bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Hosea 9
Hosea 9
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
1
Usakondwera, Israyeli, ndi kusekerera, ngati mitundu ya anthu; pakuti wacita cigololo kuleka Mulungu wako, wakonda mphotho ya cigololo pa dwale la tirigu liri lonse.
2
Dwale ndi coponderamo mphesa sizidzawadyetsa, vinyo watsopano adzamsowa.
3
Sadzakhala m'dziko la Yehova; koma Efraimu adza bwerera kumka ku Aigupto; ndipo adzadya cakudya codetsa m'Asuri.
4
Sadzatsanulira Yehova nsembe zavinyo; sizidzamkomera Iye nsembe zao; zidzakhala kwa iwo ngati mkate wa acisoni; onse akudyako adzadetsedwa; pakuti mkate wao udzakhala wa njala yao, uwu sudzalowa m'nyumbaya Yehova.
5
Mudzacitanji tsiku la masonkhano oikika, ndi tsiku la madyerero a Yehova?
6
Pakuti taonani, anacokera cionongeko, koma Aigupto adzawasonkhanitsa, Mofi adzawaika m'manda; khwisa adzalanda zofunika zao zasiliva; minga idzakhala m'mahema mwao.
7
Masiku a kulanga afika, masiku a kubwezera afika; Israyeli adzadziwa; mneneri ali wopusa, munthu wamzimu ali wamisala, cifukwa ca kucuruka mphulupulu yako, ndi popeza udani ndi waukuru.
8
Efraimu ndiye wozonda kwa Mulungu wanga; kunena za mneneri, msampha wa msodzi uli m'njira zace zonse, ndi udani m'nyumba ya Mulungu wace.
9
Anadzibvunditsa kwambiri, monga masiku a Gibeya; adzakumbukila mphulupulu yao, adzalanga zocimwa zao.
10
Ndinapeza Israyeli ngati mphesa m'cipululu, ndinaona makolo anu ngati cipatso coyamba ca mkuyu nyengo yace yoyamba; koma anadza kwa Baala Peori, nadzipatulira conyansaco, nasandulika onyansa, conga cija anacikonda.
11
Kunena za Efraimu, ulemerero wao udzauluka ndi kucoka ngati mbalame; sipadzakhala kubala, ndi kukhala ndi pakati, ndi kuima.
12
Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwacokera.
13
Efraimu, monga ndaona, akunga Turo, wookedwa pokoma; koma Efraimu adzaturutsira ana ace wakuwaphera.
14
Apatseni, Yehova; mudzapatsa ciani? muwapatse mimba yotayataya, ndi mawere ouma.
15
Coipa cao conse ciri m'Giligala; pakutipamenepo ndinawada, cifukwa ca kuipa kwa macitidwe ao ndidzawainga kuwacotsa m'nyumba mwanga; sindidzawakondanso; akalonga ao onse ndiwo opanduka.
16
Efraimu wakanthidwa, muzu wao wauma, iwo sadzabala zipatso; inde ngakhale abala, koma ndidzapha zipatso zofunika za mimba yao.
17
Mulungu wanga adzawataya, pakuti sanammvera Iye; ndipo adzakhala othawathawa mwa amitundu.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14