bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Samuel 13
1 Samuel 13
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 14 →
1
Sauli anali ndi zaka makumi atatu pamene anayamba ufumu wace; nakhala mfumu ya Israyeli zaka ziwiri.
2
Pamenepo Sauli anadzisankhira anthu zikwi zitatu a Israyeli; zikwi ziwiri za iwowa zinali ndi Sauli ku Mikimasi, ndi ku phiri la ku Beteli; ndi cikwi cimodzi anali ndi Jonatani ku Gibeya wa ku Benjamini; ndipo anawauza anthu ena onse amuke ku mahema ao.
3
Ndipo Jonatani anathyola kaboma ka Afilisti lokhala ku Geba, ndipo Afilisti anamva za ici. Ndipo Sauli analiza lipenga m'dziko monse, nati, Amve Ahebri.
4
Ndipo Aisrayeli onse anamva kunena kuti Sauli anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisrayeli. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Sauli ku Giligala.
5
Ndipo Afilisti anasonkhana kuti akamenyane ndi Aisrayeli, anali nao magareta zikwi makumi atatu, ndi apakavalo zikwi zisanu ndi cimodzi, ndi anthu akucuruka monga mcenga wa pa dooko la nyanja. Iwowa anakwera namanga zithando ku Mikimasi kum'mawa kwa Betaveni.
6
Pamene anthu a Israyeli anazindikira kuti ali m'kupsinjika, pakuti anthuwo anasauka mtima, anthuwo anabisala m'mapanga, ndi m'nkhalango, ndi m'matanthwe, ndi m'malinga, ndi m'maenje.
7
Ndipo Ahebri ena anaoloka Yordano nafika ku dziko la Gadi ndi Gileadi; koma Sauli akali ku Giligala, ndipo anthu onse anamtsata ndi kunthunthumira.
8
Ndipo iye anatsotsa masiku asanu ndi awiri, monga nthawi anampanga Samueli; koma Samueli sanafika ku Giligala, ndipo anthu anabalalika namsiya Sauli.
9
Pamenepo Sauli anati, Andipatsire kuno nsembe yopsereza, ndi nsembe zoyamika. Ndipo iye anapereka nsembe yopserezayo.
10
Ndipo kunali kuti pakutsiriza iye kupereka nsembe yopserezayo, pomwepo, onani, Samueli anafika. Ndipo Sauli anamcingamira kukamlankhula iye.
11
Ndipo Samueli anati, Mwacitanji? Nati Sauli, Cifukwa ndinaona kuti anthuwo alinkubalalika kundisiya ine, ndi kuti inu simunafika masiku aja tinapangana, ndi kuti Afilisti anasonkhana ku Mikimasi;
12
cifukwa cace ndinati, Afilisti adzatitsikira pane pa Giligala, ndisanapembedze Yehova; potero ndinadzifulumiza, ndi kupereka nsembe yopsereza.
13
Ndipo Samueli ananena ndi Sauli, Munacita kopusa; simunasunga lamulo la Yehova Mulungu wanu, limene iye anakulamulirani; mwenzi Yehova atakhazikitsa nthawi yino ufumu wanu, ukhale pa Israyeli nthawi yosatha.
14
Koma tsopano ufumu wanu sudzakhala cikhalire; Yehova wadzifunira munthu wa pamtima pace; ndipo Yehova wamuika iye akhale mtsogoleri wa anthu ace, cifukwa inu simunasunga cimene Yehova anakulamulirani.
15
Ndipo Samueli anauka nacoka ku Giligala kunka ku Gibeya wa ku Benjamini. Ndipo Sauli anawerenga anthu amene anali naye, monga mazana asanu ndi limodzi.
16
Ndipo Sauli, ndi Jonatani mwana wace, ndi anthu akukhala nao anakhala ku Geba wa ku Benjamini; koma Afilistiwo anali nazo zithando zao ku Mikimasi.
17
Ndipo owawanya anaturuka ku zithando za Afilisti magulu atatu; gulu limodzi linalowa njira yonka ku Ofra, ku dera la Sauli;
18
gulu lina linalowa njira yonka ku Betihoroni; ndi gulu linanso linalowa ku njira ya kumalire, akuyang'ana ku cigwa ca Zeboimu kucipululuko.
19
Ndipo m'dziko lonse la Israyeli simunapezeka wosula; popeza Afilisti adati, Kuti Aisrayeli angadzisulire malupanga kapena mikondo;
20
koma Aisrayeli onse adafotsikira kwa Afilisti, kuti awasaniire munthu yense cikhasu cace, colimira cace, nkhwangwa yace, ndi khasu lace;
21
koma analf nao matupa kukonza makasu, ndi zikhasu ndi makasu a mana ndi nkhwangwazo; ndi kusongola zothwikira.
22
Comweco kunali kuti tsiku lankhondolo sunapezeka mkondo kapena lupanga m'manja a anthu onse anali ndi Sauli ndi Jonatani; koma Sauli yekha ndi Jonatani mwana wace anali nazo.
23
Ndipo a ku kaboma ka Afilisti anaturuka kunka ku mpata wa ku Mikimasi.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31