bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Deuteronomy 27
Deuteronomy 27
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 28 →
1
Ndipo Mose ndi akuru a Israyeli anauza anthu, nati, Sungani malamulo onse ndikuuzani lero.
2
Ndipo kudzali, tsiku lakuoloka inu Yordano kulowa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, kuti mudziutsire miyala yaikuru, ndi kuimata ndi njeresa;
3
ndipo mulemberepo mau onse a cilamulo ici, mutaoloka; kuti mulowe m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu.
4
Ndipo kudzali, mutaoloka Yordano, muutse miyala iyi ndikuuzani lero, m'phiri la Ebala, ndi kuimata ndi njeresa.
5
Ndipo komweko mumangire Yehova Mulungu wanu guwa la nsembe, guwa la nsembe lamiyala; musakwezepo cipangizo cacitsulo.
6
Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu;
7
ndi kuphera nsembe zoyamika, ndi kudyapo, ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.
8
Ndipo mulembere pa miyalayi mau onse a cilamulo ici mopenyeka bwino.
9
Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israyeli wonse, ndi kuti, Khalani cete, imvanitu, Israyeli; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu.
10
Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kucita malamulo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino.
11
Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti,
12
Aimirire awa pa phiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordano: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.
13
Naimirire awa pa phiri la Ebala, kutemberera: Rubeni, Gadi, ndi Aseri, ndi Zebuloni, Dani, ndi Nafitali.
14
Ndipo ayankhe Alevi ndi kunena kwa amuna onse a Israyeli, ndi mau omveka.
15
Wotembereredwa munthu wakupanga fano losema kapena loyenga, lonyansidwa nalo Yehova, nchito ya manja a mmisiri, ndi kuliika m'malo a m'tseri. Ndipo anthu onse: ayankhe ndi kuti, Amen.
16
Wotembereredwa iye wakupeputsa atate wace kapena mai wace. Ndi anthu onse anene, Amen.
17
Wotembereredwa iye wakusendeza malire a mnansi wace. Ndi anthu onse anene, Amen.
18
Wotembereredwa wakusokeretsa wakhungu m'njira, Ndi anthu onse anene, Amen.
19
Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.
20
Wotembereredwa iye wakugona ndi mkazi wa atate wace; popeza wabvula atate wace. Ndi anthu onse anene, Amen.
21
Wotembereredwa iye wakugona ndi nyama iri yonse. Ndi anthu onse anene, Amen.
22
Wotembereredwa iye wakugona ndi mlongo wace, mwana wamkazi wa atate wace, kapena mwana wamkazi wa mace. Ndi anthu onae anene, Amen.
23
Wotembereredwa iye wakugona ndi mpongozi wace. Ndi anthu onse anene, Amen.
24
Wotembereredwa iye wakukantha mnansi wace m'tseri. Ndi anthu onse anene, Amen.
25
Wotembereredwa iye wakulandira camwazi cakuti akanthe munthu wosacimwa. Ndi anthu onse anene, Amen.
26
Wotembereredwa iye wosabvomereza mau a cilamulo ici kuwacita. Ndi anthu onse anene, Amen.
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34