bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Genesis 19
Genesis 19
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 20 →
1
Ndipo anadza ku Sodomu madzulo amithenga awiri; ndipo Loti anakhala pa chipata cha Sodomu, ndipo Loti anaona iwo, nauka kuti akakomane nao, ndipo anaweramitsa pansi nkhope yake.
2
Ndipo anati, Taonanitu, Ambuye anga, tembenukanitu, kulowa m'nyumba mwa kapolo wanu, mugone usiku wonse, mutsuke mapazi anu, ndipo mudzalawira m'mawa kunka ulendo wanu. Ndipo anati, Iai; koma tigone m'khwalalamu usiku wonse.
3
Ndipo anawaumiriza iwo ndithu: ndipo anapatukira kwa iye, nalowa m'nyumba mwake; ndipo anawakonzera iwo madyerero, naphika mikate yopanda chotupitsa, ndipo anadya.
4
Koma asanagone, anthu a m'mudzimo anthu a Sodomu, anazinga nyumba, anyamata ndi okalamba, anthu onse a m'mbali zonse;
5
ndipo anamuitana Loti, nati kwa iye, Ali kuti anthu amene anadza kwa iwe madzulo ano, utitulutsire iwo kuti tiwadziwe.
6
Ndipo Loti anatulukira kwa iwo pakhomo, natseka chambuyo pakhomo pake.
7
Ndipo anati, Abale anga, musachitetu koipa kotere.
8
Taonanitu, ndili ndi ana akazi awiri, amene sanadziwe mwamuna; ndiwatulutsire iwo kwa inu, muchite nao chomwe chikomera inu; koma anthu awa musawachitire iwo kanthu; chifukwa kuti anadza iwo pansi pa mthunzi wa chindwi langa.
9
Ndipo anati iwo, Baima; natinso, Uyu anadza kuno kukhala ngati mlendo, ndipo afuna kutilamulira; tsopano tidzakuchitira iwe koipa koposa iwo. Ndipo iwo anamkakamiza munthuyo Loti ndithu, nayandikira kuti aswe chitseko.
10
Koma anthu aja anatulutsa dzanja lao, namlowetsa Loti momwe anali iwo m'nyumba, natseka pakhomo.
11
Ndipo anachititsa khungu m'maso mwa anthu amene anali pakhomo pa nyumba, ang'ono ndi akulu, ndipo anavutika kufufuza pakhomo.
12
Ndipo anthu aja anati kwa Loti, Kodi muli nao ena pano? Mkamwini, ndi ana ako amuna, ndi ana ako akazi, ndi onse ali nao m'mudzi muno, utuluke nao m'malo muno:
13
popeza ife tidzaononga malo ano, chifukwa kulira kwao kwakula pamaso pa Yehova, ndipo Yehova anatitumiza ife kuti tiuononge.
14
Ndipo anatuluka Loti nanena nao akamwini ake amene anakwata ana ake akazi, nati, Taukani, tulukani m'malo muno; popeza Yehova adzaononga mudziwu; koma akamwini ake anamyesa wongoseka.
15
Pamene kunacha, amithengawo anafulumiza Loti, nati, Uka, tenga mkazi wako, ndi ana ako akazi awiri amene ali kunowa, kuti munganyeke m'mphulupulu ya mudzi.
16
Koma anachedwa; ndipo anthuwo anamgwira dzanja lake, ndi dzanja la mkazi wake ndi dzanja la ana ake akazi awiri; chifukwa cha kumchitira chifundo Yehova; ndipo anamtulutsa iye, namuika kunja kwa mudzi.
17
Ndipo panali pamene anawatulutsa iwo kunja, anati, Tapulumuka ndi moyo wako; usacheuke, usakhale pachigwa paliponse; thawira kuphiri, kuti unganyeke.
18
Ndipo Loti anati kwa iwo, Iaitu, mfumu;
19
taonanitu, kapolo wanu anapeza ufulu pamaso panu, ndipo munakuza chifundo chanu, chimene munandichitira ine, pakupulumutsa moyo wanga; ine sindikhoza kuthawira kuphiri kuti chingandipeze ine choipacho ndingafe;
20
taonanitu, mudzi uwu uli pafupi pothawirapo, ndipo uli waung'ono; ndithawiretu kumeneko, suli waung'ono nanga? Ndipo ndidzakhala ndi moyo.
21
Ndipo anati kwa iye, Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso kuti sindidzaononga mudzi uwu umene wandiuza.
22
Fulumira, thawira kumeneko; pakuti sindithai kuchita kanthu usadafike kumeneko. Chifukwa chake anatcha dzina la mudziwo Zowari.
23
Ndipo dzuwa lidakwera pa dziko pamene Loti anafika ku Zowari.
24
Ndipo Yehova anavumbitsa pa Sodomu ndi pa Gomora miyala ya sulufure ndi moto kutuluka kwa Mulungu kumwamba;
25
ndipo anaononga midziyo, ndi chigwa chonse, ndi onse akukhala m'midzimo, ndi zimene zimera panthaka.
26
Koma mkazi wake anacheuka ali pambuyo pake pa Loti, nasanduka mwala wamchere.
27
Ndipo Abrahamu analawira m'mamawa kunka kumalo kumene anaima pamaso pa Yehova:
28
ndipo anayang'anira ku Sodomu ndi ku Gomora ndi ku dziko lonse la chigwa, ndipo anapenya, taonanitu, utsi wa dzikolo unakwera, monga utsi wa ng'anjo.
29
Ndipo panali pamene Mulungu anaononga midzi ya m'chigwa, Mulungu anakumbukira Abrahamu, natulutsa Loti pakati pa chionongeko, pamene anaononga midzi m'mene anakhalamo Loti.
30
Ndipo Loti anabwera kutuluka m'Zowari nakhala m'phiri ndi ana akazi awiri pamodzi naye: chifukwa anaopa kukhala m'Zowari, ndipo anakhala m'phanga, iye ndi ana ake akazi.
31
Woyamba ndipo anati kwa wamng'ono, Atate wathu akalamba, ndipo palibe pa dziko lapansi mwamuna amene adzalowa kwa ife monga amachita pa dziko lonse lapansi:
32
tiyeni, timwetse atate vinyo, tidzagona naye, kuti tisunge mbeu za atate wathu.
33
Ndipo anamwetsa atate wao vinyo usiku womwewo; woyamba ndipo analowa nagona naye atate wake; ndipo sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.
34
Ndipo panali m'mamawa, woyamba anati kwa wamng'ono, Taona, ndinagona ine ndi atate wanga usiku walero: timwetsenso iye usikunso: udzalowe nugone naye kuti tisunge mbeu za atate wathu.
35
Ndipo anamwetsa vinyo atate wao usiku womwenso; wamng'ono ndipo anauka nagona naye; ndipo iye sanadziwe pomwe anagona ndi pomwe anauka.
36
Ndipo ana akazi awiri a Loti anali ndi pakati pa atate wao.
37
Woyamba ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake. Mowabu; yemweyo ndi atate wa Amowabu kufikira lero.
38
Wamng'ono ndipo anabala mwana wamwamuna, namtcha dzina lake Benami; yemweyo ndi atate wa Aamoni kufikira lero.
← Chapter 18
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 20 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50