bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Samuel 8
1 Samuel 8
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 9 →
1
Ndipo kunali, pamene Samueli anakalamba, anaika ana ace amuna akhale oweruza a Israyeli.
2
Dzina la mwana wace woyamba ndiye Yoeli, ndi dzina la waciwiri ndiye Abiya; ndiwo oweruza a ku Beereseba.
3
Ndipo ana ace sanatsanza makhalidwe ace, koma anapambukira ku cisiriro, nalandira cokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.
4
Pamenepo akuru onse a Israyeli anasonkhana, nadza kwa Samueli ku Rama;
5
nanena naye, Taonani, mwakalamba, ndipo ana anu satsanza makhalidwe anu; tsono, mutilongere mfumu kuti ikatiweruze, monga umo mucitidwa m'mitundu yonse ya anthu.
6
Koma cimeneci sicinakondweretsa Samueli, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samueli anapemphera kwa Yehova.
7
Ndipo Yehova ananena ndi Samueli, Umvere mau onse anthuwo alikulankhula nawe; popeza sindiwe anakukana, koma ndine anandikana, kuti ndisakhale mfumu yao.
8
Monga nchito zao zonse anazicita kuyambira tsiku lija ndinawaturutsa ku Aigupto, kufikira lero lino kuti anandisiya Ine, natumikira milungu yina, momwemo alikutero ndi iwenso.
9
Cifukwa cace tsono umvere mau ao koma uwacenjeze kolimba, ndi kuwadziwitsa makhalidwe ace a mfumu imene idzawaweruza.
10
Ndipo Samueli anauza anthu akumpempha iye mfumu mau onse a Yehova,
11
Nati, Awa ndi makhalidwe a mfumu imene idzaweruza inu; idzatenga ana anu amuna, akhale akusunga magareta, ndi akavale ace; ndipo adzathamanga ndi kutsogolera magareta ace;
12
idzawaika akhale otsogolera cikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yace, ndi kutema dzinthu zace, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magareta.
13
Ndipo idzatenga ana anu akazi apange zonunkhira, naphikire, naumbe mikate.
14
Ndipo idzalanda minda yanu, ndi minda yamphesa yanu, ndi minda yaazitona, inde minda yoposayo, nidzaipatsa anyamata ace.
15
Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yamphesa, nidzalipatsa akapitao ace, ndi anyamata ace.
16
Ndipo idzatenga akapolo anu, ndi adzakazi anu, ndi anyamata anu okongola koposa, ndi aburu anu, nidzawagwiritsa nchito yace.
17
Idzatenga limodzi la magawo khumi la zoweta zanu; ndipo inu mudzakhala akapoloace.
18
Ndipotsiku lija mudzapfuula cifukwa ca mfumu yanu munadzisankhira nokha; koma Yehova sadzayankha inu tsiku lijalo.
19
Koma anthu anakana kumvera mau a Samueli; nati, Iai, koma tifuna kukhala nayo mfumu yathu;
20
kuti ifenso tikafanane nao anthu a mitundu yonse; kuti mfumu yathuyo ikatiweruzire, ndi kuturuka kutitsogolera, ndi kuponya nafe nkhondo zathu.
21
Ndipo Samueli anamva mau onse a anthuwo, nawafotokozanso m'makutu a Yehova.
22
Ndipo Yehova anati kwa Samueli, Umvere mau ao, nuwalongere mfumu, Ndipo Samueli anati kwa amuna a Israyeli, Mupite, munthu yense ku mudziwace.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31