bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Hosea 1
Hosea 1
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 2 →
1
MAU a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobiamu mwana wa Yoasi mfumu ya Israyeli.
2
Ciyambi ca kunena kwa Yehova mwa Hoseya, Ndipo Yehova anati kwa Hoseya, Muka, udzitengere mkazi wacigololo ndi ana acigololo; pakuti dziko latsata cigololo cokha cokha kuleka kutsata Yehova.
3
Ndipo anamuka natenga Gomeri mwana wamkazi wa Diblaimu; iye naima, nambalira mwana wamwamuna.
4
Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Yezreeli; pakuti katsala kanthawi, ndipo ndidzabwezera cilango mwazi wa Yezreeli pa nyumba ya Yehu, ndi kuleketsa ufumu wa nyumba ya Israyeli.
5
Ndipo kudzacitika tsiku lomwelo, ndidzatyola uta wa Israyeli m'cigwa ca Yezreeli.
6
Ndipo anaimanso, nabala mwana wamkazi. Ndipo Yehova anati kwa iye, Umuche dzina lace Wosacitidwacifundo; pakuti sindidzacitiranso cifundo nyumba ya Israyeli, kuti ndiwakhululukire konse.
7
Koma ndidzacitira cifundo nyumba ya Yuda, ndi kuwapulumutsa mwa Ine Yehova Mulungu wao, osawapulumutsa ndi uta, kapena lupanga, kapena nkhondo ndi akavalo, kapena apakavalo.
8
Ataleka tsono kuyamwitsa Wosacitidwa cifundo, anaima, nabala mwana wamwamuna.
9
Ndipo Yehova anati, Umuche dzina lace Si-anthuanga; pakuti inu sindinu anthu anga, ndipo Ine sindine wanu.
10
Angakhale anatero, kuwerenga kwace kwa ana a Israyeli kudzanga mcenga wa kunyanja, wosayeseka kapena kuwerengeka; ndipo kudzatero kuti m'mene adawanena, Simuli anthu anga, adzanena nao, Muli ana a Mulungu wamoyo.
11
Ndipo ana a Yuda ndi ana a Israyeli adzasonkhanidwa pamodzi, nadzadziikira mkuru mmodzi, nadzakwera kucoka m'dziko; pakuti tsiku la Yezreeli ndi lalikuru.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14