bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Genesis 27
Genesis 27
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 28 →
1
Ndipo panali atakalamba Isaki, ndi maso ake anali akhungu losaona nalo, anamuitana Esau mwana wake wamwamuna wamkulu, nati kwa iye, Mwana wanga; ndipo anati kwa iye, Ndine pano.
2
Ndipo anati, Taonatu, ndakalamba, sindidziwa tsiku la kufa kwanga:
3
Tsopano tengatu zida zako ndi phodo lako ndi uta wako, numuke kuthengo kundisakira ine nyama:
4
nundikonzere ine chakudya chokolera chonga chomwe ndichikonda ine, nudze nacho kwa ine kuti ndidzadye; kuti moyo wanga ukadalitse iwe ndisanafe.
5
Ndipo anamva Rebeka pamene Isaki ananena ndi Esau mwana wake. Ndipo Esau ananka kuthengo kukasaka nyama ndi kubwera nayo.
6
Ndipo Rebeka ananena kwa Yakobo mwana wake, nati, Taona ndinamva atate wako alimkunena ndi Esau mkulu wako kuti,
7
Unditengere ine nyama, undikonzere ine chakudya chokolera, kuti ndidzadye, ndi kudalitsa iwe pamaso pa Yehova, ndisanafe.
8
Tsopanotu mwana wanga, tamvera mau anga monga momwe nditi ndikuuze iwe.
9
Pitatu kubusa, ukanditengere ine kumeneko tiana tiwiri tabwino tambuzi; ndikonzere nato chakudya chokolera cha atate wako chonga chomwe achikonda:
10
ndipo udzapita nacho kwa atate wako, kuti adye, ndi kukudalitsa iwe asanafe.
11
Yakobo ndipo anati kwa Rebeka amake, Taonani, Esau mkulu wanga ndiye munthu waubweya, ine ndine munthu wosalala.
12
Kapena atate wanga adzandiyambasa, ndipo ndidzaoneka pamaso pake ngati wakunyenga; pamenepo ndidzadzitengera ine temberero, si mdalitso.
13
Ndipo amake anati kwa iye, Pa ine likhale temberero lako mwana wanga; koma tamvera mau anga, kazimuka kunditengera timeneto.
14
Ndipo anamuka nakatenga nadza nato kwa amake; amake ndipo anakonza chakudya chokolera chonga chimene anachikonda atate wake.
15
Ndipo Rebeka anatenga zovala zokoma za Esau mwana wake wamkulu zinali m'nyumba, naveka nazo Yakobo mwana wake wamng'ono;
16
ndipo anaveka zikopa za tiana tambuzi pamanja ake ndi pakhosi pake posalala;
17
ndipo anapereka m'dzanja la mwana wake Yakobo chakudya chokoleracho, ndi mikate imene anaipanga.
18
Ndipo iye analowa kwa atate wake, nati, Atate wanga; iye anati, Ndine pano; ndani iwe mwana wanga?
19
Ndipo Yakobo anati kwa atate wake, Ndine Esau mwana wanu wamkulu; ndachita monga mwandiuza ine; ukanitu, khalani tsonga, idyani nyama yanga kuti moyo wanu undidalitse ine.
20
Ndipo Isaki anati kwa mwana wake, Unaipeza msanga bwanji mwana wanga? Ndipo anati, Chifukwa kuti Yehova Mulungu wanu anandiyendetsa ine bwino.
21
Ndipo Isaki anati kwa Yakobo, Sendera kuno, ndikuyambase mwana wanga, ngati ndiwe mwana wanga Esau ndithu, kapena wina.
22
Ndipo Yakobo anasendera kwa Isaki atate wake, ndipo anamyambasa nati, Mau ndi mau a Yakobo, koma manja ndi manja a Esau.
23
Ndipo sanamzindikire iye, chifukwa kuti manja ake anali aubweya, onga manja a Esau mkulu wake; ndipo anamdalitsa iye.
24
Ndipo anati, Kodi ndiwe mwana wanga weniweni Esau? Ndipo anati, Ndine amene.
25
Ndipo iye anati, Usendere nayo kwa ine, ndidye nyama ya mwana wanga, kuti moyo wanga ukudalitse iwe. Ndipo anasendera nayo kwa iye, nadya iye; ndipo anamtengera vinyo, namwa iye.
26
Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Senderatu, undimpsompsone mwana wanga.
