bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Deuteronomy 8
Deuteronomy 8
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 9 →
1
Muzisamalira kucita malamulo onse amene ndikuuzani lero lino, kuti mukhale ndi moyo, ndi kucuruka, ndi kulowa, ndi kulandira dziko limene Yehova analumbirira makolo anu.
2
Ndipo mukumbukile njira yonse imene Yehova Mulungu wanu anakuyendetsani m'cipululu zaka izi makumi anai, kuti akucepetseni, kukuyesani, kudziwa cokhala mumtima mwanu, ngati mudzasunga malamulo ace, kapena iai.
3
Ndipo anakucepetsani, nakumvetsani odala, nakudyetsani ndi mana, amene simunawadziwa, angakhale makolo anu sanawadziwa; kuti akudziwitseni kuti munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakuturuka m'kamwa mwa Yehova.
4
Zobvala zanu sizinatha pathupi panu, phazi lanu silinatupa zaka izi makumi anai.
5
Ndipo muzindikire m'mtima mwanu, kuti monga munthu alanga mwana wace, momwemo Yehova Mulungu wanu akulangani inu.
6
Ndipo muzisunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, kuyenda m'njira zace, ndi kumuopa.
7
Pakuti Yehova Mulungu wanu akulowetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje yamadzi, la akasupe, ndi la maiwe akuturuka m'zigwa, ndi m'mapiri;
8
dziko la tirigu ndi barele, ndi mipesa, ndi mikuyu, ndi makangaza; dziko la azitona a mafuta, ndi uci;
9
dziko loti mudzadyamo mkate wosapereweza; simudzasowamo kanthu; dziko loti miyala yace nja citsulo, ndi m'mapiri ace mukumbe mkuwa.
10
Ndipo mudzadya ndi kukhuta, ndi kuyamika Yehova Mulungu wanu cifukwa ca dziko lokomali anakupatsani.
11
Cenjerani mungaiwale Yehova Mulungu wanu, ndi kusasunga malamulo ace, ndi maweruzo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino;
12
kuti, mutadya ndi kukhuta, ndi kumanga nyumba zokoma, ndi kukhalamo;
13
ndipo zitacuruka ng'ombe zanu, ndi nkhosa zanu, zitacurukanso siliva wanu ndi golidi wanu, zitacurukanso zonse muli nazo;
14
mtima wanu ungatukumuke, nimungaiwale Yehova Mulungu wanu, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo;
15
amene anakutsogolerani m'cipululu cacikuru ndi coopsaco, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi; amene anakuturutsirani madzi m'thanthwe lansangalabwi;
16
amene anakudyetsani m'cipululu ndi mana, amene makolo anu sanawadziwa; kuti akucepetseni, ndi kuti akuyeseni, kuti akucitireni cokoma potsiriza panu;
17
ndipo munganene m'mtima mwanu, Mphamvu yanga ndi mkono wanga wolimba zinandifunira cuma ici.
18
Koma mukumbukile Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera cuma; kuti akhazikitse cipangano cace cimene analumbirira makolo anu, monga cikhala lero lino.
19
Ndipo kudzakhala kuti mukaiwalatu Yehova Mulungu wanu, ndi kutsata milungu yina ndi kuitumikira, ndikucitirani mboni lero lino kuti mudzaonongeka ndithu.
20
Monga amitundu amene Yehova awaononga pamaso panu, momwemo mudzaonongeka; cifukwa ca kusamvera mau a Yehova Mulungu wanu.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34