bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Ephesians 6
Ephesians 6
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
1
Inu ana, popeza kuti ndinu ake a Khristu, muzimvera anakubala anu, pakuti zimenezi ndiye zoyenera.
2
Mau a Mulungu akuti, “Lemekeza atate ako ndi amai ako.” Limeneli ndiye lamulo loyamba kukhala ndi lonjezo.
3
Lonjezolo likuti, “Ukatero, udzakhala wodala, ndipo moyo wako udzakhala wautali pansi pano.”
4
Inu atate, musamaŵapsetsa mtima ana anu, koma muziŵalera bwino pakuŵasungitsa mwambo ndi malangizo a Ambuye.
5
Inu akapolo, ambuye anu a pansi pano muziŵamvera mwamantha ndi monjenjemerera. Muzichita zimenezi ndi mtima woona, ngati kuti mukuchitira Khristu yemwe.
6
Musazichite mwachiphamaso chabe, ngati kuti mukungofuna kukondweretsa anthu. Koma ngati akapolo a Khristu, muzichita ndi mtima wonse zimene Mulungu afuna.
7
Muzitumikira mosangalala, ngati kuti mukutumikira Ambuye, osati anthu chabe.
8
Mukudziŵa kuti Ambuye adzampatsa munthu aliyense mphotho chifukwa cha ntchito yake yabwino imene adaigwira, ngakhale munthuyo ndi kapolo kapena mfulu.
9
Inu ambuye, muziŵachitiranso chimodzimodzi akapolo anu, ndipo muleke zoŵaopseza. Paja mukudziŵa kuti iwoŵa ndi inuyo, nonse muli ndi Mbuye wanu Kumwamba, ndipo Iyeyo alibe tsankho.
10
Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye, mwa mphamvu yao yaikulu.
11
Valani zida zonse zimene Mulungu akupatsani, kuti muthe kulimbika polimbana ndi ndale za Satana.
12
Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.
13
Nchifukwa chake valani zida zonse za Mulungu. Pamenepo mudzatha kulimbika, osagonja pa tsiku loipa, ndipo mutatsiriza kulimbanaku, mudzaimabe kuti nji.
14
Imirirani tsono mutavala choona ngati lamba m'chiwuno mwanu. Valani chilungamo ngati chovala chachitsulo chotchinjirizira pachifuwa panu.
15
Ndipo changu chanu polalika Uthenga Wabwino wa mtendere chikhale ngati nsapato zanu.
16
Nthaŵi zonse mukhale ndi chikhulupiriro ngati chishango chanu chokutetezani, chimene mudzatha kuzimitsira mivi yonse yoyakamoto ya Satana.
17
Landirani chipulumutso ngati chisoti chanu, ndi mau a Mulungu ngati lupanga limene Mzimu Woyera akupatsani.
18
Chitani zonse mopemphera, ndi kupempha chithandizo cha Mulungu nthaŵi zonse. Nthaŵi iliyonse muzipemphera motsogoleredwa ndi Mzimu Woyera. Nchifukwa chake muchezere kupemphera mosalekeza, kupempherera anthu onse a Mulungu.
19
Inenso muzindipempherera, kuti Mulungu aike mau m'kamwa mwanga pamene ndizilankhula, kuti ndidziŵitse anthu chinsinsi cha Uthenga Wabwino molimba mtima.
20
Ngakhale ndili womangidwa m'ndende, ndine nthumwi ndithu chifukwa cha Uthenga Wabwinowu. Mundipempherere tsono kuti ndizilankhula molimba mtima za Uthenga Wabwinowu, monga ndiyenera kulankhulira.
21
Tikiko adzakudziŵitsani zonse za ine ndi zimene ndikuchita. Iyeyu ndi mbale wathu wokondedwa, ndiponso mtumiki wokhulupirika pa ntchito ya Ambuye.
22
Ndikumtuma kwa inu kuti mudziŵe za m'mene tiliri, ndipo kuti akulimbitseni mtima.
23
Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu apatse abale onse mtendere, chikondi ndi chikhulupiriro.
24
Onse okonda Ambuye athu Yesu Khristu ndi chikondi chosafa, Mulungu aŵadalitse.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
All chapters:
1
2
3
4
5
6