bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Samuel 24
1 Samuel 24
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 25 →
1
Ndipo kunali, pakubwerera Sauli potsata Afilisti, anamuuza, kuti, Taonani, Davide ali ku cipululu ca Engedi.
2
Tsono Sauli anatenga anthu zikwi zitatu osankhika pakati pa Aisrayeli onse, namuka kukafuna Davide ndi anthu ace m'matanthwe a zinkhoma.
3
Ndipo panjira anafika ku makola a nkhosa, kumene kunali phanga; ndipo Sauli analowa kuti akapfunde mapazi ace. Ndipo Davide ndi anyamata ace analikukhala m'kati mwa phangamo,
4
Ndipo anyamata a Davide ananena naye, Onani, lero ndilo tsiku limene Yehova anati kwa inu, Onani, Ine ndidzapereka mdani wako m'dzanja lako, kuti ukamcitira iye cokukomera. Ndipo Davide ananyamuka, nadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli mobisika.
5
Ndipo kunali m'tsogolo mwace kuti a mtima wa Davide unamtsutsa cifukwa adadula mkawo wa mwinjiro wa Sauli.
6
Nati kwa anyamata ace, Mulungu andiletse kucitira ici mbuye wanga, wodzozedwa wa Yehova, kumsamulira dzanja langa, popeza iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
7
Comweco Davide analetsa anyamata ace ndi mau awa, osawaloleza kuukira Sauli. Ndipo Sauli ananyamuka, naturuka m'phangamo, namuka njira yace.
8
Bwino lace Davide yemwe ananyamuka, naturuka m'phangamo, napfuulira Sauli, nati, Mbuye wanga, mfumu. Ndipo pakuceuka Sauli, Davide anaweramira nkhope yace pansi, namgwadira.
9
Davide nanena ndi Sauli, Bwanji mulikusamalira mau a anthu akuti, Onani, Davide afuna kukucitirani coipa.
10
Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, Sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; cifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.
11
Ndiponso atate wanga, penyani, inde penyani mkawo wa mwinjiro wanu m'dzanja langa; popeza ndinadula mkawo wa mwinjiro wanu, osakuphani, mudziwe, nimuone kuti mulibe coipa kapena kulakwa m'dzanja langa, ndipo sindinakucimwirani, cinkana inu musaka moyo wanga kuti muugwire,
12
Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu; ndipo Yehova adzandibwezera cilango kwa inu; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.
13
Monga umanena mwambi wa makolo, kuti, Ucimo uturukira mwa ocimwa; koma dzanja langa silidzakhala pa inu.
14
Nanga mfumu ya Israyeli inaturukira yani; inu mulikupitikitsa yani? Garu wakufa, kapena nsabwe.
15
Cifukwa cace Yehova akhale woweruza, naweruze pakati pa ine ndi inu, nayang'anire, oandigwirire moyo, oandipulumutse m'dzanja lanu.
16
Ndipo kunali, pakutsiriza Davide kulankhula mau awa kwa Sauli, Sauli anati, Ndiwo mau ako kodi, mwana wanga Davide? Sauli nakweza mau ace, nalira misozi.
17
Nati kwa Davide, Iwe ndiwe wolungama woposa ine; popeza unandibwezera zabwino, koma ine ndinakubwezera zoipa.
18
Ndipo unatsimikiza lero lino kuti wandicitira zabwino cifukwa sunandipha pamene Yehova anandipereka m'dzanja lako.
19
Pakuti munthu akapeza mdani wace, adzamleka kodi kuti acoke bwino? Cifukwa cace Yehova akubwezere zabwino pa ici unandicitira ine lero lomwe.
20
Ndipo tsono taona ndidziwa kuti udzakhala mfumu ndithu, ndi kuti ufumu wa Israyeli udzakhazikika m'dzanja lako.
21
Cifukwa cace tsono undilumbirire ndi Yehova, kuti sudzatha mbeu yanga nditamuka ine, ndi kuti sudzaononga dzina langa m'nyumba ya atate wanga.
22
Ndipo Davide analumbirira Sauli. Sauli namuka kwao; koma Davide ndi anthu ace anakwera kumka kungaka.
← Chapter 23
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 25 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31