27
Ndipo anasendera nampsompsona; ndipo anamva kununkhira kwa zovala zake, namdalitsa, nati, Taona, kununkhira kwa mwana wanga, kufanana ndi kununkhira kwa munda anaudalitsa Yehova;
28
Mulungu akupatse iwe mame a kumwamba, ndi zonenepa za dziko lapansi, ndi tirigu wambiri ndi vinyo.
29
Anthu akutumikire iwe, mitundu ikuweramire iwe; uchite ufumu pa abale ako, ana a amai ako akuweramire iwe. Wotemberereka aliyense akutemberera iwe, wodalitsika aliyense akudalitsa iwe.
30
Ndipo panali atatha Isaki kumdalitsa Yakobo, atatuluka Yakobo pamaso pa Isaki atate wake, Esau mkulu wake analowa kuchokera kuthengo.
31
Ndipo iyenso anakonza chakudya chokolera, nadza nacho kwa atate wake, nati kwa atate wake, Auke atate wanga, adye nyama ya mwana wake, kuti moyo wanu undidalitse ine.
32
Ndipo Isaki atate wake anati kwa iye, Ndiwe yani? Ndipo iye anati, Ndine mwana wanu woyamba Esau.
33
Ndipo Isaki ananthunthumira ndi kunthunthumira kwakukulu, nati, Ndani uja anatenga nyama, nadza nayo kwa ine, ndipo ndadyako zonse usadalowe iwe, ndipo ndamdalitsa iye? Inde, adzadalitsika.
34
Pamene Esau anamva mau a atate wake Isaki, analira ndi kulira kwakukulu ndi kowawa kopambana, nati kwa atate wake, Mundidalitse ine, inenso atate wanga.
35
Ndipo iye anati, Mphwako anadza monyenga, nalanda mdalitso wako.
36
Ndipo iye anati, Kodi si ndicho chifukwa anamutcha dzina lake Yakobo? Kuti wandinyenga ine kawiri aka; analanda ukulu wanga ndipo taonani, tsopano walanda mdalitso wanga. Ndipo anati, Kodi simunandisungira ine mdalitso?
37
Ndipo anayankha Isaki nati kwa Esau, Taona, ndamuyesa iye mkulu wako, ndi abale ake onse ndampatsa iye akhale akapolo ake; ndakhazikitsa iye ndi tirigu ndi vinyo; nanga pamenepo mwana wanga, ndidzakuchitira iwe chiyani?
38
Ndipo Esau anati kwa atate wake, Kodi muli nao mdalitso umodzi wokha, atate wanga? Mundidalitse ine, inenso, atate wanga. Ndipo Esau anakweza mau ake nalira.
39
Ndipo Isaki atate wake anayankha nati kwa iye, Taona, pokhala pako mpa zonenepa za dziko lapansi, pa mame a kumwamba akudzera komwe.
40
Udzakhala ndi moyo ndi lupanga lako, nudzakhala kapolo wa mphwako. Ndipo padzakhala pamene udzapulumuka, udzachotsa goli lake pakhosi pako.
41
Ndipo Esau anamuda Yakobo chifukwa cha mdalitso umene atate wake anamdalitsa nao: ndipo Esau anati m'mtima mwake, Masiku a maliro a atate wanga ayandikira; pamenepo ndipo ndidzamupha mphwanga Yakobo.
42
Ndipo anauza Rebeka mau a Esau mwana wake wamkulu: ndipo iye anatumiza naitana Yakobo mwana wake wamng'ono, nati kwa iye, Taona, mkulu wako Esau, kunena za iwe, adzitonthoza yekha mtima wake kuti adzakupha iwe.
43
Ndipo tsopano mwana wanga, tamvera mau anga: tauka, nuthawire kwa Labani mlongo wanga ku Harani;
44
ukhale naye masiku akuwerengeka, mpaka wamchokera ukali wa mkulu wako;
45
mpaka wakuchokera mkwiyo wa mkulu wako, kuti aiwale chimene wamchitira iye; pamenepo ndipo ndidzatumiza kukutenganso iwe kumeneko; ndidzakhala bwanji wopanda inu nonse awiri tsiku limodzi?
46
Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana akazi a Heti: akatenga Yakobo mkazi wa ana akazi a Heti, onga ana akazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?
← Chapter 26
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 28 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50