bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
/
Lamentations 3
Lamentations 3
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
1
Ine ndine munthu amene ndaona mavuto, ndalangidwa ndi ndodo ya ukali wa Mulungu.
2
Adandiyendetsa ndi kubwera nane mu mdima mopanda nkuŵala komwe.
3
Zoonadi adandikantha ndi dzanja lake, ankachita zimenezi mobwerezabwereza tsiku lonse.
4
Adandipweteka m'thupi lonse, ndipo adaphwanya mafupa anga onse.
5
Adandizinga ndi kundizunguliza ponseponse ndi mazunzo ndi masautso.
6
Adanditaya m'malo a mdima wabii, kuti ndikhale ngati munthu wofa kalekale.
7
Adanditsekera m'malinga kuti ndisathaŵe. Adandimanga ndi maunyolo olemera kwambiri.
8
Ngakhale pamene ndinkafuula ndi kupempha chithandizo, sankalimva pemphero langalo.
9
Adanditsekera mseu ndi miyala yosema, ndipo adakhotetsa njira zanga.
10
Adandiwukira ngati chimbalangondo kapena ngati mkango wondilalira.
11
Adandisiyitsa njira nanding'ambang'amba, kenaka nkundisiya.
12
Adakoka uta wake nandiyesa chinthu chochitirapo chandamale.
13
Adalasa mtima wanga ndi mivi ya m'phodo lake.
14
Ndasanduka chinthu chomachiseka, kwa anthu a mitundu ina, amandiimba nyimbo zondinyoza.
15
Chauta adandidyetsa zoŵaŵa, adandimwetsa chivumulo.
16
Adandigulula mano ndi timiyala, adandivimviniza m'phulusa.
17
Mumtima mwanga mulibenso mtendere, chimwemwe ndidachiiŵaliratu.
18
Choncho ndikuti, “Ulemerero wanga wonse watha, chandithera chikhulupiriro cholandira kanthu ka Chauta.”
19
Ndimakumbukira masautso anga ndi kuzunzika kwanga, zili ngati chivumulo ndi ndulu.
20
Nthaŵi zonse ndimangozilingalirabe zimenezi, nkuwona ndataya mtima.
21
Koma pali chinanso chimene ndimachikumbukira, chimenecho ndicho chimandilimbitsa mtima.
22
Chikondi chosasinthika cha Chauta sichitha, chifundo chakenso nchosatha.
23
M'maŵa mulimonse zachifundozo zimaoneka zatsopano, chifukwa Chauta ndi wokhulupirika kwambiri.
24
Chauta ndiye zanga zonse motero ndimadalira Iyeyo.
25
Chauta ndi wabwino kwa amene amamudalira, kwa onse amene amafuna kuchita zimene Iye afuna.
26
Nkwabwino kumdikira Chauta mopirira kuti aonetse chipulumutso chake.
27
Nkwabwinonso kuti munthu asenze goli la kupirira pamene iye ali pa unyamata.
28
Akhale pansi yekha mkachete, pamene Chauta amsenzetsa golilo.
29
Agwetse nkhope yake pa fumbi, mwina chikhulupiriro nkukhalapobe.
30
Apereke tsaya lake kwa wofuna kumumenya, apirire zomunyoza zonse.
31
Ndithudi Ambuye sadzataya atumiki ao mpaka muyaya.
32
Angathe kulanga mwankhalwe, komabe adzaonetsa chifundo, chifukwa chikondi chao nchochuluka.
33
Savutitsa mwadala, sakonda kusautsa munthu aliyense.
34
Chauta amadziŵa pamene akulu amapondereza am'ndende am'dziko.
35
Amadziŵa pamene olamula amapsinja munthu popanda chilungamo pamaso pa Wopambanazonse.
36
Pamene iwo amagamula mlandu mokondera, kodi Ambuye saona zimenezi?
37
Ndani angathe kulamula kuti zakutizakuti zichitike, ngati Chauta waletsa zimenezo?
38
Paja madalitso ndi matsoka zonse nzochokera kwa Wopambanazonse.
39
Munthu wina aliyense wamoyo angadandaulirenji pamene alangidwa chifukwa cha machimo ake?
40
Tiyeni tiŵaone ndi kuŵayesa makhalidwe athu, ndipo tibwerere kwa Chauta.
41
Tikweze mitima yathu ndi manja athu kwa Mulungu kumwamba.
42
Ifeyo tachimwa, ndipo tapanduka, tsono Inu simudakhululuke.
43
Mwatipirikitsa muli okwiya, ndipo mwatipha mopanda chifundo.
44
Mwadzibisa ndi mitambo, kumene mapemphero athu sangathe kufikako.
45
Mwatisandutsa onyozeka ngati zinyatsi, m'maso mwa anthu a mitundu ina.
46
Adani athu akutinyodola.
47
Tagwa m'zoopsa ndi m'mbuna, m'chipasupasu ndi m'chiwonongeko.
48
M'maso mwanga misozi ikungoti mbwembwembwe, chifukwa anthu anga aonongeka.
49
Ndidzalira misozi kosalekeza ndiponso osapumulira,
50
mpaka Chauta adzayang'ane pansi kuchokera kumwamba ndi kuwona mavuto anga.
51
Mtima wanga ukupweteka poona zimene zikuŵachitikira akazi a mumzinda mwanga.
52
Amene anali adani anga popanda chifukwa, akhala akundisaka ngati mbalame.
53
Adandiponya m'dzenje ndili moyo, nkumandiponya miyala ndili momwemo.
54
Madzi adaamiza mutu wanga, ine nkunena ku, “Mayo, ndikufa ine!”
55
Ndidatama dzina lanu mopemba, Inu Chauta, ndili m'dzenje lozamalo.
56
Inu mudamva mau anga akuti, “Musagonthetse dala makutu anu pamene ndikupemphera kuti mudzandithandize.”
57
Inu mudasendera pafupi pamene ndinkakutamani mopemba, ndipo mudanena kuti “Usachite mantha.”
58
Inu Chauta, mudandithandiza pa mlandu wanga, ndipo mudaombola moyo wanga.
59
Inu Chauta, mudaona zoipa zimene anthu adandichita, tsono muweruze ndinu pamenepo.
60
Mudaona m'mene ankandilipsirira, mudaonanso ziwembu zimene adandichita.
61
Inu Chauta mudamva kunyoza kwao koopsa ndiponso ziwembu zimene ankakonzekera kuti andichite.
62
Mudamva manong'onong'ono ao, ndi m'mene adani anga ankandinenera tsiku lonse.
63
Onani m'mene akundinyozera, m'maŵa ndi madzulo akungokhalira kundiimba nyimbo.
64
Inu Chauta, muŵalange potsata zolakwa zao, potsata ntchito zimene adachita.
65
Muŵazamitse mtima muŵatemberere basi.
66
Inu Chauta, muŵapirikitse mwaukali, muŵaonongeretu pa dziko lapansi.
← Chapter 2
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 4 →
All chapters:
1
2
3
4
5