bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Lamentations 1
Lamentations 1
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 2 →
1
Ha! Mzinda wa Yerusalemu wakhala wokhawokha, m'menemo kale udaali wodzaza ndi anthu! Kale unali wotchuka pakati pa mitundu ya anthu, koma tsopano wasanduka ngati mkazi wamasiye. Kale unali mzinda wolemekezeka koposa mizinda ina, koma tsopano wasanduka kapolo.
2
Ukungolira usiku wonse, misozi ikungoti mbwembwembwe pamasaya pake. Mwa onse amene ankaukonda, palibe ndi mmodzi yemwe amene watsala woti aziwusangalatsa. Abwenzi ake onse auchita zaupandu, onse asanduka adani ake.
3
Ayuda apita ku ukapolo kukazunzika, ndi kukagwira ntchito yakalavulagaga. Akukhala m'maiko ena, osaona malo opumulira. Onse oŵapirikitsa aŵapeza, ali pa mavuto zedi.
4
Miseu yopita ku Ziyoni yaŵirira, chifukwa palibe wopitako kuti akapembedze pa masiku achikondwerero. Zipata zake zonse zili pululu, ansembe ake akungodandaula. Anamwali ake aja mtima wao ukupweteka, ndithu Ziyoni ali pa masautso oopsa.
5
Adani ake asanduka omulamulira, odana naye akupeza bwino, popeza kuti Chauta wamugwetsa m'mavuto chifukwa cha machimo ochuluka a anthu ake. Ana ake amuchokera, atengedwa ukapolo ndi adani.
6
Ulemerero wonse wa Ziyoni wachokeratu. Akalonga ake asanduka ngati mphoyo zosoŵa msipu. Ankathaŵa opanda ndi mphamvu zomwe, pofika adani.
7
Pa masiku a mavuto ake ndi a kuzunzika kwake, Yerusalemu amakumbukira zabwino zonse zimene anali nazo masiku amakedzana. Pamene anthu ake adagwa m'manja mwa adani, panalibe womuthandiza. Adani ake ankamupenyetsetsa monyodola namaseka kugwa kwake.
8
Yerusalemu adachimwa kwambiri, motero wasanduka wonyansa. Onse amene ankamulemekeza, akumunyoza tsopano, chifukwa aona maliseche ake. Iyeyo akungobuula ndipo akuyang'ana kumbali.
9
Uve wake unkaonekera poyera, iye osaganizako za tsoka lake lakutsogolo. Nchifukwa chake kugwa kwake kunali koopsa, ndipo panalibe womuthuzitsa mtima. Akungoti, “Inu Chauta, muyang'ane mavuto anga, pakuti adani anga apambana.”
10
Adani adamulanda chuma chake chonse. M'malo ake oyera mudaloŵa anthu a mitundu ina, amene Inu Chauta mudaŵaletsa kuloŵa mumsonkhano mwanu.
11
Anthu ake onse amabuula akamafunafuna chakudya. Chuma chao amagulitsana ndi chakudya, kuti apezenso mphamvu. Akuti, “Inu Chauta penyani, muwone m'mene akundinyozera.”
12
Kodi zimenezi mukuziyesa zachabe, inu amene mukudutsanu? Tangopenyani, muwone ngati pali mavuto ena onga angaŵa, mavuto amene Chauta adandigwetsamo, pamene adandikwiyira koopsa.
13
Adatumiza moto kuchokera Kumwamba. Udaloŵa mpaka m'kati mwa mafupa anga. Adayala ukonde kuti akole mapazi anga, nandibweza. Adandisiya ndili ndi chisoni chachikulu, ndili wolefuka tsiku lonse.
14
Zolakwa zanga adazimanga pamodzi kuti zikhale ngati goli. Adazimanga ndi manja ake. Adazimangirira m'khosi mwanga, adafooketsa mphamvu zanga. Chauta wandipereka kwa anthu amene sindingathe kulimbana nawo.
15
Chauta adaŵamwaza anthu anga onse amphamvu amene ankakhala nane. Adasonkhanitsa gulu lina la anthu kuti liwononge anyamata anga. Chauta adapondereza Ayuda, anthu ake opatulika, monga m'mene anthu amachitira mphesa mopondera mwake.
16
Chifukwa cha zimenezi ndikulira, misozi ili mbwembwembwe m'masomu. Pakuti wondisangalatsa sali pafupi, wondilimbitsa mtima ali kutali. Anthu anga asiyidwa chifukwa mdani watigonjetsa.
17
Ziyoni wakweza manja, koma palibe ndi mmodzi yemwe womusangalatsa. Chauta adalamula kuti Yakobe anansi ake asanduke adani ake. Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao.
18
Pamenepo Chauta wakhoza, chifukwa ndine ndidapandukira malamulo ake. Imvani, inu anthu a mitundu yonse, onani kuvutika kwanga. Anamwali anga ndi anyamata anga atengedwa ukapolo.
19
Ndidaitana abwenzi anga, koma iwo adanditaya. Ansembe anga ndi akuluakulu anga adafa mu mzinda, pamene ankafunafuna chakudya kuti mphamvu zao zibwereremo,
20
Onani Inu Chauta m'mene ndavutikira mumtima mwanga, moyo wanga wazunzika zedi. Mtima wanga wakongonyala, chifukwa choti ndapanduka kwambiri. Mu mseu anthu akuphedwa ndi lupanga, m'nyumbanso ndi imfa yokhayokha.
21
Anthu akundimva pamene ndikudandaula, koma palibe wondisangalatsa. Adani anga onse atamva za tsoka langa, adakondwa chifukwa cha zimene mudachita. Tsiku limene mudalonjeza lija mulifikitse ndithu. Nawonso adzasauke ngati ine ndemwe.
22
Ntchito zao zonse zoipa mudzaŵaimbe nazo mlandu. Muŵalange monga mudandilangira ine chifukwa cha zolakwa zanga zonse. Ndikubuula kwambiri, ndipo mtima wanga wafookeratu.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5