bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Genesis 34
Genesis 34
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 35 →
1
Ndipo Dina mwana wamkazi wa Leya, amene anambalira Yakobo, ananka kukaona akazi a kumeneko.
2
Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.
3
Ndipo mtima wake unakhumba Dina mwana wake wamkazi wa Yakobo, ndipo anamkonda namwaliyo, nanena momkopa namwaliyo.
4
Ndipo anati Sekemu kwa atate wake Hamori kuti, Munditengere ine mkazi uyo akhale mkazi wanga.
5
Ndipo anamva Yakobo kuti anamuipitsa Dina, mwana wake wamkazi; ana ake amuna anali ndi zoweta zake kudambo: ndipo Yakobo anakhala chete mpaka anafika iwo.
6
Ndipo Hamori atate wake wa Sekemu anatuluka kunka kwa Yakobo kukanena ndi iye.
7
Ndipo pakumva icho ana ake amuna a Yakobo anabwera pochokera kudambo: amunawo ndipo anapwetekwa mtima, nakwiya kwambiri, chifukwa iyeyo anachita chopusa choipira Israele pakugona ndi mwana wamkazi wa Yakobo; ndicho chosayenera kuchita.
8
Ndipo Hamori ananena ndi iwo, kuti, Mtima wa Sekemu mwana wanga umkhumba mwana wako wamkazi: umpatsetu kuti akhale mkazi wake.
9
Mukwatirane ndi ife: tipatseni ife ana anu akazi, ndiponso dzitengereni ana athu akazi.
10
Ndipo mudzakhala pamodzi ndi ife, dziko lidzakhala pamaso panu; khalani m'menemo ndi kuchita malonda, ndi kukhala nazo zanuzanu m'menemo.
11
Ndipo Sekemu anati kwa atate wake wa mkazi ndi kwa abale ake, Tipeze ufulu pamaso panu, chimene mudzanena kwa ine ndidzapereka.
12
Mundipemphe ine za mitulo ndi zaulere zambirimbiri, ndipo ndidzapereka monga mudzanena kwa ine; koma mundipatse ine namwaliyo akhale mkazi wanga.
13
Ndipo ana ake amuna a Yakobo anayankha Sekemu ndi Hamori atate wake monyenga, nanena, popeza anamuipitsa Dina mlongo wao,
14
nati kwa iwo, Sitingathe kuchita ichi, kupereka mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa; chifukwa kumeneko ndiko kutichepetsa ife.
15
Koma apa pokha tidzakuvomerezani: ngati mudzakhala onga ife ndi kudulidwa amuna onse;
16
pamenepo tidzakupatsani inu ana athu akazi, ndipo tidzadzitengera ana anu akazi, ndipo tidzakhala pamodzi ndi inu, ndi kukhala mtundu umodzi.
17
Koma mukapanda kutimvera ndi kusadulidwa, pamenepo tidzatenga mwana wathu wamkazi, ndi kumuka naye.
18
Mau ao ndipo anakomera Hamori ndi Sekemu mwana wake wa Hamori.
19
Ndipo mnyamatayo sanachedwe kuchichita popeza anakondwera ndi mwana wake wamkazi wa Yakobo; ndipo iye anali wolemekezedwa woposa onse a pa banga la atate wake.
20
Ndipo Hamori ndi Sekemu mwana wake anafika ku chipata cha mudzi wao, nalankhulana ndi anthu a mudzi wao, kuti,
21
Anthu amenewa ali amtendere pamodzi ndi ife; chifukwa chake akhale m'dzikomo, achite malonda m'menemo: pakuti taonani dzikolo lili lalikulu lokwanira iwo; tidzitengere ana ao akazi akhale akazi athu, tiwapatse amenewa ana athu akazi.
22
Anthuwo adzatiloleza ife tikhale nao anthu amodzi, pokhapo amuna onse a mwa ife adzadulidwa, monga iwo adulidwa.
23
Kodi ng'ombe zao ndi chuma chao ndi zoweta zao sizidzakhala zathu? Pokhapo tivomerezana nao ndipo adzakhala pamodzi ndi ife.
24
Ndipo onse amene anatuluka pa chipata cha mudzi wao anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, nadulidwa amuna onse akutuluka pa chipata cha mudzi wao.
25
Ndipo panali tsiku lachitatu pamene anamva kuwawa, ana amuna awiri a Yakobo, Simeoni ndi Levi, abale ake a Dina, anatenga wina lupanga lake wina lake, nalimbika mtima nalowa m'mudzi napha amuna onse.
26
Ndipo anapha Hamori ndi Sekemu mwana wake ndi lupanga, natulutsa Dina m'nyumba ya Sekemu nachoka naye.
27
Ndipo ana amuna a Yakobo anadza kwa ophedwa nafunkha mudzi chifukwa anamuipitsa mlongo wao.
28
Ndipo analanda nkhosa zao ndi zoweta zao ndi abulu ao, ndi za m'mudzi, ndi za m'munda;
29
ndi chuma chao chonse ndi ana ao ndi akazi ao anawagwira, nafunkha zonse za m'nyumba.
30
Ndipo Yakobo anati kwa Simeoni ndi Levi, Mwandisautsa ndi kundinukhitsa ine mwa anthu okhala m'dzikomu, mwa Akanani ndi mwa Aperizi; ndipo ine ndine wa anthu owerengeka, adzandisonkhanira ine ndi kundikantha: ndipo ndidzapasulidwa ine ndi a pa nyumba yanga.
31
Ndipo iwo anati, Kodi iye ayenera kusandutsa mlongo wathu wadama?
← Chapter 33
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 35 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50