bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Samuel 1
1 Samuel 1
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 2 →
1
NDIPO panali munthu wina wa ku Ramatayimu Zofimu, wa dziko la mapiri la Efraimu, dzina lace ndiye Elikana, mwana wace wa Yerohamu, mwana wa Elihu, mwana wa Tohu, mwana wa Zufu, M-efraimu.
2
Iyeyu anali nao akazi awiri; winayo dzina lace ndi Hana, mnzace dzina lace ndi Penina. Ndipo Penina anaona ana, koma Hana anali wouma.
3
Ndipo munthuyu akakwera caka ndi caka kuturuka m'mudzi mwace kukalambira ndi kupereka nsembe kwa Mulungu wa makamu m'Silo. Ndipo pomwepo panali ana amuna awiri a Eli, ansembe a Yehova, ndiwo Hofeni ndi Pinehasi.
4
Ndipo pofika tsiku lakuti Elikana akapereka nsembe, iye anapatsa Penina mkazi wace, ndi ana ace onse, amuna ndi akazi, gawo lao;
5
koma anapatsa Hana magawo awiri, cifukwa anakonda Hana, koma Mulungu anatseka mimba yace.
6
Ndipo womnyodolayo anamputa kwakukuru, kuti amuwawitse mtima, popeza Yehova anatseka mimba yace.
7
Ndipo popeza munthuyo adatero caka ndi caka, popita mkaziyo ku nyumba ya Yehova, mnzaceyo amamputa; cifukwa cace iye analira misozi, nakana kudya.
8
Ndipo mwamuna wace Elikana anati kwa iye, Hana, umaliriranji? ndipo umakaniranji kudya? ndipo mtima wako uwawa ninji? Ine sindiri wakuposa ana khumi kwa iwe kodi?
9
Comweco Hana anauka atadya m'Silo, ndi kumwa. Ndipo Eli wansembeyo anakhala pa mpando wace pa mphuthu ya Kacisi wa Yehova.
10
Ndipo mkaziyo anali ndi mtima wowawa, napemphera kwa Yehova, naliratu misozi;
11
nalonjeza cowinda, nati, Yehova wa makamu, mukapenyera ndithu kusauka kwa mdzakazi wanu, ndi kukumbukila ine, ndi kusaiwala mdzakazi wanu, mukapatsa mdzakazi wanu mwana wamwamuna, ine ndidzampereka kwa Yehova masiku onse a moyo wace, ndipo palibe lumo lidzapita pamutu pace.
12
Ndipo panali, m'mene iye analikupempherabe pamaso pa Yehova, Eli anapenyerera pakamwa pace.
13
Koma Hana ananena mu mtima; milomo yace inatukula, koma mau ace sanamveka; cifukwa cace Eli anamuyesa woledzera.
14
Ndipo Eli anati kwa iye, Udzaleka liti kuledzera? cotsa vinyo wako.
15
Ndipo Hana anayankha, nati, Iai, mbuyanga. Ine ndiri mkazi wa mtima wacisoni; sindinamwa vinyo kapena cakumwa cowawa, koma ndinatsanulira mtima wanga pamaso pa Yehova.
16
Musamandiyesa mdzakazi wanu mkazi woipa; cifukwa kufikira lero ndinalankhula mwa kucuruka kwa kudandaula kwanga ndi kubvutika kwanga.
17
Pamenepo Eli anayankha nati, Pita ndi mtendere; ndipo Mulungu wa Israyeli akupatse copempha cako unacipempha, kwa iye.
18
Ndipo iye anati, Mumkomere mtima mdzakazi wanu. Comweco mkaziyo anamuka, nakadya, ndi nkhope yace siinakhalanso yacisoni.
19
Ndipo iwo anauka mamawa, nalambira pamaso pa Yehova, nabwerera, nafikanso kwao ku Rama; ndipo Elikana anadziwa mkazi wace Hana, Yehova namkumbukila iye.
20
Ndipo panali pamene nthawi yace inafika, Hana anaima, nabala mwana wamwamuna: namucha dzina lace Samueli, nati, Cifukwa ndinampempha kwa Yehova,
21
Ndipo munthuyo Elikana, ndi a pa banja lace onse, anakwera kukapereka kwa Yehova nsembe ya caka ndi caka, ndi ya cowinda cace.
22
Koma Hana sadakwera, cifukwa kuti anati kwa mwamuna wace, Sindidzakwerako kufikira mwanayo ataleka kuyamwa, pamenepo ndidzapita naye kuti aoneke pamaso pa Yehova, ndi kukhalako cikhalire.
23
Ndipo Elikana mwamuna wace anati, Cita cimene cikukomera nukhale kufikira utamletsa kuyamwa; komatu Yehova akhazikitse mau ace. Comweco mkaziyo anakhala nayamwitsa mwana wace, kufikira anamletsa kuyamwa.
24
Ndipo atamletsa kuyamwa anakwera naye, pamodzi ndi ng'ombe ya zaka zitatu, ndi efa wa ufa, ndi thumba la vinyo, nafika naye ku nyumba ya Yehova ku Silo; koma mwanayo anali wamng'ono.
25
Ndipo iwo anapha ng'ombe, nabwera naye mwanayo kwa Eli.
26
Ndipo mkaziyo ananena, Mbuye wanga, pali moyo wanu, zoonadi ine ndine mkazi uja ndidaima pano ndi inu, ndi kupemphera kwa Yehova.
27
Ndinampempha mwanayu; ndipo Yehova anandipatsa copemphacanga ndinacipempha kwa iye;
28
cifukwa cace inenso ndinampereka kwa Yehova; masiku onse a moyo wace aperekedwa kwa Yehova. Ndipo analambira Yehova pomwepo.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31