bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Deuteronomy 6
Deuteronomy 6
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 7 →
1
Ndipo awa ndi malamulo, malemba, ndi maweruzo, amene Yehova Mulungu wanu analamulira kukuphunzitsani, kuti muziwacita m'dziko limene muolokerako kulilandira;
2
kuti muope Yehova Mulungu wanu, kusunga malemba ace onse ndi malamulo ace, amene ndikuuzani inu ndi ana anu, ndi zidzukulu zanu, masiku onse a moyo wanu, ndi kuti masiku anu acuruke.
3
Potero imvani, Israyeli, musamalire kuwacita, kuti cikukomereni ndi kuti mucuruke cicurukire, monga Yehova Mulungu wa makolo anu anena ndi inu, m'dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.
4
Imvani, Israyeli; Yehova Mulungu wathu, Yehova ndiye mmodzi;
5
ndipo muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.
6
Ndipo mau awa ndikuuzanilero, azikhala pamtima panu;
7
ndipo muziwaphunzitsa mwacangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m'nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.
8
Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati cizindikilo, ndipo akhale ngati capamphumi pakati pa maso anu.
9
Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pa zipata zanu.
10
Ndipo kudzakhala, Yehova Mulungu wanu atakulowetsani m'dziko limene analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo, kuti adzakupatsani ili; midzi yaikuru ndi yokoma, imene simunaimanga;
11
ndi nyumba zodzala nazo zokoma ziri zonse, zimene simunazidzaza, ndi zitsime zosema, zimene simunazisema, minda yampesa, ndi minda yaazitona, zimene simunazioka, ndipo mutakadya ndi kukhuta;
12
pamenepo mudzicenjere mungaiwale Yehova, amene anakuturutsani m'dziko la Aigupto, m'nyumba ya akapolo,
13
Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzichula dzina lace.
14
Musamatsata milungu yina, milungu yina ya mitundu ya anthu akuzinga inu;
15
pakuti Yehova Mulungu wanu ali pakati panu, ndiye Mulungu wansanje; kuti ungapse mtima wa Yehova Mulungu wanu, ndi kukuonongani, kukucotsani pankhope pa dziko lapansi.
16
Musamayesa Yehova Mulungu wanu, monga munamyesa m'Masa.
17
Muzisunga mwacangu malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi mboni zace, ndi malemba ace, amene anakulamulirani.
18
Ndipo muzicita zolunjika ndi zokoma pamaso pa Yehova; kuti cikukomereni, ndi kuti mulowe kukalandira dziko lokomali Yehova analumbirira makolo anu,
19
kuingitsa adani anu onse pamaso panu, monga Yehova adanena.
20
Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani?
21
Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao m'Aigupto; ndipo Yehova anatiturutsa m'Aigupto ndi dzanja lamphamvu.
22
Ndipo Yehova anapatsa zizindikilo ndi zozizwa zazikuru ndi zowawa m'Aigupto, pa Farao, ndi pa nyumba yace yonse, pamaso pathu;
23
ndipo anatiturutsa komweko, kuti atilowetse, kutipatsa dzikoli analumbirira makolo athu.
24
Ndipo Yehova anatilamulira tizicita malemba awa onse, kuopa Yehova Mulungu wathu, kuti tipindule nako masiku onse, kuti atisunge amoyo, monga lero lino.
25
Ndipo kudzakhala kwa ife cilungamo, ngati tisamalira kucita malamulo awa onse pamaso pa Yehova Mulungu wathu, monga anatilamuliraife.
← Chapter 5
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 7 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34