bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
1 Samuel 27
1 Samuel 27
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 28 →
1
Ndipo Davide ananena mumtima mwace, Tsiku tina Sauli adzandipha; palibe cina condikomera koma kuti ndithawire ku dziko la Afilisti; ndipo Sauli adzakhala kakasi cifukwa ca ine, osandifunanso m'malire onse a Israyeli, momwemo ndidzapulumuka m'dzanja lace.
2
Ndipo Davide ananyamuka, naoloka pamodzi ndi anthu mazana asanu ndi limodzi amene anali naye, nafika kwa Akisi mwana wa Maoki, mfumu ya ku Gati.
3
Ndipo Davide anakhala ndi Akisi ku Gati, iye ndi anthu ace, munthu yense ndi a pabanja pace, inde Davide ndi akazi ace awiri, Ahinoamu wa ku Jezreeli, ndi Abigayeli wa ku Karimeli, mkazi wa Nabala.
4
Ndipo anauza Sauli kuti Davide anathawira ku Gati; ndipo iye sanamfunanso.
5
Ndipo Davide anati kwa Akisi, Ngati mwandikomera mtima, andipatse malo kumudzi kwina kumiraga, kuti ndikakhale kumeneko; pakuti mnyamata wanu adzakhala bwanji m'mudzi wacifumu pamodzi ndi inu?
6
Ndipo Akisi anampatsa Zikilaga tsiku lomweli; cifukwa cace Zikilaga ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.
7
Ndipo kuwerenga kwace kwa masiku Davide anakhala ku dziko la Afilisti ndiko caka cimodzi ndi miyezi inai.
8
Ndipo Davide ndi anthu ace anakwera, nathira nkhondo yobvumbulukira pa Agesuri, ndi Agirezi, ndi Aamaleki; pakuti awa ndiwo anthu akale a m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Aigupto.
9
Ndipo Davide anapasula dzikolo, sanasunga ndi moyo mwamuna kapena wamkazi; natenga nkhosa, ndi ng'ombe, ndi aburu, ndi ngamila, ndi zobvala; nabwera nafika kwa Akisi.
10
Ndipo Akisi anati, Wapooyana nkhondo ndi yani lero? Nati Davide, Ndi a kumwera kwa Ayuda, ndi a kumwera kwa Ayerameli, ndi a kumwera kwa Akeni.
11
Ndipo Davide sadasunga wamoyo mwamuna kapena mkazi, kubwera nao ku Gati; popeza adati, Kuti angatiulule, ndi kuti, Davide anatero, ndi makhalidwe ace ndi otere, masiku onse akukhala ku dziko la Afilisti.
12
Ndipo Akisi anakhulupirira Davide, nati Anadziipitsa ndithu pakati pa anthu a Israyeli, cifukwa cace iye adzakhala mnyamata wanga cikhalire.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31