bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Samuel 7
1 Samuel 7
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
1
Ndipo anthu a ku Kiriati-yearimu anabwera, natenga likasa la Yehova, nafika nalo m'nyumba ya Abinadabu paphiri; napatula mwana wace wamwamuna Eleazeri kuti asunge likasa la Yehova.
2
Ndipo kunali, kuti likasalo linakhala nthawi yaikuru m'Kiriati-yearimu; popeza linakhalako zaka makumi awiri; ndipo banja lonse la Israyeli linalirira Yehova.
3
Ndipo Samueli analankhula ndi banja lonse la Israyeli nati, Ngati mukuti mubwerere kunka kwa Yehova ndi mitima yanu yonse, cotsani pakati pa inu milungu yacilendo, ndi Asitaroti, nimukonzere Yehova mitima yanu, ndi kumtumikira iye yekha; mukatero, iye adzakupulumutsani m'manja a Afilisti.
4
Pomwepo ana a Israyeli anacotsa. Abaala ndi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.
5
Ndipo Samueli anati, Musonkhanitse Aisrayeli onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.
6
Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala cakudya tsiku lija, nati, Tinacimwira Yehova. Ndipo Samueli anaweruza ana a Israyeli m'Mizipa.
7
Ndipo pamene Afilisti anamva kuti Aisrayeli anasonkhana pamodzi ku Mizipa, mafumu a Afilisti anakwera kukayambana ndi Aisrayeli. Ndipo Aisrayeli pakumva ici, anacita mantha ndi Afilistiwo.
8
Ndipo ana a Israyeli anati kwa Samueli, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.
9
Ndipo Samueli anatenga mwana wa nkhosa woyamwa, nampereka wathunthu kwa Yehova, nsembe yopsereza; ndipo Samueli anapempherera Israyeli kwa Yehova; ndipo Yehova anambvomereza.
10
Ndipo pamene Samueli analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisrayeli; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukuru pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisrayeli.
11
Ndipo Aisrayeli anaturuka ku Mizipa, nathamangira Afilisti, nawakantha mpaka anafika pansi pa Betikara.
12
Pamenepo Samueli anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Seni, naucha dzina lace. Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehovaanatithandiza.
13
Comweco anagonjetsa Afilisti, ndino iwo sanatumphanso malire a Israyeli ndipo dzanja la Yehova linasautsa Afilisti masiku onse a Samueli.
14
Ndipo midzi ya Israyeli imene Afilisti adailanda kale inabwezedwa kwa Aisrayeli, kuyambira ku Ekroni kufikira ku Gati; ndi Aisrayeli analanditsa miraga yao m'manja a Afilisti. Ndipo pakati pa Aisrayeli ndi Aamori panali mtendere;
15
ndipo Samueli anaweruza Israyeli masiku onse a moyo wace.
16
Ndipo anayenda cozungulira caka ndi caka ku Beteli, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israyeli m'malo onse amenewa.
17
Ndipo anabwera ku Rama, pakuti nyumba yace inali kumeneko; ndipo pamenepo anaweruza Israyeli; namangapo guwa la nsembe la Yehova.
← Chapter 6
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 8 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31