bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Hosea 10
Hosea 10
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 11 →
1
Israyeli ndi mpesa wotambalala, wodzibalira wokha zipatso; monga umo zinacurukira zipatso zace, momwemo anacurukitsa maguwa a nsembe ace; monga mwa kukoma kwace kwa dziko lace anapanga zoimiritsa zokoma.
2
Mtima wao wagawikana, tsopano adzapezeka oparamula, adzapasula maguwa ao a nsembe, nadzaononga zoimiritsa zao.
3
Pakuti tsopano adzati, Tiribe mfumu, popeza sitiopa Yehova; ndi mfumu idzaticitira ciani?
4
Anena mau akulumbira monama, pakucita mapangano momwemo; ciweruzo ciphuka ngati zitsamba zowawa m'micera ya munda.
5
Okhala m'Samariya adzaopera cifanizo ca ana a ng'ombe a ku Betaveni; pakuti anthu ace adzamva naco cisoni, ndi ansembe ace amene anakondwera naco, cifukwa ca ulemerero wace, popeza unacicokera.
6
Adzacitengeranso ku Asuri cikhale mphatso ya kwa mfumu Yarebu; Efraimu adzatenga manyazi, ndi Israyeli adzacita manyazi ndi uphungu wace.
7
Ndipo Samariya, mfumu yace yamwelera ngati thobvu pamadzi.
8
Ndipo misanje ya Aveni, ndiyo cimo la Israyeli, idzaonongeka; minga ndi mitungwi idzamera pa maguwa ao a nsembe; ndipo adzati kwa mapiri, Tiphimbeni; ndi kwa zitunda, Tigwereni.
9
Israyeli, wacimwa kuyambira masiku a Gibeya; pomwepo anaimabe; nkhondo ya pa ana a cosalungama siinawapeza ku Gibeya.
10
Pamene ndifuna ndidzawalanga, ndi mitundu ya anthu idzawasonkhanira pomangidwa iwo pa zolakwa zao ziwiri.
11
Ndipo Efraimu ndiye ng'ombe yaikazi yaing'ono, yozereweredwa, yokonda kupuntha tirigu; koma ndapita pa khosi lace lokoma; ndidzamsenzetsa Efraimu goli; Yuda adzalima, Yakobo adzaphwanya cibuluma cace.
12
Mudzibzalire m'cilungamo mukolole monga mwa cifundo; limani masala anu, pakuti yafika nthawi ya kufuna Yehova, mpaka afika Iye, nabvumbitsira inu cilungamo.
13
Mwalima coipa, mwakolola cosalungama, mwadya zipatso za mabodza; pakati watama njira yako ndi kucuruka kwa anthu ako amphamvu.
14
Momwemo phokoso lidzaukira anthu ako, ndi malinga ako onse adzapasuka, monga Salimani anapasula Betaribeli; tsiku la nkhondo amai anaphwanyika pamodzi ndi ana ace.
15
Momwemo adzakucitirani Betele, cifukwa ca coipa canu cacikuru; mbanda kuca mfumu ya Israyeli idzalikhika konse.
← Chapter 9
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 11 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14