bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Genesis 49
Genesis 49
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 48
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 50 →
1
Ndipo Yakobo anaitana ana ake amuna, nati, Sonkhanani inu, kuti ndikuuzeni inu chimene chidzakugwerani inu masiku akudzawo.
2
Sonkhanani, tamvani, ana amuna a Yakobo; tamverani Israele atate wanu.
3
Rubeni, ndiwe woyamba wanga, mphamvu yanga ndi chiyambi cha mphamvu yanga; ulemu wopambana, ndi mphamvu yopambana.
4
Wobwabwada ngati madzi; sudzapambana; chifukwa unakwera pa kama wa atate wako; pamenepo unaipitsapo; anakwera paja ndigonapo.
5
Simeoni ndi Levi ndiwo abale; zida za mphulupulu ndizo malupanga ao.
6
Mtima wangawe, usalowe mu chiungwe chao; ulemerero wanga, usadziphatike pa masonkhano ao; chifukwa m'kukwiya kwao anapha munthu. M'kufuna kwao anapundula ng'ombe.
7
Kutembereredwe kukwiya kwao, chifukwa kunali koopsa; ndi kupsa mtima kwao, chifukwa kunali kwankhalwe. Ndidzawagawanitsa m'Yakobo. Ndidzabalalitsa iwo m'Israele.
8
Yuda, abale ako adzakuyamika iwe; dzanja lako lidzakhala pa khosi la adani ako; ana amuna a atate wako adzakuweramira.
9
Yuda ndi mwana wa mkango, kuchokera kuzomotola, mwananga, wakwera; anawerama pansi, anabwatama ngati mkango, ndipo ngati mkango waukazi; ndani adzamukitsa iye?
10
Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo; ndipo anthu adzamvera iye.
11
Adamanga mwana wa kavalo wake pampesa, ndi mwana wa bulu wake pa mpesa wosankhika; natsuka malaya ake m'vinyo, ndi chofunda chake m'mwazi wa mphesa.
12
Maso ake adzafiira ndi vinyo, ndipo mano ake adzayera ndi mkaka.
13
Zebuloni adzakhala m'mphepete mwa nyanja; ndipo iye adzakhala dooko la ngalawa; ndipo malire ake adakhala pa Sidoni.
14
Isakara ndiye bulu wolimba, alinkugona pakati pa makola.
15
Ndipo anaona popumulapo kuti panali pabwino, ndi dziko kuti linali lokondweretsa; ndipo anaweramitsa phewa lake kuti anyamule, nakhala kapolo wakugwira ntchito ya msonkho.
16
Dani adzaweruza anthu ake, monga limodzi la mafuko a Israele.
17
Dani adzakhala njoka m'khwalala, songo panjira, imene iluma zitende za kavalo, kuti womkwera wake agwe chambuyo.
18
Ndadikira chipulumutso chanu, Yehova.
19
Ndi Gadi, achifwamba adzampsinja iye; koma iye adzapsinja pa chitende chao.
20
Ndi Asere, chakudya chake ndicho mafuta, ndipo adzapereka zolongosoka zachifumu.
21
Nafutali ndi mbawala yomasuka; apatsa mau abwino.
22
Yosefe ndi nthambi yobala, nthambi yobala pambali pa kasupe; nthambi zake ziyangayanga palinga.
23
Eni uta anavutitsa iye kwambiri, namponyera iye, namzunza.
24
Koma uta wake unakhala wamphamvu, ndi mikono ya manja ake inalimbitsidwa. Ndi manja a Wamphamvu wa Yakobo. (Kuchokera kumeneko ndi mbusa, mwala wa Israele,)
25
Ndi Mulungu wa atate wako amene adzakuthangata iwe, ndi Wamphamvuyonse, amene adzakudalitsa iwe. Ndi madalitso a Kumwamba, madalitso a madzi akuya akukhala pansi, madalitso a mawere, ndi a mimba.
26
Madalitso a atate wako apambana mphamvu ndi madalitso a makolo anga, aufikira ku malekezero a patali a mapiri a chikhalire. Adzakhala pa mutu wa Yosefe, ndi pakati pa mutu wa iye amene ali wolekanitsidwa ndi abale ake.
27
Benjamini ndiye mmbulu wakulusalusa; m'mamawa adzadya chomotola, madzulo adzagawa zofunkha.
28
Awa onse ndiwo mafuko khumi ndi awiri a Israele: izo ndizo zomwe ananena kwa iwo atate wao nawadalitsa; yense monga mdalitso wake anawadalitsa.
29
Ndipo analangiza iwo nati kwa iwo, Ine nditi ndisonkhanizidwe kwa anthu a mtundu wanga; mundiike ine pamodzi ndi makolo anga m'phanga lili m'munda wa Efuroni Muhiti,
30
m'phanga lili m'munda wa Makipela, umene uli patsogolo pa Mamure, m'dziko la Kanani, limene Abrahamu analigula kwa Efuroni Muhiti pamodzi ndi munda, likhale poikira pake:
31
pamenepo anaika Abrahamu ndi Sara mkazi wake; pamenepo anaika Isaki ndi Rebeka mkazi wake: pamenepo ndinaika Leya:
32
munda ndi phanga lili m'menemo, zinagulidwa kwa ana a Hiti
33
Pamene Yakobo anatha kulangiza ana ake amuna, anafunya mapazi ake pakama, natsirizika, nasonkhanizidwa kwa anthu a mtundu wake.
← Chapter 48
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 50 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50