa cha zolakwa zanu ndi machimo anu.
2
Pa nthaŵi imeneyo, munkayenda m'zoipa potsata nzeru zapansipano, ndipo munkamvera mkulu wa aulamuliro amumlengalenga. Mkuluyo ndi mzimu woipa umene ukugwira ntchito tsopano pakati pa anthu oukira Mulungu.
3
Nthaŵi imene ija ifenso tonse tinali ndi moyo wonga wao, ndipo tinkatsata zilakolako za khalidwe lathu lokonda zoipa. Tinkachitanso zilizonse zimene matupi athu ndi maganizo athu ankasirira. Nchifukwa chake, mwachibadwa chathu, tinali oyenera mkwiyo wa Mulungu, monga anthu ena onse.
4
Koma Mulungu ndi wachifundo chachikulukulu, adatikonda ndi chikondi chachikulu kopambana.
5
Motero, pamene tinali akufa chifukwa cha machimo athu, Iye adatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu. Kukoma mtima kwa Mulungu ndi kumene kudakupulumutsani.
6
Popeza kuti tili mwa Khristu Yesu, Mulungu adachita ngati kutiwukitsa kwa akufa pamodzi naye, kuti choncho atipatse malo aulemu pamodzi naye m'dziko la Kumwamba.
7
Adachita zimenezi kuti mwa chifundo chake chimene adatichitira mwa Khristu Yesu, aonetse kwa nthaŵi zonse zam'tsogolo kuti ngwokomadi mtima kopambana.
8
Ndi kukoma mtima kwa Mulungu kumene kudakupulumutsani pakukhulupirira. Simudapulumuke chifukwa cha zimene inuyo mudaachita ai, kupulumuka kwanu ndi mphatso ya Mulungu.
9
Munthu sapulumuka chifukwa cha ntchito zake, kuwopa kuti angamanyade.
10
Mulungu ndiye adatipanga. Adatilenga mwa Khristu Yesu kuti moyo wathu ukhale wogwira ntchito zabwino zimene Iye adakonzeratu kuti tizichite.
11
Inu amene mtundu wanu sindinu Ayuda, kumbukirani m'mene munaliri kale. Ayuda amadzitchula oumbala, chifukwa cha mwambo umene amachita pa thupi lao, ndipo inu amakutchulani osaumbala.
12
Tsono kumbukirani kuti nthaŵi imene ija munali opanda Khristu. Munali alendo, ndipo simunali a mtundu wa anthu osankhidwa ndi Mulungu. Munali opanda gawo pa zimene Mulungu, mwa zipangano zake, adaalonjeza anthu ake. Munkakhala pansi pano opanda chiyembekezo, opandanso Mulungu.
13
Koma tsopano, mwa Khristu Yesu, inu amene kale lija munali kutali ndi Mulungu, mwakhala pafupi, chifukwa cha imfa ya Khristu.
14
Khristu mwini wake ndiye mtendere wathu. Iye adasandutsa Ayuda ndi anthu a mitundu ina kuti akhale amodzi. Pakupereka thupi lake, adagamula khoma la chidani limene linkatilekanitsa.
15
Iye adathetsa Malamulo a Mose pamodzi ndi malangizo ake ndi miyambo yake. Adachita zimenezi kuti kuchokera ku mitundu iŵiri ija, alenge mtundu umodzi watsopano, wokhala mwa Iye, kuti choncho adzetse mtendere.
16
Khristu adafa pa mtanda kuti athetse chidani, ndipo kuti mwa mtandawo aphatikize pamodzi m'thupi limodzi mitundu iŵiriyo, ndi kuiyanjanitsa ndi Mulungu.
17
Khristu adadzalalika Uthenga Wabwino wa mtendere kwa inu a mitundu inanu, amene munali kutali ndi Mulungu, ndiponso kwa Ayuda, amene anali pafupi naye.
18
Tsopano kudzera mwa Khristu ife tonse, Ayuda ndi a mitundu ina, tingathe kufika kwa Atate mwa Mzimu Woyera mmodzi yemweyo.
19
Nchifukwa chake tsono, inu amene simuli Ayuda, sindinunso alendo kapena akudza ai, koma ndinu nzika pamodzi ndi anthu ake a Mulungu, ndiponso ndinu a m'banja lake la Mulungu.
20
Ndinu omangidwa pamodzi m'nyumba yomangidwa pa maziko amene ndi atumwi ndi aneneri, ndipo Khristu Yesu mwini ndiye mwala wapangodya.
21
Mwa Iyeyu nyumba yonse ikumangidwa molimba, ndipo ikukula kuti ikhale nyumba yopatulika ya Ambuye.
22
Mwa Iyeyu inunso mukumangidwa pamodzi ndi ena onse, kuti mukhale nyumba yokhalamo Mulungu mwa Mzimu Woyera.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6