bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Lamentations 5
Lamentations 5
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
1
Inu Chauta, kumbukirani zimene zatigwera. Muyang'ane, muwone m'mene anthu akutinyozera.
2
Choloŵa chathu chaperekedwa kwa alendo, nyumba zathu zili m'manja mwa anthu akudza.
3
Ife tili ngati ana amasiye, opanda bambo wao. Amai athu ali ngati akazi amasiye.
4
Madzi amene timamwaŵa tiyenera kuchita chogula. Nkhuni zosonkhera moto nzoyeneranso kuchita chogula.
5
Amatikankha mwankhanza, goli lili m'khosi mwathu. Ngakhale titope, satilola kupumula.
6
Tidachita chibwenzi ndi Aejipito ndiponso ndi Aasiriya, kuti mwina iwo nkutipatsako chakudya.
7
Makolo athu adachimwa, ndipo adatha. Ndiye ife tatengana nacho chilango chifukwa cha machimo ao.
8
Amene akutilamulira ndi akapolo, palibe ndi mmodzi yemwe wotipulumutsa m'manja mwao.
9
Pofunafuna chakudya, timagwa m'zoopsa chifukwa cha anthu opha anzao ku chipululu.
10
Khungu lathu likutentha ngati lili m'ng'anjo chifukwa cha ululu wa njala.
11
Ku Ziyoni akazi akuŵachita zadama mwakhakhamizo. M'mizinda ina ya ku Yuda anamwali akuŵachita chimodzimodzi.
12
Akalonga akuŵapachika pomangirira manja ao, akuluakulu sakuŵalemekeza konse.
13
Achinyamata akuŵakakamiza kupera tirigu, anyamata akudzandira nayo mitolo ya nkhuni.
14
Akuluakulu adachokapo pa bwalo la mzinda, achinyamata nyimbo zao zija zati zi!
15
Chimwemwe chachoka m'mitima mwathu. Kuvina kwathu kwasanduka kulira.
16
Chisoti chathu chaufumu chachoka kumutu, kugwa pansi. Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa.
17
Nchifukwa chake mitima yathu yalefuka, chifukwa cha zimenezi m'masomu mwachita chidima.
18
Phiri la Ziyoni lasanduka bwinja, nkhandwe zikungoyendayendapo.
19
Koma Inu Chauta, ndinu mfumu mpaka muyaya, mpando wanu waufumu udzakhalapo pa mibadwo yonse.
20
Chifukwa chiyani mwakhala mukutiiŵala nthaŵi yonse? Chifukwa chiyani mwatisiya nthaŵi yaitali chotere?
21
Inu Chauta mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere mwakale. Mutipatsenso masiku onga amakedzana aja.
22
Kaya, monga nkuti mwatitayiratu? Monga nkuti mwatikwiyira kopitirira?
← Chapter 4
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
All chapters:
1
2
3
4
5