bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Deuteronomy 14
Deuteronomy 14
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 15 →
1
Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadziceka, kapena kumeta tsitsi pakati pa maso cifukwa ca akufa.
2
Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope pa dziko lapansi.
3
Musamadya conyansa ciri conse,
4
Nyamazi muyenera kumadya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, ndi mbuzi,
5
ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale.
6
Ndipo nyama iri yonse yogawanika ciboda, nikhala yogawanikadi ciboda, nibzikula, imeneyo muyenera kudya.
7
Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika ciboda: ngamila, ndi ka'ulu, ndi mbira, popezazibzikula, komazosagawanika ciboda, muziyese zodetsa;
8
ndi nkhumba, popeza igawanika ciboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.
9
Mwa zonse ziri m'madzi muyenera kumadya izi: ziri zonse ziri nazo zipsepse ndi mamba, zimenezi muyenera kumadya;
10
koma ziri zonse zopanda zipsepse kapena mamba musamadya; muziyese zonyansa.
11
Mbalame zosadetsazonse muyenera kumadya.
12
Koma izi ndi zimene simuyenera kumadya: mphungu, ndi nkhwazi, ndi cikambi,
13
ndi kamtema, ndi mphamba, ndi muimba monga mwa mtundu wace;
14
ndi khungubwe ali yense monga mwa mtundu wace;
15
ndi nthiwatiwa, ndi cipudo, ndi kakoa, ndi kabawi monga mwa mtundu wace;
16
ndi nkhutukutu, ndi mancici, ndi tsekwe;
17
ndi bvuwo, ndi dembu, ndi nswankhono;
18
ndi iodwa, ndi cimeza, monga mwa mtundu wace, ndi sadzu, ndi mleme.
19
Ndipo zokwawa zonse zakuuluka muziyesa zonyansa; musamazidya.
20
Mbalame zonse zosadetsa muyenera kumadya.
21
Musamadya cinthu ciri conse citafa cokha; muzipereka ico kwa mlendo ali m'mudzi mwanu, acidye ndiye; kapena ucigulitse kwa mlendo; popeza ndinu mtundu wa anthu wopatulika wa Yehova Mulungu wanu. Musamaphika mwana wa mbuzi mu mkaka wa mace.
22
Muzipereka ndithu limodzi la magawo khumi la zipatso zonse za mbeu zanu, zofuma kumunda, caka ndi caka.
23
Ndipo muzidye pamaso pa Yehova Mulungu wanu, m'malo m'mene asankhamo iye, kukhalitsamo dzina lace; limodzi la magawo khumi la tirigu wanu, la vinyo wanu, ndi la mafuta anu, ndi oyamba kubadwa a ng'ombe zanu ndi a nkhosa ndi mbuzi zanu; kuti muphunzire kuopa Yehova Mulungu wanu masiku onse.
24
Ndipo ikakutalikirani njira kotero kuti simukhoza kulinyamula, popeza malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha, kuikapo dzina lace, akutanimphirani; atakudalitsani Yehova Mulungu wanu;
25
pamenepo mulisinthe ndarama, ndi kumanga ndarama ikhale m'dzanja mwanu, ndi kupita ku malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha;
26
ndipo mugule ndi ndaramazo ciri conse moyo wanu ukhumba, ng'ombe kapena nkhosa, kapena vinyo, kapena cakumwa colimba, kapena ciri conse moyo wanu ukufunsani; nimudye pomwepo pamaso pa Yehova Mulungu wanu, ndi kukondwera, inu ndi a pabanja panu.
27
Koma Mlevi wokhala m'mudzi mwanu, musamamtaya, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu.
28
Pakutha pace pa zaka zitatu muziturutsa magawo onse a magawo khumi a zipatso zanu za caka ico, ndi kuwalinditsa m'mudzi mwanu;
29
ndipo abwere Mlevi, popeza alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi inu, ndi mlendo, ndi ana amasiye, ndi mkazi wamasiye, okhala m'mudzi mwanu, nadye nakhute; kuti Yehova Mulungu wanu akakudalitseni mu nchito zonse za dzanja lanu muzicitazi.
← Chapter 13
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 15 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34