bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Lamentations 2
Lamentations 2
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
1
Chauta wakwiya kwambiri, taonani m'mene waphimbira Ziyoni ndi mdima! Ulemerero wa Israele wautaya pansi kuuchotsa Kumwamba. Pa tsiku la mkwiyo wake sadakumbukirenso kuti Ziyoni anali ngati mphondero yake.
2
Chauta adaononga midzi yonse ya Yakobe popanda ndi chifundo chomwe. Chifukwa cha kupsa mtima adathyola malinga a mizinda ya Yuda. Adagwetsera pansi mochititsa manyazi, ufumu wa Israele ndi olamulira ake.
3
Chauta atapsa mtima adathyola nyonga zomwe ankanyadira Israele. Adabweza dzanja lake loteteza, adani atayandikira. Mkwiyo wake udalanga fuko la Yakobe ngati moto walaŵilaŵi wonka nuwononga zonse.
4
Adalozetsa mivi yake kwa ife ngati mdani wathu, wasamuladi dzanja ngati mdani. Adapha onse amene tinkaŵayang'ana monyadira, pakati pa anthu a mu mzinda wa Ziyoni. Ukali wake unkachita kuyaka ngati moto.
5
Chauta adakhala ngati mdani, adaononga Israele. Adaononga nyumba zonse zachifumu, malinga ao onse adaŵasandutsa mabwinja. Adachulukitsa kulira ndi kudandaula pakati pa anthu a ku Yuda.
6
Adapasula Nyumba yake ngati khumbi lam'munda, malo ake a msonkhano adaŵasandutsa bwinja. Chauta adathetseratu ku Ziyoni masiku achikondwerero ndi a Sabata. Ndipo atakwiya kwambiri adanyoza mfumu pamodzi ndi ansembe.
7
Chauta adanyoza ngakhale guwa lake lomwe, ndipo adaŵakana malo ake opatulika. Adapereka malinga a nyumba zake zachifumu m'manja mwa adani ake. M'nyumba yeniyeni ya Chauta adaniwo adafuula ndi chimwemwe monga momwe zimachitikira pa tsiku lachikondwerero.
8
Chauta adaatsimikiza zoti aononge malinga a mzinda wa Ziyoni. Adauyesa ndi chingwe chake, ndipo sadafune kuleka kuuwononga kotheratu. Adaliritsa okhala pa malinga ndi pa makoma ake, onsewo akuzunzikira limodzi.
9
Zipata za mzindawo zakwiririka pansi. Mipiringidzo yake yathyoka ndi kusakazika. Mfumu yake ndi akalonga ake ali ku ukapolo pakati pa anthu akunja, malamulo a Mulungu palibenso oŵalalika. Aneneri ake omwe sakuchitanso zija zoona zinthu m'masomphenya zochokera kwa Mulungu.
10
Akuluakulu a mu mzinda wa Ziyoni, akhala pansi atangoti chete. Adzithira fumbi kumutu, ndipo avala ziguduli. Anamwali a ku Yerusalemu aŵeramitsa mitu yao pansi.
11
Maso anga atopa nkulira, moyo wanga wazunzika zedi, Mumtima mwanga mwadzaza chisoni, chifukwa choti anthu anga aonongeka, ana ndi makanda omwe akukomoka m'miseu yamumzinda.
12
Anawo akufunsa amai ao kuti, “Kodi chakudya ndi chakumwa tingazipeze kuti?” Akufunsa zimenezi pamene akukomoka m'miseu yamumzinda ngati anthu olasidwa. Akuthatha ndi moyo pa mfukato wa amai ao.
13
Iwe mzinda wa Yerusalemu, ndinganene chiyani za iwe, kaya nkukuyerekeza ndi chiyani? Iwe mzinda wangwiro wa Ziyoni, kodi ndingakufanizire ndi yani, kuti choncho ndikusangalatse? Kuwonongeka kwako nkwakukulu ngati nyanja. Ndani angathe kukukonzanso?
14
Zinthu zimene aneneri ako adakuwonera m'masomphenya zinali zabodza ndi zonyenga. Iwo sadaonetse uchimo wako, kuti ukhalenso pabwino. Mau amene adakutengeraniwo anali abodza ndi osokeretsa.
15
Onse odutsa m'njira akukuwombera m'manja mokunyodola. Akukutsonya ndi kukupukusira mitu, iwe mzinda wa Yerusalemu. Akunena kuti, “Kodi mzinda uja ndi uwu umene kale lija ankautcha wodala kotheratu, mzinda wokondweretsa dziko lonse lapansi?”
16
Adani ako onse akukuyasamira kukamwa mwaukali, ndipo akukunyodola. Akukutsonya ndi kumakukuta mano ao namanena kuti, “Tafikapodi pousakaza! Ah! Tsiku lija tinkafunali ndi lero. Tagonera, taliwonadi.”
17
Chauta wachitadi zimene adakonzekera kuti achite. Wachitadi zimene ankanena moopseza. Monga momwe adaakonzeratu masiku amakedzana, wakuwononga mopanda chifundo, walola adani kuti akondwe chifukwa cha tsoka lako, ndipo wakulitsa kwambiri mphamvu za adani ako.
18
Fuulani kwamphamvu kwa Ambuye, inu anthu a ku Ziyoni. Misozi yanu ichite kuti yoyoyo, ngati mtsinje, usana ndi usiku. Musadzipatse nthaŵi yoti mupumule. Misozi yanu isalekeze.
19
Dzukani, ndipo mufuule usiku pachiyambi penipeni pa maulonda. Nenani zanu zonse zakukhosi pamaso pa Ambuye. Kwezani manja ndi kupemphera kwa Ambuyewo chifukwa cha moyo wa ana anu amene akukomoka ndi njala m'miseu yonse.
20
Inu Chauta onani, ndipo mupenye! Kodi ndani amene Inu mwamuvuta chotereyu? Kodi akazi achite kudya ana ao, ana amene iwo omwe adaŵalera bwino? Nanga ansembe ndi aneneri, kodi achite kuŵaphera m'malo opatulika a Ambuye?
21
Anyamata ali gonegone m'miseu pamodzi ndi nkhalamba zomwe. Anamwali anga ndi anyamata anga aphedwa ndi nkhondo. Mwaŵapha pa tsiku la mkwiyo wanu, mwaŵapha mopanda chifundo.
22
Monga momwe mumaitanira ku chikondwerero, ndi m'mene mwandiitanira zoopsa kuchokera mbali zonse. Inu Chauta, pa tsiku la mkwiyo wanu, palibe amene adathaŵako kapena kupulumuka. Onse amene ndidaŵabala ndi kuŵalera, adani anga adaŵaononga.
← Chapter 1
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 3 →
All chapters:
1
2
3
4
5