bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Deuteronomy 18
Deuteronomy 18
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 19 →
1
Ansembe Alevi, pfuko lonse la Levi, alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi Israyeli; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi colowa cace,
2
Alibe colowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wace ndiye colowa cao, monga ananena nao.
3
Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chipfu.
4
Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.
5
Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mapfuko anu onse, aimirire natumikire m'dzina la Yehova, iwo ndi ana ao amuna kosalekeza.
6
Ndipo Mlevi akacokera ku mudzi wanu wina m'Israyeli monse, kumene akhalako, nakadza ndi cifuniro conse ca moyo wace ku malo amene Yehova adzasankha;
7
pamenepo azitumikira m'dzina la Yehova Mulungu wace, monga amacita abale ace onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova.
8
Cakudya cao cizifanana, osawerengapo zolowa zace zogulitsa.
9
Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kucita mongamwa zonyansa za amitundu aja.
10
Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wace wamwamuna kapena mwana wace wamkazi ku mota wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.
11
Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.
12
Popeza ali yense wakucita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo cifukwa ca zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu.
13
Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.
14
Pakuti amitundu awa amene mudzawalandira, amamvera iwo akuyesa mitambo, ndi a ula; koma inu, Yehova Mulungu wanu sakulolani kucita cotero.
15
Yehova Mulungu wanu adzakuukitsirani mneneri wa pakati panu, wa abale anu, wonga ine; muzimvera iye;
16
monga mwa zonse munafunsa Yehova Mulungu wanu m'Horebe, tsiku lakusonkhana lija, ndi kuti, Tisamvenso mau a Yehova Mulungu wathu, ndipo tisaonenso mota waukuru uwu, kuti tingafe.
17
Ndipo Yehova anati kwa ine, Cokoma ananenaci.
18
Ndidzawaukitsira mneneri wa pakati pa abale ao, wonga iwe; ndipo ndidzampatsa mau anga m'kamwa mwace, ndipo adzanena nao zonse ndimuuzazi.
19
Ndipo kudzakhala kuti munthu wosamvera mau anga amene amanena m'dzina langa, ndidzamfunsa.
20
Koma mneneri wakucita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulira anene, kapena kunena m'dzina la milungu yina, mneneri ameneyo afe.
21
Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananena?
22
Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sacitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanena; mneneriyo ananena modzikuza, musamuopa iye.
← Chapter 17
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 19 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34