bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Genesis 50
Genesis 50
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 49
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
1
Ndipo Yosefe anagwa pa nkhope ya atate wake, namlirira iye nampsompsona iye.
2
Ndipo Yosefe anauza akapolo ake asing'anga kuti akonze atate wake ndi mankhwala osungira thupi: ndipo asing'anga anakonza Israele.
3
Ndipo anatha masiku ake makumi anai a iye; chifukwa chomwecho amatsiriza masiku akukonza thupi; ndipo Aejipito anamlira iye masiku makumi asanu ndi awiri.
4
Atapita masiku akumlira iye, Yosefe anati kwa mbumba ya Farao, kuti, Ngatitu ndapeza ufulu pamaso panu, nenanitu m'makutu a Farao kuti,
5
Atate wanga anandilumbiritsa ine, kuti, Taona, ndilinkufa; m'manda m'mene ndadzikonzeratu ndekha m'dziko la Kanani, m'menemo udzandiika ine. Tsopano mundiloletu, ndikwereko, ndipite, ndikaike atate wanga, nditatero ndidzabweranso.
6
Ndipo Farao anati, Pita, kaike atate wako, monga iye anakulumbiritsa iwe.
7
Ndipo Yosefe anapita kukaika atate wake; ndipo anakwera pamodzi ndi akapolo onse a Farao, ndi akulu a pa mbumba yake, ndi akulu onse a m'dziko la Ejipito,
8
ndi mbumba yonse ya Yosefe ndi abale ake, ndi mbumba ya atate wake: ang'ono ao okha, ndi nkhosa zao, ndi ng'ombe zao, anazisiya m'dziko la Goseni.
9
Ndipo anakwera pamodzi ndi iye magaleta ndi apakavalo; ndipo panali khamu lalikulu.
10
Ndipo anafika pa dwale la Atadi, lili tsidya lija la Yordani, pamenepo anamlira maliro a atate wake masiku asanu ndi limodzi.
11
Ndipo pamene anthu okhala m'dzikomo, Akanani, anaona maliro a m'dwale la Atadi, anati, Awa ndi maliro akulu a Aejipito: chifukwa chake dzina la pamenepo linatchedwa Abele-Mizraimu, pali tsidya lija la Yordani.
12
Ndipo ana ake amuna anamchitira iye monga anawalamulira iwo;
13
chifukwa kuti ana ake amuna anamnyamula iye kulowa naye m'dziko la Kanani, ndi kumuika iye m'phanga la munda wa Makipela, limene Abrahamu analigula pamodzi ndi munda, likhale poikira pake, kwa Efuroni Muhiti, patsogolo pa Mamure.
14
Ndipo ataika atate wake, Yosefe anabwera ku Ejipito, iye ndi abale ake, ndi onse amene anakwera pamodzi naye kukaika atate wake.
15
Ndipo pamene abale ake a Yosefe anaona kuti atate wao anafa, anati, Kapena Yosefe adzatida ife, ndipo adzatibwezera ife zoipa zonse tidamchitira iye.
16
Ndipo anatumiza mthenga kwa Yosefe kuti, Atate wathu asanafe analamulira, kuti,
17
Muziti chotero kwa Yosefe, Mukhululukiretu tsopano kulakwa kwa abale anu, ndi kuchimwa kwao, chifukwa kuti anakuchitirani inu choipa; tsopano mutikhululukiretu kulakwa kwa akapolo a Mulungu wa atate wanu. Ndipo Yosefe analira pamene iwo ananena ndi iye.
18
Ndiponso abale ake anamuka namgwadira pamaso pake; nati, Taonani, ife ndife akapolo anu.
19
Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Musaope; pakuti ndili ine kodi m'malo a Mulungu?
20
Koma inu, munandipangira ine choipa; koma Mulungu anachipangira chabwino, kuti kuchitike monga lero, kupulumutsa amoyo anthu ambiri.
21
Ndipo tsopano musaope; ine ndidzachereza inu, ndi ana anu ang'ono. Ndipo anawatonthoza iwo mitima yao, nanena nao mokoma mtima.
22
Ndipo Yosefe anakhala m'Ejipito, iye, ndi mbumba ya atate wake; ndipo Yosefe anakhala ndi moyo zaka zana limodzi ndi khumi.
23
Ndipo Yosefe anaona ana a Efuremu a mbadwo wachitatu; ananso a Makiri mwana wamwamuna wa Manase anabadwa pa maondo a Yosefe.
24
Yosefe ndipo anati kwa abale ake, Ndilinkufa ine, koma Mulungu adzaonekera kwa inu, adzakuchotsani inu m'dziko muno kubwera kunka ku dziko limene analumbirira kwa Abrahamu ndi kwa Isaki, ndi kwa Yakobo.
25
Ndipo Yosefe analumbiritsa ana a Israele kuti, Mulungu adzaonekera kwa inu ndithu, ndipo mudzakwera nao mafupa anga kuchokera kuno.
26
Ndipo anafa Yosefe, anali wa zaka zana limodzi ndi khumi; ndipo anakonza thupi lake ndi mankhwala osungira, ndipo anamuika iye m'bokosi m'Ejipito.
← Chapter 49
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50
Recommended Reading
Commentary
Genesis Commentaries
→
Devotional
Genesis Devotional Guide
→
Get This Bible
Chewa (Buku Lopatulika) Study Bible
→