bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Genesis 9
Genesis 9
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 10 →
1
Ndipo Mulungu anadalitsa Nowa ndi ana ake, nati kwa iwo, Mubalane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi.
2
Kuopsa kwanu, ndi kuchititsa mantha kwanu kudzakhala pa zinyama zonse za dziko lapansi, ndi pa zouluka zonse za m'mlengalenga; ndi pa zonse za m'nyanja, zapatsidwa m'dzanja lanu.
3
Zoyenda zonse zamoyo zidzakhala zakudya zanu; monga therere laliwisi ndakupatsani inu zonsezo.
4
Koma nyama, m'mene muli moyo wake, ndiwo mwazi wake, musadye.
5
Zoonatu mwazi wanu wa miyoyo yanu ndidzafuna; pa dzanja la zinyama zonse ndidzaufuna: ndi pa dzanja la munthu, pa dzanja la mbale wake wa munthu ndidzaufuna moyo wa munthu.
6
Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m'chifanizo cha Mulungu Iye anampanga munthu.
7
Ndi inu, mubalane, muchuluke; muswane pa dziko lapansi, nimuchuluke m'menemo.
8
Ndipo Mulungu ananena kwa Nowa ndi kwa ana ake pamodzi naye, kuti,
9
Ndipo Ine, taonani, Ine ndikhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu, ndi mbeu zanu pambuyo panu;
10
ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, zouluka, ng'ombe, ndi zinyama zonse za dziko lapansi, pamodzi ndi inu; zonse zotuluka m'chingalawa, zinyama zonse za dziko lapansi.
11
Ndipo ndidzakhazikitsa pangano langa pamodzi ndi inu; zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula cha kuononga dziko lapansi.
12
Ndipo anati Mulungu, Ichi ndichi chizindikiro cha pangano limene ndipangana ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zili pamodzi ndi inu, ku mibadwomibadwo;
13
ndiika utawaleza wanga m'mtambomo, ndipo udzakhala chizindikiro cha pangano lopangana ndi Ine ndi dziko lapansi.
14
Ndipo padzakhala pophimba ndi mtambo Ine dziko lapansi, utawo udzaoneka m'mtambomo;
15
ndipo ndidzakumbukira pangano langa limene lili ndi Ine ndi inu, ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo; ndipo madzi sadzakhalanso konse chigumula chakuononga zamoyo zonse.
16
Ndipo utawo udzakhala m'mtambo; ndipo ndidzauyang'anira kuti ndikumbukire pangano lachikhalire lili ndi Mulungu ndi zamoyo zonse zokhala ndi moyo pa dziko lapansi.
17
Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, Ichi ndichi chizindikiro cha pangano ndalikhazikitsa popangana ndi Ine ndi zamoyo zonse za pa dziko lapansi.
18
Ndi ana amuna a Nowa amene anatuluka m'chingalawa ndiwo Semu, ndi Hamu, ndi Yafeti: Hamu ndiye atate wake wa Kanani.
19
Amenewa ndiwo ana amuna atatu a Nowa: ndiwo anafalikira dziko lonse lapansi.
20
Ndipo anayamba Nowa kukhala munthu wakulima nthaka, ndipo analima munda wamphesa:
21
namwa vinyo wake, naledzera; ndipo anali wamaliseche m'kati mwa hema wake.
22
Ndipo Hamu atate wake wa Kanani, anauona umaliseche wa atate wake, nauza abale ake awiri amene anali kunja.
23
Semu ndi Yafeti ndipo anatenga chofunda, nachiika pa mapewa ao a onse awiri, nayenda chambuyo, nafunditsa umaliseche wa atate wao: nkhope zao zinali chambuyo, osaona umaliseche wa atate ao.
24
Nowa ndipo anauka kwa kuledzera kwake, nadziwa chimene anamchitira iye mwana wake wamng'ono.
25
Ndipo anati, Wotembereredwa ndi Kanani; adzakhala kwa abale ake kapolo wa akapolo.
26
Ndipo anati, Ayamikike Yehova, Mulungu wa Semu; Kanani akhale kapolo wake.
27
Mulungu akuze Yafeti, akhale iye m'mahema a Semu; Kanani akhale kapolo wake.
28
Ndipo Nowa anakhala ndi moyo chigumula chitapita, zaka mazana atatu kudza makumi asanu.
29
Ndipo masiku onse a Nowa anali mazana asanu ndi anai kudza makumi asanu: ndipo anamwalira.
← Chapter 8
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 9
Chapter 10
Chapter 11
Chapter 12
Chapter 13
Chapter 14
Chapter 15
Chapter 16
Chapter 17
Chapter 18
Chapter 19
Chapter 20
Chapter 21
Chapter 22
Chapter 23
Chapter 24
Chapter 25
Chapter 26
Chapter 27
Chapter 28
Chapter 29
Chapter 30
Chapter 31
Chapter 32
Chapter 33
Chapter 34
Chapter 35
Chapter 36
Chapter 37
Chapter 38
Chapter 39
Chapter 40
Chapter 41
Chapter 42
Chapter 43
Chapter 44
Chapter 45
Chapter 46
Chapter 47
Chapter 48
Chapter 49
Chapter 50
Chapter 10 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8
9
10
11
12
13
14
15
16
17
18
19
20
21
22
23
24
25
26
27
28
29
30
31
32
33
34
35
36
37
38
39
40
41
42
43
44
45
46
47
48
49
50