bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Hosea 8
Hosea 8
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 9 →
1
Lipenga kukamwa kwako, Akudza ngati ciombankhanga, kulim bana ndi nyumba ya Yehova; cifukwa analakwira cipangano canga, napikisana naco cilamulo canga.
2
Adzapfuulira kwa Ine, Mulungu wanga, ife Aisrayeli tikudziwani.
3
Israyeli wacitaya cokoma, mdani adzamlondola.
4
Analonga mafumu, koma sikunacokera kwa Ine; anaika akalonga, koma sindinadziwa; anadzipangira mafano a siliva wao ndi golidi wao, kuti akalikhidwe.
5
Mwana wa ng'ombe wako wakutaya, Samariya iwe; mkwiyo wanga wayakira iwo; adzalephera kuyera mtima mpaka liti?
6
Pakuti ici comwe cafumira kwa Israyeli; mmisiri wampanga, koma sali Mulungu; inde mwana wa ng'ombe wa Samariya adzaphwanyika-phwanyika.
7
Pakuti abzala mphepo, nadzakolola kabvumvulu; alibe tirigu wosasenga; ngala siidzaturutsa ufa; cinkana iuturutsa, alendo adzaumeza.
8
Israyeli wamezedwa; tsopano ali mwa amitundu ngati cotengera coti munthu sakondwera naco.
9
Pakuti anakwera kumka ku Asuri, ngati mbidzi ya pa yokha mwini wace; Efraimu walembera omkonda ngati anchito.
10
Inde angakhale alembera mwa amitundu ndidzawasonkhanitsa tsopano; ndipo ayamba kucepa cifukwa ca katundu wa mfumu ya akalonga.
11
Popeza Efraimu anacurukitsa maguwa a nsembe akucimwako, maguwa a nsembe omwewo anamcimwitsa.
12
Ndinamlembera zinthu zambirimbirizo za cilamulo canga, koma zinayesedwa ngati cinthu cacilendo.
13
Kunena za nsembe za zopereka zanga, aphera nsembe yanyama, naidya; koma Yehova sazilandira; tsopano adzakumbukila mphulupulu yao, nadzalanga zocimwa zao; adzabwerera kumka ku Aigupto.
14
Pakuti Israyeli waiwala Mlengi wace, namanga akacisit ndipo Yuda wacurukitsa midzi yamalinga; koma ndidzatumizira midzi yace moto, nudzatha nyumba zace zazikuru.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 9 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14