bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Song of Solomon 1
Song of Solomon 1
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 2 →
1
Nyimbo yoposa, ndiyo ya Solomoni.
2
Mnyamatayo andipsompsonetse ndi m'kamwa mwake; pakuti chikondi chako chiposa vinyo.
3
Mafuta ako anunkhira bwino; dzina lako likunga mafuta onunkhira otsanulidwa; chifukwa chake anamwali akukonda.
4
Undikoke; tikuthamangire; mfumu yandilowetsa m'zipinda zake: Tidzasangalala ndi kukondwera ndi iwe. Tidzatchula chikondi chako koposa vinyo: Akukonda molungama.
5
Wakuda ine, koma wokongola, ana akazinu a ku Yerusalemu, ngati mahema a Kedara, ngati nsalu zotchinga za Solomoni.
6
Musayang'ane pa ine, pakuti ndada, pakuti dzuwa landidetsa. Ana amuna a amai anandikwiyira, anandisungitsa minda yamipesa; koma munda wangawanga wamipesa sindinausunga.
7
Ndiuze, iwe amene moyo wanga ukukonda, umaweta kuti gulu lako? Umaligonetsa kuti pakati pa usana? Pakuti ndikhalirenji ngati wosochera pambali pa magulu a anzako?
8
Ngati sudziwa, mkaziwe woposa kukongola, dzituluka kukalondola bande la gululo, nukawete anaambuzi zako pambali pa mahema a abusa.
9
Ndakulinganiza, wokondedwa wanga mnyamatawe, ngati akavalo a magaleta a Farao.
10
Masaya ako akongola ndi nkhata zatsitsi, ndi khosi lako ndi zinganga za mkanda wonyezimira.
11
Tidzakupangira nkhata zagolide ndi njumu zasiliva.
12
Pokhala mfumu podyera pake, narido wanga ananunkhira.
13
Wokondedwa wanga mnyamatayo ali kwa ine ngati thumba la mure, logona pakati pa mawere anga.
14
Wokondedwa wanga ali kwa ine ngati chipukutu cha maluwa ofiira m'minda yamipesa ya ku Engedi.
15
Taona, wakongolatu, bwenzi langa; namwaliwe taona, wakongola, maso ako akunga a nkhunda.
16
Taona, wakongolatu, bwenzi langa, mnyamatawe, inde, wakongoletsa; pogona pathu mpa msipu.
17
Mitanda ya nyumba zathu nja mikungudza, ndi mapaso athu nga mlombwa.
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
Chapter 2 →
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8