bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Hosea 11
Hosea 11
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 12 →
1
Pamene Israyeli anali mwana, ndinamkonda, ndinaitana mwana wanga ali m'Aigupto.
2
Monga anawaitana, momwemo anawacokera; anaphera nsembe Abaala, nafukizira mafano osema.
3
Koma Ine ndinaphunzitsa Efraimu kuyenda, ndinawafungata m'manja mwanga; koma sanadziwa kuti ndinawaciritsa.
4
Ndinawakoka ndi zingwe za munthu, ndi zomangira za cikondi; ndinakhala nao ngati iwo akukweza goli pampuno pao, ndipo ndinawaikira cakudya.
5
Iye sadzabwerera kumka ku dziko la Aigupto, koma Asuri adzakhala mfumu yace, popeza anakana kubwera.
6
Ndi lupanga lidzagwera midzi yace, lidzatha mipiringidzo yace, ndi kuononga cifukwa ca uphungu wao.
7
Ndipo anthu anga alimbika kubwerera m'mbuyo kundileka Ine; cinkana akawaitana atsate Iye ali m'mwamba, sadzakweza ndi mmodzi yense.
8
Ndidzakusiya bwanji, Efraimu? ndidzakupereka bwanji, Israyeli? ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zacifundo zanga zilira zonse pamodzi.
9
Sindidzacita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efraimu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mudzi.
10
Adzatsata Yehova, Iye adzabangula ngati mkango; pamene abangula, ana adzafika ndi kunjenjemera kucokera kumadzulo.
11
Adzafika ndi kunjenjemera ngati mbalame ya ku Aigupto, ndi ngati nkhunda m'dziko la Asuri; ndipo ndidzawakhalitsa m'nyumba zao, ati Yehova.
12
Efraimu andizinga ndi bodza, ndi nyumba ya Israyeli ndi cinyengo, ndi Yuda apikisana ndi Mulungu, ndiye Woyera wokhulupirika.
← Chapter 10
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 12 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14