bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
/
Hosea 13
Hosea 13
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 14 →
1
Pamene Bfraimu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza m'Israyeli; koma pamene anaparamula mwa Baala, anafa.
2
Ndipo tsopano aonjeza kucimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo nchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone ana a ng'ombe.
3
Cifukwa cace adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame asansuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi woturuka kukafwambira.
4
Koma Ine ndine Yehova Mulungu wako cicokere m'dziko la Aigupto, ndipo suyenera kudziwa mulungu wina koma Ine; ndi popanda Ine palibe mpulumutsi.
5
Ndinakudziwa m'cipululu, m'dziko lotentha kwambiri.
6
Monga mwa podyetsa pao, momwemo anakhuta; anakhuta, ndi mtima wao unakwezeka; cifukwa cace anandiiwala Ine.
7
Cifukwa cace ndikhala nao ngati mkango; ngati nyalugwe ndidzalalira kunjira.
8
Ndidzakomana nao ngati cimbalangondo cocilanda ana ace, ndi kung'amba cokuta mtima wao; ndi pomwepo ndidzawalusira ngati mkango; cirombo cidzawamwetula.
9
Israyeli, cikuononga ndi ici, cakuti utsutsana ndi Ine, cithandizo cako.
10
Iri kuti mfumu yako tsopano, kuti ikupulumutse m'midzi yako yonse? ndi oweruza ako amene unanena za iwo, Ndipatseni mfumu ndi akalonga?
11
Ndinakupatsa mfumu mu mkwiyo wanga; ndinamcotsanso m'ukali wanga.
12
Mphulupulu ya Efraimu yamangika, cimo lace lisungika.
13
Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asacedwe mobalira ana.
14
Ndidzawaombola ku, mphamvu ya kumanda, ndidzawaombola kuimfa; imfa, miliri yako iri kuti? manda, cionongeko cako ciri kuti? Kulekerera kudzabisika pamaso panga.
15
Cinkana abala mwa abale ace, mphepo ya kum'mawa idzafika, mphepo ya Yehova yokwera kucokera kucipululu; ndi gwero lace lidzaphwa, ndi kasupe wace adzauma, adzafunkha cuma ca akatundu onse ofunika.
16
Samariya adzasanduka wabwinja, pakuti anapandukana ndi Mulungu wace; iwo adzagwa ndi lupanga, ana ao amakanda adzaphwanyika, ndi akazi ao okhala ndi pakati adzatumbulidwa.
← Chapter 12
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 14 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14