bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Lamentations 4
Lamentations 4
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 5 →
1
Ha! Golide wathu tsopano wathimbirira kwambiri. Golide wathu wosalala uja wasinthika kotheratu. Miyala ya ku malo oyera yamwazikana, ili vuu, ku mphambano zonse za miseu.
2
Onani ana okondedwa a m'Ziyoni amene kale anali ngati golide kwa ife, tsopano akuŵayesa mbiya zadothi zimene woumba amachita kuumba ndi manja ake.
3
Ngakhale nkhandwe siziwumira bere, zimayamwitsa ana. Koma anthu anga ndi ankhalwe, ali ngati nthiŵatiŵa zakunkhalango.
4
Lilime la mwana wakhanda limakangamira kukhosi chifukwa cha ludzu. Ana aang'ono amafuna chakudya, koma palibe woŵapatsa mpang'ono pomwe.
5
Amene ankadya zokoma akuthera m'miseu. Amene ankavala zokongola zokhazokha tsopano ali gone pa dzala.
6
Chilango cha anthu anga nchachikulu kwambiri kupambana chilango cha anthu a ku Sodomu, amene adalangidwa pa kamphindi chabe, ndipo panalibe wochitapo kanthu kuti aŵathandize.
7
Akalonga ake anali oŵala koposa chisanu chambee, oyera kuposa mkaka. Matupi ao anali ofiira kupambana miyala ya rubi. Anali ndi maonekedwe okongola ngati miyala ya safiro.
8
Koma tsopano nkhope zao zasanduka zakuda ngati mwaye. Palibe amene akuŵazindikira m'miseu. Khungu lao lachita makwinyamakwinya, langoti gwa ngati mtengo.
9
Amene adaphedwa pa nkhondo anali amwai kwambiri kupambana amene adafa ndi njala. Ameneŵa ankafooka pang'onopang'ono mpaka kutsirizika, chifukwa chosoŵa chakudya.
10
Ngakhale akazi achifundo ndi manja ao omwe adafika pophika ana ao. Ana aowo adasanduka chakudya chao pa nthaŵi imene anthu anga adaonongedwa.
11
Chauta adakwiya kwambiri, nagwetsa pansi mkwiyo wake wamotowo. Adayatsa moto ku Ziyoni ndipo motowo udaononga maziko a mzindawo.
12
Mafumu a pa dziko lapansi sadakhulupirire, kapena wina aliyense wokhala pa dziko lapansi, kuti adani kapena ankhondo nkuloŵa pa zipata za Yerusalemu.
13
Zimenezi zidachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi ntchito zoipa za ansembe ake, amene ankakhetsa magazi a anthu osalakwa m'malinga amumzindamu.
14
Ankangoyendayenda m'miseu ngati akhungu, zovala zao zili magazi psu, mwakuti palibe munthu woti nkuzikhudza.
15
Anthu ankaŵafuulira kuti, “Chokani, inu anthu oipitsidwa. Chokani! Chokani apa! Musakhudzane ndi ife!” Motero adathaŵa, namangoyendayenda, anthu a mitundu ina ankati, “Asadzakhalenso ndi ife.”
16
Chauta mwiniwake ndiye adaŵamwaza, salabadakonso za iwo. Ansembe sadaŵalemekezenso. Akuluakulu sadaŵamvere chifundo.
17
Maso athu adatopa nkuyang'anira chithandizo, koma popanda phindu. Tidadikiradikira mtundu wina wa anthu amene sangathe kutipulumutsa.
18
Anthu ankangotilondola nthaŵi zonse, kotero kuti sitinkathanso kuyenda m'miseu yathu. Masiku athu ankacheperachepera, imfa yathu idaayandikira, ndithu chimalizo chinali chitafika.
19
Anthu otilondolawo anali aliŵiro kupambana adembo ouluka mu mlengalenga. Adatipirikitsa ku mapiri, adatilalira ku chipululu kuti atiphe.
20
Wodzozedwa wa Chauta uja, amene anali ngati mpweya wotipatsa moyo, adakodwa m'misampha mwao. Iyeyo amene tinkati adzatithandiza ife okhala pakati pa anthu a mitundu ina.
21
Kondwerani ndipo musangalale, inu anthu a ku Edomu, inu anthu okhala m'dziko la Uzi. Inunso chikho cha mavuto chidzakufikirani pa nthaŵi yanu. Mudzaledzera mpaka kuvula zovala.
22
Chilango cha machimo anu, inu anthu a ku Ziyoni, chatheratu, Chauta satalikitsa ukapolo wanu. Koma inu anthu a ku Edomu, Chauta adzakulangani chifukwa cha machimo anu. Zolakwa zanu adzaziwulula poyera.
← Chapter 3
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 5 →
All chapters:
1
2
3
4
5