bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Deuteronomy 25
Deuteronomy 25
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 26 →
1
Pakakhala ndeu pakati pa anthu, nakapita kukaweruzidwa iwowa, nakaweruza mlandu wao oweruza; azimasula wolungama, namange woipa.
2
Ndipo kudzali, wocita coipa akayenera amkwapule, woweruza amgonetse kuti amkwapule pamaso pace, amwerengere zofikira coipa cace.
3
Amkwapule kufikira makumi anai, asaonjezepo; pakuti, akaonjezapo ndi kumkwapula mikwapulo yambiri, angapeputse mbale wanu pamaso panu.
4
Musamapunamiza ng'ombe popuntha tirigu.
5
Abale akakhala pamodzi, nafa wina wa iwowa, wopanda mwana wamwamuna, mkazi wa wafayo asakwatibwe ndi mlendo wakunja; mbale wa mwamuna wace alowane naye, namtenge akhale mkazi wace, namcitire zoyenera mbale wa mwamuna wace.
6
Ndipo kudzali, kuti woyamba kubadwa amene adzambala, adzalowa dzina lace la mbale wace wafayo, kuti dzina lace lisafafanizidwe m'Israyeli.
7
Ndipo ngati mwamunayo safuna kutenga mkazi wa mbale wace, mkazi wa mbale waceyo azikwera kumka kucipata, kwa akuru, ndi kuti, Mbale wa mwamuna wanga akana kuutsira mbale wace dzina m'Israyeli; safuna kundicitira ine zoyenera mbale wa mwamuna.
8
Pamenepo akuru a mudzi wace amuitane, ndi kulankhula naye; ndipo akaimirira ndi kuti, Sindifuna kumtenga;
9
pamenepo mkazi wa mbale wace azimyandikiza pamaso pa akuru, nacotse nsapato yace ku ph zi la mwamunayo, ndi kumthira malobvu pankhope pace, ndi kumyankha ndi kuti, Atere naye mwamuna wosamanga nyumba ya mbale wace.
10
Ndipo azimucha dzina lace m'Israyeli, Nyumba ya uje anamcotsa nsapato.
11
Akalimbana wina ndi mnzace, nakayandikiza mkazi wa winayo kulanditsa mwamuna wace m'dzanja la wompandayo, nakaturutsa dzanja lace, ndi kumgwira kudzibvalo;
12
pamenepo muzidula dzanja lace; diso lanu lisamcitire cifundo.
13
Musamakhala nayo m'thumba mwanu miyala ya miyeso iwiri, waukuru ndi waung'ono.
14
Musamakhala nayo m'nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukuru ndi waung'ono.
15
Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu acuruke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
16
Pakuti onse akucita zinthu izi, onse akucita cisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.
17
Kumbukilani cocitira inu Amaleki panjira, poturuka inu m'Aigupto;
18
kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofok a akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaopa Mulungu,
19
Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu canu, kuti muzifafaniza cikumbutso ca Amaleki pansi pa thambo; musamaiwala.
← Chapter 24
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 26 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34