bible
ra
🌐 Language
English
Español
Français
Deutsch
Português
Italiano
Nederlands
Русский
中文
日本語
한국어
العربية
Türkçe
Tiếng Việt
ไทย
Indonesia
All Languages
Home
/
Chewa
/
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
/
Song of Solomon 8
Song of Solomon 8
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
1
Mwenzi utakhala ngati mlongo wanga, woyamwa pa bere la amai! Ndikadakupeza panja, ndikadakupsompsona; osandinyoza munthu.
2
Ndikadakutsogolera, kukulowetsa m'nyumba ya amai, kuti andilange mwambo; ndikadakumwetsa vinyo wokoleretsa, ndi madzi a makangaza anga.
3
Dzanja lamanzere lake akadanditsamiritsa kumutu, lamanja lake ndi kundifungatira.
4
Ndikulumbirirani, ana akazi inu a ku Yerusalemu, muutsiranji, mugalamutsiranji chikondi, chisanafune mwini.
5
Ndaniyu achokera kuchipululu, alikutsamira bwenzi lake? Pa tsinde la muula ndinakugalamutsa mnyamatawe: Pomwepo amai ako anali mkusauka nawe, pomwepo wakukubala anali m'pakati pa iwe.
6
Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova.
7
Madzi ambiri sangazimitse chikondi, ngakhale mitsinje yodzala kuchikokolola: Mwamuna akapereka katundu yense wa m'nyumba yake ngati sintho la chikondi, akanyozedwa ndithu.
8
Tili ndi mlongwathu wamng'ono, alibe mawere; timchitirenji mlongo wathu tsiku lokhoma unkhoswe wake?
9
Ngati ndiye khoma, tidzamanga pa iye nsanja yasiliva: Ngati ndiye chitseko tidzamtsekereza ndi matabwa amikungudza.
10
Ndine khoma, mawere anga akunga nsanja zake: Pamaso pa mnyamatayo ndinafanana ngati wopeza mtendere.
11
Solomoni anali ndi munda wamipesa ku Baala-Hamoni; nabwereka alimi mundawo; yense ambwezere ndalama chikwi chifukwa cha zipatso zake.
12
Koma munda wanga wamipesa, uli pamaso panga ndiwo wangatu; nacho chikwicho, Solomoni iwe, koma olima zipatso zake azilandira mazana awiri.
13
Namwaliwe wokhala m'minda, anzako amvera mau ako: Nanenanso undimvetse.
14
Dzifulumira, mnyamatawe wokondedwa wanga, dzifanane ngati mphoyo pena mwana wa mbawala pa mapiri a mphoka.
← Chapter 7
Jump to:
Chapter 1
Chapter 2
Chapter 3
Chapter 4
Chapter 5
Chapter 6
Chapter 7
Chapter 8
All chapters:
1
2
3
4
5
6
7
8